1 2Maf. 23.36—24.6; 2Mbi. 36.5-7 Pamene Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, adayamba kulamulira, Chauta adauza Yeremiya kuti,
2“Kaime m'bwalo la Nyumba ya Chauta. Ndipo ukalankhule kwa anthu onse okhala m'mizinda ya ku Yuda, amene amakapembedza ku Nyumba imeneyo. Ukaŵauze zonse zimene ndakulamula kuti ukanene, osasiyapo kanthu.
3Mwina mwake nkutheka kuti adzamvera, ndipo aliyense adzaleka machimo ake. Tsono ndidzaleka osaŵapatsa chilango chimene ndidaati ndiŵalange nacho, chifukwa cha ntchito zao zoipa.
4Ukaŵauze kuti, Chauta akuti: Ngati simundimvera Ine, ngati simutsata malamulo amene ndidakupatsani,
5ngati simumvera mau a aneneri, atumiki anga, amene ndakhala ndikuŵatuma kwa inu, ngakhale kuti inu simunkaŵamvera,
6Yos. 18.1; Mas. 78.60; Yer. 7.12-14 ndiye kuti Nyumba ino ndidzaiwononga monga m'mene ndidaonongera Silo. Ndipo mzinda uno ndidzausandutsa chinthu chonyozeka kwa mitundu yonse ya pa dziko lapansi!”
7Tsono ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu ena ambiri, adamva Yeremiya akulankhula mau ameneŵa m'Nyumba ya Chauta.
8Yeremiya atatsiriza kulankhula zimene Chauta adamlamula kuti auze anthu onse, ansembe, aneneri ndi anthu onsewo adamgwira, namuuza kuti, “Ukuyenera kuphedwa.
9Chifukwa chiyani walosa m'dzina la Chauta kuti Nyumba ino idzaonongedwa ngati Silo, ndipo kuti mzinda uno udzasanduka wopanda anthu, ngati chipululu?” Motero anthu onse adasonkhana nazinga Yeremiya m'Nyumba ya Chauta.
10Akuluakulu a ku Yuda atamva zimene zinkachitikazo, adanyamuka kuchokera ku nyumba ya mfumu kupita ku Nyumba ya Chauta, nakakhala pa bwalo lao ku chipata chatsopano cha Nyumba ya Chauta.
11Pamenepo ansembe ndi aneneri adauza akuluakuluwo ndi anthu ena onse kuti, “Munthu ameneyu ndi woyenera kumupha, chifukwa choti amalosa zoipa za mzinda uno, monga inu nomwe mwadzimvera.”
12Tsono Yeremiya adauza akuluakulu aja ndi anthu onse kuti, “Chauta adachita kundituma kuti ndilengeze mau onse mwamvaŵa oinena Nyumba ya Mulungu ino pamodzi ndi mzindawu.
13Ngati tsopano mukonza makhalidwe anu ndi ntchito zanu zomwe, ndi kuyamba kumvera mau a Chauta Mulungu wanu, ndiye kuti Iye adzakhululuka osakulangani monga m'mene adaaganizira.
14Ineyo ndili m'manja mwanu. Mundichite chilichonse chimene chikukomereni.
15Koma tsono mudziŵe kuti mukangondipha, ndiye kuti inuyo pamodzi ndi mzinda uno ndi anthu onse okhalamo, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi, nzoona kuti Chauta ndiye adandituma kwa inu, kuti mumve zonse ndikunenazi.”
16Pamenepo akuluakuluwo ndi anthu ena adauza ansembe ndi aneneri kuti, “Munthuyu sayenera kufa, popeza kuti walankhula nafe m'dzina la Chauta, Mulungu wathu.”
17Akuluakulu ena am'dzikomo adaimiriranso nauza anthu onse amene adasonkhanawo kuti,
18Mik. 3.12 “Nthaŵi imene Hezekiya anali mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosa, ndipo adauza anthu onse a ku Yuda kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti,
“ ‘Ziyoni adzalimidwa ngati munda.
Yerusalemu adzasanduka bwinja,
phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango.’
19Nanga kodi mfumu Hezekiya ndi anthu onse a ku Yuda adamupha amene uja? Kodi suja mfumu idaopa Chauta nipempha kuti aikomere mtima? Ndipo suja Chauta adaleka osaŵapatsa chilango chimene adaati aŵalange nacho? Koma ife tili pafupi kudziitanira tsoka lalikulu.”
20Padaalinso munthu wina amene ankalosa m'dzina la Chauta, dzina lake Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu. Iyeyo adaalosanso zodzagwera mzinda uno ndi dziko lino monga momwe adachitira Yeremiya.
21Mfumu Yehoyakimu ndi akuluakulu ake onse ndiponso ankhondo ake, atamva zimene adaanena, adaafuna kumupha. Uriya atamva choncho, adachita mantha, nathaŵira ku Ejipito.
22Komabe mfumu Yehoyakimu adatuma Elinatani mwana wa Akibori, pamodzi ndi anthu ena, ku Ejipito.
23Iwowo adakagwira Uriya ku Ejipito komweko, nkubwera naye kwa mfumu Yehoyakimu. Mfumuyo idalamula kuti Uriyayo aphedwe, ndipo mtembo wake adakauika ku manda a anthu wamba.
24Koma Ahikamu mwana wa Safani ndiye adatchinjiriza Yeremiya, motero sadaperekedwe kwa anthu kuti amuphe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.