2 Ako. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kutumikira chipangano chatsopano

1Kodi ponena izi ndiye kuti tikuyamba kudzichitira umboni tokha? Kodi kapena nkofunika kuti ifenso, monga anthu ena, tikhale ndi makalata otichitira umboni kwa inu, kapena makalata aumboni ochokera kwa inu?

2Kalata yotichitira umboniyo ndinu nomwe. Idalembedwa m'mitima mwathu, kuti anthu onse aidziŵe ndi kumaiŵerenga.

3 koma m'mitima mwa anthu.

4Mulungu akudziŵa kuti tikunena zimenezi chifukwa Khristu ndiye amatipatsa kulimba mtima kotere.

5Pakuti mwa ife tokha mulibe kanthu kamene kangatiganizitse kuti tingathe kuchita ntchitoyi patokha. Amene amatipatsa mphamvu ndi Mulungu kuti tithe kuichita.

6Yer. 31.31Ndiye amene adatipatsa mphamvu kuti tikhale otumikira chipangano chatsopano, osati mwa malamulo olembedwa, koma mwa Mzimu Woyera. Paja malamulo olembedwa amadzetsa imfa, koma Mzimu Woyera amapatsa moyo.

7 Eks. 34.29 Malamulo ongolembedwa pa miyala aja adaperekedwa ndi ulemerero waukulu, kotero kuti Aisraele sankatha kuyang'anitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha kuŵala kwake. Komabe kuŵala kwakeko kunali kosakhalitsa. Tsono ngati malamulowo, amene ali odzetsa imfa, adaperekedwa ndi ulemerero wotere,

8nanji ntchito ya Mzimu Woyera, kodi siidzakhala ndi ulemerero wopambana pamenepo?

9Ngati ntchito yoweruza anthu kuti alangidwe inali yaulemerero, ndiye kuti ntchito yoti anthu apezeke olungama pamaso pa Mulungu idzakhala yaulemerero koposa.

10Chifukwa cha ulemerero wopambanawu umene waoneka tsopano, zinthu zimene kale zidaali ndi ulemerero, masiku ano zilibenso ulemerero konse.

11Tsono ngati zinthu zosakhalitsa zidaafika ndi ulemerero, ndiye kuti zinthu zokhala mpaka muyaya zidzakhala ndi ulemerero wopambana.

12Popeza kuti timayembekeza zimenezi, timalimba mtima kwambiri.

13Eks. 34.33 Sitichita ngati Mose amene ankaphimba nkhope yake ndi nsalu, kuwopa kuti Aisraele angamapenye kutha kwake kwa kuŵala kosakhalitsa kuja.

14Koma iwo nzeru zao zidauma, pakuti mpaka lero lino chophimba chomwe chija chimakhalapobe akamaŵerenga mabuku a m'Chipangano Chakale. Pajatu chophimbacho chimachotsedwa pokhapokha munthu akakhala mwa Khristu.

15Ndithu, mpaka lero lino nthaŵi zonse akamaŵerenga Malamulo a Mose, chophimba chija chimaphimbabe mitima yao.

16Eks. 34.34Koma munthu akatembenukira kwa Ambuye, chophimbacho chimachotsedwa.

17Tsono tikamati, “Ambuye,” tikunena Mzimu Woyera. Ndipo kumene kuli Mzimu wa Ambuye, kuli ufulu.

18Tonsefe, opanda chophimba nkhope yathu, timaonetsa ulemerero wa Ambuye, monga momwe galasi limaonetsera nkhope ya munthu. Monsemo Ambuye, amene ali Mzimu, amatisandutsa kuti tifanefane naye, ndi kukhala nawo ulemerero wake mochulukirachulukira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help