1Ku Babiloni kudaali munthu wina dzina lake Yowakimu.
2Adaakwatira mkazi wokongola kwambiri ndi woopa Mulungu, dzina lake Suzana, mwana wa Hilikiya.
3Makolo a Suzana anali Ayuda oopa Mulungu, ndipo mwana waoyo adaamlera motsata malamulo a Mose.
4Yowakimu anali munthu wolemera kwambiri, ndipo anali ndi dimba labwino la mitengo pakhomo pake. Ayuda ankakumana kumeneko kaŵirikaŵiri, chifukwa iye anali munthu wotchuka kupambana iwo onse.
5Chaka chimenecho akuluakulu ena aŵiri adaasankhidwa kuti akhale aweruzi. Ponena za iwowo Ambuye adati,
“Zoipa zidachokera ku Babiloni kwa akuluakulu oweruza amene akadayenera kuŵaongolera bwino anthu anga.”
6Anthu aŵiriwo ankakhala nawo kunyumba kwa Yowakimu kaŵirikaŵiri, ndipo aliyense amene anali ndi mlandu ankabwera kwa iwo.
7Anthu onse atapita kukadya chakudya chamasana, Suzana uja ankayenda ku dimba la mwamuna wake.
8Tsiku ndi tsiku akuluakulu aŵiri aja ankamuwona akuyenda m'dimbamo, ndipo ankalakalaka kuchita naye zadama.
9Maganizo ao adasanduka opotoka kotero kuti adaleka kupemphera kwa Mulungu, osakumbukiranso kuweruza kolungama.
10Onse aŵiri ankamukhumbira kwambiri mkaziyo, koma sankauzana za maganizo aowo.
11Zidaatero chifukwa ankachita manyazi kunena kuti ankafuna kugona naye.
12Tsiku ndi tsiku ankafunafuna mpata woti amuwonere.
13Ndiye tsiku lina adauzana kuti, “Tiyeni tipite kunyumba, yakwana nthaŵi yakudya chakudya chamasana.”
14Adasiyanadi, nachita ngati aliyense akupita kwao. Koma posachedwa aliyense adabwerera kudzafuna Suzana, ndiye gululu akumana. Pofunsana bwino zolinga zao, aliyense adaulula mosabisa kuti ankafuna Suzana. Choncho adangopangana nthaŵi yoti adzampeze ali yekha.
15M'mene iwo ankadikira tsiku labwino, Suzana adapita tsiku lina ku dimba ndi adzakazi aŵiri okha, monga ankachitira nthaŵi zonse. Kunkatentha, ndipo adafuna kukasamba kumeneko.
16Munalibenso wina aliyense m'dimbamo, kupatula akuluakulu aŵiri aja, amene adaabisala nkumamsuzumira Suzanayo.
17Iye adatuma adzakazi ake aŵiri aja kuti, “Takanditengerani mafuta ndi zonunkhira, tsono mutsekeko zitseko m'dimba muno kuti ndisambe.”
18Adzakaziwo adachitadi zimene adaaŵauzazo. Adatseka zitseko natulukira pa khomo lina lakumbali kukatenga zinthu zimene adaaŵatumazo. Sadaŵaone akuluakulu aja, chifukwa adaabisala.
19Adzakazi aja atangochoka, akuluakulu aja adaimirira, nathamangira Suzana.
20Adamuuza kuti, “Mai, onani zitseko za m'dimba muno nzotseka, palibe amene angatiwone. Pepani, kutereku ife tikukufunani, ndiye mutivomere basi.
21Tangoyesani kukana, ife tikuzengani mlandu woti munali ndi mnyamata, nchifukwa chake mudapirikitsa adzakazi anu.”
22Suzana adatsitsa moyo, nati, “Nanga ine nditani? Ndikavomera zimenezi, ndiye kuti kwanga nkukaphedwa. Ndikakana, sindipulumuka m'manja mwanu.
23Koma ai, ine ndikuti toto. Ndi bwino kuti mundiphe, kupambana kuti ndichimwire Ambuye.”
24Motero Suzana adafuula kwambiri, akuluakulu aja nawonso adayamba kufuula.
25Mmodzi mwa iwo adakatsekula chitseko cha m'dimba.
26Antchito akunyumba atamva kufuula ku dimba, adathamangira khomo lakumbali, kuti akaone chimene chamchitikira Suzana.
27Akuluakulu aja atafotokoza nkhani yao, antchito aja adagwidwa ndi manyazi, chifukwa chikhalire sadamumverepo zotere Suzana.
Akuluakulu aja aneneza Suzana28M'maŵa mwake, pamene anthu adaasonkhana kunyumba kwa mwamuna wake Yowakimu, akuluakulu aŵiri aja adafika, atatsimikiza zofuna kulipsira, kuti Suzana aphedwe.
29Pamaso pa anthuwo adati, “Kaitaneni Suzana mwana wa Hilikiya, mkazi wa Yowakimu.”
30Adapita kukamuitana, iye nkubwera pamodzi ndi makolo ake, ana ake ndi anansi ake onse.
31Suzanatu anali wa nkhope yochititsa chidwi ndi yokongola.
32Pamene ankafika pa bwalo, anali atavala nsalu yochinga kumaso. Tsono anthu oipa aja adalamula kuti amuchotse nsaluyo kumaso, kuti amuwone bwino kukongola kwake.
33Am'banja mwake pamodzi ndi anthu onse amene adamuwona, adayamba kulira.
34Akuluakulu aja adaimirira pamaso pa anthu aja, nasanjika manja pamutu pa Suzana.
35Iye adayang'ana kumwamba akulira, chifukwa ankakhulupirira Mulungu.
36Akuluakuluwo adati, “Ife tinkangodziyendera tokha m'dimbamu. Tidangoona mkazi uyu akufika ndi adzakazi ake aŵiri. Adatseka zitseko za m'dimba, adzakazi aja nkuŵabweza kunyumba.
37Tsono mnyamata wina amene adaabisala, adapita kwa iye, nkugona naye.
38Ife nkuti tili ku mapeto a dimba. Tsono poona zoipa zinkachitikazo, tidathamangira komweko.
39Ngakhale tidaŵaona atakumbatirana, sitidathe kumugwira mwamunayo. Anali wamphamvu kwambiri, choncho adatsekula chitseko nkuthaŵa.
40Tidangogwirako mkaziyu, nkumufunsa za mnyamatayo, koma adakana kutiwuza chilichonse. Tikulumbira kuti umboni wathuwu ngwoona.”
41Poti akuluakulu aja anali oyang'anira ndi oweruza anthu, onse amene adaadzasonkhana pamenepo adaŵakhulupirira, navomereza kuti Suzana aphedwe.
Daniele apulumutsa Suzana42Apo Suzana adanena mokweza mau kuti, “Inu Mulungu wamuyaya, mumadziŵa zinsinsi zonse, mumadziŵiratu zinthu zonse zisanachitike nkomwe.
43Mukudziŵa kuti anthuŵa akundinyengezera. Tsopano ndilikufa, komabe ine sindidachite konse zimene andinenezazi.”
44Ambuye adamva pemphero lakelo.
45Pamene anthu ankapita naye kukamupha, Mulungu adautsa nzeru mwa mnyamata wina dzina lake Daniele.
46Iyeyo mokweza mau adati, “Ine musandiŵerengereko pa imfa ya mai ameneyu.”
47Anthu onse adamcheukira, namufunsa kuti, “Iwe ukuti chiyani?”
48Daniele adaimirira nati, “Inu Aisraele, kodi mungapuse chotere? Inu mungagamule kuti mai Wachiisraele aphedwe, musanafufuze nkhani ndi kupeza chenicheni chimene adalakwa?
49Uyambeninso mlanduwu, umboni umene apereka anthu aŵa, kuneneza maiyu, ngwonama.”
50Tsono anthu adabwerera ku bwalo lamilandu, ndipo akuluakulu ena adauza Daniele kuti, “Dzakhale nafe, udzatiwuze zimene uli nazo kukhosi, chifukwa Mulungu wakupatsa nzeru ngati za akulu.”
51Daniele adaŵauza kuti, “Muŵalekanitse anthu oweruzaŵa, akhalirane kutali, kenaka ndiŵafunsitsa bwino.”
52Ataŵalekanitsa, Daniele adaitana mmodzi mwa iwo. Adamuuza kuti, “Akulu inu, mudakalambira m'nkhanza, akubwererani machimo anu akale:
53Munkagamula milandu mopanda chilungamo: kumalanga osalakwa, nkumamasula olakwa amene. Chonsecho Ambuye adanena kuti, ‘Usaphe munthu wosachimwa ndi wosalakwa.’
54Tsopano ngati mudamuwonadi maiyu akuchimwa ndi mnyamata, mudaŵaona ali patsinde pa mtengo wanji?” Iye adayankha kuti, “Patsinde pa mkuyu.”
55Daniele adati, “Ndithudi, bodza lanu lakubwererani. Mngelo wa Mulungu walamulidwa kale kuti akulangeni, adzakudulani pakati.”
56Atatero adamuuza kuti aime pambali, nalamula anthu aja kuti abwere ndi wina uja. Tsono Daniele adamuuza kuti, “Akulu inu, mukukhala ngati ndinu Mkanani osati Myuda! Kukongola kwa akazi kwakusokonezani, ndipo dama lakusandutsani chitsiru.
57Ndikudziŵa m'mene mwakhala mukuvutitsira akazi a ku Israele, iwo amangovomera chifukwa cha mantha. Koma mai wa ku Yudayu wakukanikani kuti muchimwe naye.
58Tanenani tsono, ndi patsinde pa mtengo wanji mudaŵapezera ali aŵiri?” Iye adayankha kuti, “Patsinde pa mtengo wa thundu.”
59Daniele adati, “Ndithudi, bodza lanu lakubwererani. Mngelo wa Mulungu akukudikirani ndi lupanga kuti akuchekeni pakati ndi kukuwonongani aŵirinu.”
60Pamenepo anthu onse adafuula kwambiri, natamanda Mulungu, Mpulumutsi wa anthu okhulupirira Iye.
61Kenaka adatembenukira oweruza aŵiri aja, amene Daniele adaaŵatsutsa chifukwa chochita umboni wabodza.
62Adaŵalanga potsata malamulo a Mose, ndi kuŵapha monga momwe iwo ndi kuipa mtima kwao adaafuna kuphera mbale wao. Motero munthu wosalakwa adapulumuka tsiku limenelo.
63Tsono Hilikiya ndi mkazi wake adathokoza Mulungu, nayenso mwamuna wake Yowakimu pamodzi ndi anansi onse aja adachita chimodzimodzi, poona kuti Suzana wapezeka wosalakwa.
64Ndiye kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake, Daniele ankamulemekeza kwambiri anthu onse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.