Mas. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide apempha Chauta kuti amtsogolere ndi kumtchinjirizaSalmo la Davide.

1Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta.

2Ndikuika mtima wanga pa Inu Mulungu wanga.

Musalole kuti adani anga andichititse manyazi,

musalole kuti akondwere pamene ine ndikuvutika.

3Zoonadi, onse okhulupirira Inu asaŵachititse manyazi,

koma muchititse manyazi

onse ochita dala zosakhulupirika.

4Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta,

mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu.

5Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza,

pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga,

ndimadalira Inu masiku onse.

6Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu

ndi chikondi chanu chosasinthika,

chifukwa mudaziwonetsa kuyambira kalekale.

7Musakumbukire machimo a unyamata wanga

ndi mphulupulu zanga.

Koma mundikomere mtima, Inu Chauta,

chifukwa cha chikondi chanu,

pakuti Inu ndinu abwino.

8Chauta ndi wabwino ndi wolungama.

Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake.

9Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama,

amaŵaphunzitsa njira zake.

10Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika,

nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake

ndi malamulo ake.

11Malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, Inu Chauta,

mundikhululukire machimo anga

pakuti mlandu wanga ndi waukulu.

12Kodi pali munthu woopa Chauta?

Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate.

13Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino,

ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao.

14Chauta amapalana chibwenzi ndi anthu omvera Iye,

ndipo amaŵadziŵitsa chipangano chake.

15Maso anga akuyang'ana kwa Chauta nthaŵi zonse,

pakuti adzaonjola mapazi anga mu ukonde.

16Inu Chauta yang'aneni ine,

ndipo mundikomere mtima,

pakuti ndili ndekhandekha,

ndipo ndazunzika kwambiri.

17Mundichotsere nkhaŵa za mumtima mwanga,

ndipo munditulutse m'masautso anga.

18Penyani mazunzo anga ndi mavuto anga,

ndipo mundikhululukire machimo anga onse.

19Onani m'mene adani anga ankhalwe achulukira

ndi m'mene chidani chao ndi ine chakulira.

20Tchinjirizani moyo wanga ndi kundipulumutsa.

Musalole kuti andichititse manyazi,

pakuti ndikuthaŵira kwa Inu.

21Kukhulupirika kwanga ndi kulungama kwanga kunditeteze,

popeza kuti ndakukhulupirirani.

22Inu Mulungu apulumutseni m'mavuto ao onse

anthu anu Aisraele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help