Bar. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Yeremiya adaatumiza kalata kwa anthu amene mfumu ya Ababiloni inali pafupi kuŵatenga ukapolo kunka nawo ku Babiloni. M'kalatamo munali uthenga umene Mulungu adaalamula Yeremiya kuti aŵauze anthuwo. Kalatayo inali yotere:

2“Inu mudamchimwira Mulungu. Nchifukwa chake Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ali pafupi kukutengani ukapolo kunka nanu ku Babiloni. Ndiyetu mukakafika ku Babiloniko, mukakhalako zaka zambiri mpaka kukwanitsa mibadwo isanu ndi iŵiri. Koma pambuyo pake ndidzakubwezerani kwanu mwamtendere.

3Tsono ku Babiloni mudzaona milungu yopangidwa ndi siliva, golide ndi mitengo. Milunguyo amaisenza pa mapewa, ndipo imaopsa anthu akunja.

4Choncho inu mukachenjere. Musakatsanzire akunjawo, musamakaiwope milungu yaoyo,

5mukakaona anthu akumeneko akuipembedza pa mdipiti. Koma mumtima mwanu muzikati, ‘Ambuye, ndinu nokha oti tizikupembedzani.’

6Chifukwa mngelo wanga ali nanu, ndipo azidzakuyang'anirani.”

Mafano ngachabechabe

7Milunguyo mmisiri adachita kuipala malilime ake, nkuikuta ndi golide ndi siliva. Koma ndiyonama ndipo ndiyosatha kulankhula.

8Anthu amatenga golide nkupanga zisoti zaufumu zoti aike pamutu pa milungu yao, monga momwe akadachitira pomupangira zokongoletsa mtsikana wokonda zoterezi.

9Nthaŵi zina, ngakhale ansembe omwe amakamchotsa mobisa golide ndi silivayo pa milungu yao nkumagulira zosoŵa zao.

10Mwinanso golide ndi silivayo amakagaŵirako akazi adama a ku nyumba ya milunguyo. Milungu imeneyi yomwe ili yopanga ndi golide, siliva kapena mtengo, amaiveka zovala ngati anthu, ngakhale kuti siingathe kuletsa dzimbiri ndi zitsenda kuti zisaiwononge.

11Ataiveka mikanjo yofiirira, amapukuta nkhope zake kuchotsa fumbi lambiri limene lidaigwera.

12Milunguyo imakhala ndi ndodo yachifumu m'manja ngati atsogoleri a dziko, komabe siingathe kumupha munthu woinyoza.

13Ina imakhala ndi lupanga kapena nkhwangwa ku dzanja lamanja, komabe siitha kudziteteza kwa adani kapena kwa mbala.

14Zimenezi nzoonetsa kuti milungu imeneyi si yeniyeni. Tsono musamachite nayo mantha.

15Monga mbale imati ikasweka, ilibenso ntchito, ndi m'menenso iliri milungu yao, akaikhazika m'nyumba zake.

16M'maso mwake mumadzaza fumbi limene amalikutumula anthu oloŵamo.

17Paja amampiringidzira zitseko munthu amene wanyoza mfumu, ndipo akuyenera kukaphedwa. Ansembe amateronso: amateteza nyumba za milunguyi ndi zitseko zolimba, maloko ndi mipiringidzo, kuwopetsa mbala.

18Amayatsa nyale zochuluka kuposa zimene zili m'nyumba zaozao, koma milunguyo siiwona nyale ndi imodzi yomwe.

19Imakhala ngati chimtanda cha m'nyumba chimene anthu amati thima lake lidafumbwa. Zitsenda zimatuluka m'dothi nkumaidya ndi zovala zake zomwe, iyoyo osamvako kanthu.

20Kumasoku kumachita kuti bii chifukwa cha utsi wa m'nyumba zake.

21Mileme, anamzeze ndi mbalame zina zimadzaitera pathupi pake ndi pamutu pomwe, apakanso amadzaseŵera pomwepo.

22Choncho mungathe kutsimikiza kuti si milungulungu, ndiye inu musaiwope.

23Golide amene amaiveka kuti iziwoneka yokongola, munthu akapanda kuchotsa litsiro lake, milungu imeneyi siingaŵale konse. Ngakhale pamene ankaiwumba, iyoyo siinkamvako kanthu.

24Inde milunguyo adaigula ndi mtengo wapatali, komabe mwa iyoyo mulibe mpweya wamoyo.

25Popeza kuti siitha kuyenda, amachita kuinyamula pa mapewa, chizindikiro chakuti ndi yachabechabe. Ngakhale anthu oipembedza imaŵachititsa manyazi, chifukwa imati ikagwa pansi, anthuwo amachita kuiimiritsa.

26Akaiimiritsa kumene, siithanso kuyenda pa yokha. Ndipo wina akaipendeketsa, siitha kuwongoka pa yokha. Kuipatsa mphatso nchimodzimodzi kupatsa anthu akufa.

27Zopereka kwa milungu imeneyi, ansembe amazigulitsa, ndalama zake nkudya iwowo. Mwina akazi a ansembewo amasungako zina mwa zoperekazo mu mchere, koma sathandizira anthu osauka ndi aumphaŵi.

28Ngakhale akazi amene ali pakati pa msambo, kapena amene ali m'chikuta, amaloledwa kugwira nsembe zopereka kwa milunguyo. Choncho mukuwona kuti imeneyi si milungu, ndiye musachite nayo mantha.

29Nanga amaitchula bwanji kodi kuti milungu, pamene ndi akazi amene amaperekera zakudya kwa milungu imeneyi yopangidwa ndi golide, siliva ndi mtengo?

30M'nyumba za milunguyo ansembe amangokhala pansi atang'amba zovala zao, tsitsi ndi ndevu atameta, kumutu osavala kanthu.

31Amadzuma ndi kumalira pamaso pa milungu yaoyo, monga m'mene anthu amachitira pa maliro.

32Ansembe amatenga zovala za milunguyo kuti aveke akazi ao ndi ana ao.

33Ngakhale aichitire zoipa kapena zabwino, siibwezera. Ilibe mphamvu zolonga mfumu kapena kuichotsa.

34Siithanso kupezetsa chuma kapena ndalama. Ngati wina adalonjezana nayo kanthu, napanda kuchita kanthuko, iyo siitha kumkakamiza kuti achite ndithu.

35Siingathe kupulumutsa munthu ku imfa, kapena kuwombola anthu ofooka m'manja mwa anthu amphamvu.

36Siingathe kupenyetsa munthu wakhungu kapena kuthandiza munthu wozunzika.

37Siingamvere chifundo mkazi wamasiye, kapena kuchitira zabwino mwana wamasiye.

38Zinthu zopanga ndi mitengozi, zokutidwa ndi golide ndi siliva, zili ngati miyala yakuphiri, ndipo amene amazipembedza adzachita manyazi.

39Tsono wina angathe bwanji kuziyesa milungu, kapena kuzitchula milungu?

Kupembedza mafano nkupusa

40Ngakhale anthu a ku Kalidea omwe sailemekeza milungu yaoyo. Akapeza munthu amene salankhula, amapita naye ku fano la Belo, ndipo amalipempha kuti limlankhulitse, ngati kapena ilolo nkumva.

41Komabe iwo satha kuzindikira kanthu pamenepo ndipo safuna kuisiya milungu yachabeyo, chifukwa alibe nzeru konse.

42Paja akazi amamanga zingwe m'chiwuno, nkukakhala pansi m'mphepete mwa miseu, namatentha gaga ngati lubani.

43Tsono mmodzi mwa iwo akatengedwa ndi mwamuna wina wodutsa, nagona naye, amapeputsa mnzake kuti ngwopanda chikoka ngati iyeyo, ndipo chingwe chake nchosaduka.

44Zonse zimene anthuwo amachitira milungu imeneyi nzabodza. Tsono wina angavomere bwanji kuti imeneyi ndi milungu?

45Milunguyo idapangidwa ndi amisiri a matabwa ndi a golide, choncho siingakhalire mwina koma monga momwe amisiriwo adaipangira.

46Ndipo kosapeneka konse amisiri oipangawo iwo omwe sadzakhalitsa pansi pano, tsono zinthu zimene amapangazo zingasanduke milungu bwanji?

47Amangosiyira anthu anzao zinthu zabodza ndi zochititsa manyazi.

48Pakabuka nkhondo kapena zoopsa zina, ansembe amakambirana za kumene angabisale pamodzi ndi milungu yao.

49Tsono amalephera bwanji kumvetsa kuti imeneyi si milungu, popeza kuti siingathe kudzipulumutsa pa nthaŵi ya nkhondo kapena ya zovuta zina?

50Milungu imeneyi, yopangidwa ndi mitengo, ndi kukutidwa ndi siliva ndi golide, idzazindikirika bwino lino kuti ndiyonama. Anthu a mitundu yonse ndi mafumu omwe adzadziŵa kuti si milungu konse, koma ndiyopangidwa ndi anthu ndipo ilibe konse mphamvu.

51Kodi aliponso wina amene sadazindikirebe kuti imeneyi si milungu konse?

52Milungu imeneyi siingathe kulonga munthu ufumu, siingathenso kugwetsera anthu mvula.

53Siingathe kuyendetsa zinthu zake kapena kupulumutsa wina amene ali pa mavuto, chifukwa ilibe mphamvu. Ili ngati makwangwala ongouluka pakati pa thambo ndi dziko lapansi.

54Moto ukadzabuka m'nyumba ya milungu imeneyi, ansembe ake adzathaŵa, nadzapulumuka, koma milungu yamitengoyo, yokutidwa ndi golide ndi siliva, idzapsa monga mitengo ya m'nyumba.

55Siingathenso kulimbana ndi mfumu kapena adani ena.

56Nanga tingathe bwanji kuvomera ngakhale kungoganizako kuti zosemazi ndi milungu?

57Milungu imeneyi siingathe kupulumuka kwa anthu akuba ndi achifwamba.

58Milungu yosemayi, yokutidwa ndi golide ndi siliva, anthu anyonga adzailanda golide ndi siliva wakeyo, pamodzi ndi zovala zake zomwe nkuthaŵa nazo, ndipo milunguyo siidzatha kudzipulumutsa yokha.

59Kukhala mfumu yoonetsa kulimba mtima kwake, kapena kukhala mtsuko wam'nyumba wogwira ntchito zofuna mwiniwake, kuli bwino koposa kukhala milungu yabodzayi. Kukhala chitseko choteteza katundu amene ali m'nyumba kapena mzati wamtengo m'nyumba ya mfumu, kuli bwino koposa kukhala milungu yonamayi.

60Dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi zimene zimaŵala zili ndi ntchito yakeyake ndipo zimagonjera Mulungu.

61Chimodzimodzi ching'aning'ani chikang'anima, chimaoneka ponseponse, ndi mphepo imakuntha pa dziko lonse.

62Mulungu akalamula mitambo kuti iyendere dziko lonse lapansi, imayenderadi. Moto wochoka kumwamba kuti utenthe mapiri ndi nkhalango, umachita zimene adaulamula.

63Koma milunguyi siilingana nazo zinthu zimenezo pa maonekedwe kapena pa mphamvu.

64Tsono tisamaganiza ndi kunena kuti imeneyi ndi milungu, chifukwa siingathe kuweruza milandu, ndipo siingathe kuchitira anthu zabwino.

65Motero popeza kuti mwazindikira kuti imeneyi si milungu, musaiwope tsono.

66Siingathe konse kutemberera mafumu kapena kuŵadalitsa.

67Siingaonetse mitundu ya anthu zizindikiro zakumwamba, siingaŵale monga dzuŵa, ndipo siingaunikire monga mwezi.

68Nyama zikuipambana milungu imeneyi, chifukwa zimatha kudzipulumutsa zokha ndi kuthaŵa zoopsa.

69Choncho palibe umboni uliwonse wotsimikiza kuti imeneyi ndi milungudi; nchifukwa chake musaiwope.

70Milungu yao yosemayo, yokutidwa ndi golide ndi siliva, ili ngati chithunzi choingira mbalame m'munda wa minkhaka, siiteteza kanthu konse.

71Milungu imeneyi ikufanafana ndi mtengo waminga m'munda m'mene mbalame zimateramo, ikufanafananso ndi mtembo umene auponya mu mdima.

72Kuwola kwa zovala zake zofiirira ndi zabafuta kumaonetsa kuti imeneyi si milungu. Potsiriza iyo yomwe idzafumbwa, ndipo dziko lonse lidzachita nayo manyazi.

73Nchifukwa chake tsono munthu wolungama, amene alibe mafano otereŵa, ali bwino kwambiri. Iyeyo anthu sadzachita naye manyazi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help