Yos. 22 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yoswa abwezera kwao mafuko akuvuma.

1Pambuyo pake Yoswa adaitana anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi, ndi hafu lina lija la fuko la Manase wakuvuma.

2Num. 32.20-32; Yos. 1.12-15 Ndipo adaŵauza kuti, “Zonse zimene Mose mtumiki wa Chauta adakulamulani kuti muchite, mwachitadi, ndipo mwamvera malamulo anga onse.

3Aisraele anzanu simudaŵasiye nthaŵi yonseyi mpaka lero lino. Mwasamaladi malamulo onse a Chauta, Mulungu wanu.

4Tsopano Chauta, Mulungu wanu, wapatsa mtendere Aisraele anzanu, monga momwe adaalonjezera. Motero bwererani kwanu ku dziko limene mudalandira, dziko limene lili patsidya pa mtsinje wa Yordani kuvuma, limene Mose mtumiki wa Chauta adakupatsani.

5Musamale bwino kuti mumvere ndithu malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Mulungu adakupatsani. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zimene Iyeyo akufuna, muzimvera malamulo ake, muzikhala okhulupirika kwa Iye, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi mzimu wanu wonse.”

6Kenaka Yoswa adaŵadalitsa anthuwo, naŵauza kuti apite. Tsono anthuwo adapita kwao.

7Mose anali atapatsa theka lina la fuko la Manase ku dziko la Basani. Koma theka lina la fuko la Manase, Yoswa adalipatsa dziko kuzambwe kwa Yordani, pamodzi ndi abale ao onse. Pamene Yoswa ankaŵatumiza kwao anthu amenewo, adaŵadalitsa,

8naŵauza kuti, “Tsopano mukubwerera kwanu mutalemera. Muli ndi ng'ombe zambiri, mulinso ndi siliva, golide, mkuŵa, zitsulo ndi zovala zambiri. Izi zimene mudafunkha kwa adani anu, mugaŵireko Aisraele anzanu.”

9Motero anthu onse a fuko la Rubeni ndi la Gadi, pamodzi ndi theka lija la fuko la Manase, adabwerera kwao. Aisraele ena onse adaŵasiya ku Silo m'dziko la Kanani, ndipo iwowo adapita ku dziko la Giliyadi. Dziko limeneli ndilo linali lao, chifukwa adalilandira potsata malamulo a Chauta kudzera mwa Mose.

Guwa la ku Yordani.

10Anthuwo atafika ku Geliloti, malo omwe anali pambali pa mtsinje wa Yordani m'dziko la Kanani, adamangako guwa lalikulu ndi lokoma pambali pa mtsinjewo.

11Tsono Aisraele ena onse adauzidwa kuti, “Tamvani! Anthu onse a fuko la Rubeni ndi la Gadi, pamodzi ndi theka lija la fuko la Manase adamanga guwa ku Geliloti m'malire a dziko la Kanani, tsidya lakuno la Yordani, moyang'anana ndi Israele.”

12Tsono Aisraele atamva zimenezi, onse pamodzi adasonkhana ku Silo, kuti apite kukamenyana nawo nkhondo.

13Pomwepo Aisraelewo adatuma Finehasi, mwana wa wansembe Eleazara kwa anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndiponso a theka lina lija la Manase, amene ankakhala ku dziko la Giliyadi.

14Finehasiyo adapita pamodzi ndi akuluakulu khumi ochokera ku fuko lililonse la Aisraele. Aliyense mwa akuluakulu amenewo anali mtsogoleri wa banja limodzi la mafukowo.

15Adafika ku dziko la Giliyadi, naŵauza anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi theka lina lija la fuko la Manase kuti,

16Deut. 12.13, 14 “Anthu onse a Chauta alikufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani inu mwachimwa chotere, potsutsana ndi Mulungu wa Israele? Mwapandukira Chauta ndi kutsutsana naye pakudzimangira guwa limeneli, ndipo simukumtsatanso.

17Num. 25.1-9 Kumbukirani tchimo la ku Peori lija limene Chauta adalanga nalo anthu ake poŵatumizira mliri woopsa. Mpaka lero lino, tchimo limene lija tidakasauka nalobe. Kodi tchimo limene lija ndi lochepa?

18Kodi tsopano mufuna kuleka kutsata Chauta, Mulungu wanu? Mukampandukira lero lino, Iye adzakwiyira mtundu wonse wa Aisraele maŵamaŵali.

19Motero tsono, ngati dziko lanulo ndi losayenera kupembedzeramo, pitani uko ku dziko la Chauta komwe kuli chihema chake chija, ndipo mugaŵane nafe dziko lathulo. Koma musapikisane ndi Chauta kapena kutisandutsanso ochimwa ife, podzimangira guwa lina kulimbana ndi Chauta, Mulungu wathu.

20Yos. 7.1-26 Kumbukirani kuti Akani, mwana wa Zera uja, adakana kumvera lamulo la zinthu zoyenera kuwonongedwa zija, ndipo Aisraele onse adalangidwa. Akaniyo sadafe yekha chifukwa cha tchimo lakelo.’ ”

21Pamenepo fuko la Rubeni, ndi la Gadi pamodzi ndi theka lina lija la fuko la Manase, adayankha atsogoleri a mabanja a Aisraelewo kuti,

22“Wamphamvu uja, Mulungu, Iyeyo ndiye Chauta. Wamphamvu uja, Mulungu, Iyeyo ndiye Chauta. Akudziŵa chifukwa chake chimene tidachitira zimenezi, ndipo inunso muyenera kudziŵa. Ngati tidapanduka ndi kuleka kukhulupirira Chauta, musatilole kukhalanso ndi moyo.

23Ngati sitidamvere Chauta pamene tidadzimangira tokha guwa lopserezapo nsembe, kapena kumapereka zopereka zatirigu kapena zopereka zamtendere, Chauta yekha ndiye atilange.

24Tidachita zimenezi chifukwa choopa kuti kutsogoloko zidzukulu zanu zingamadzanene zidzukulu zathu kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Aisraele, kodi inu muli naye nkanthu?

25Chauta adaika malire a Yordani pakati pa ife ndi inu, anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi. Motero, inu mulibe gawo mwa Chauta.’ Tsono mwina zidzukulu zanuzo nkudzaletsa zidzukulu zathu kupembedza Chauta.

26Nchifukwa chake tidamanga guwa, osati kuti tizipserezapo nsembe kapena kumapereka zopereka pamenepo,

27koma makamaka kuti chikhale chizindikiro pakati pa ife ndi inu. Ndipo chikhalenso chizindikiro kwa mibadwo yobwera pambuyo pathu, kuti idzadziŵe kuti timapembedzanso Chauta ndi nsembe zathu zopsereza, zopereka, ndiponso nsembe zamtendere. Motero zidzukulu zanu zisadzanene kwa zidzukulu zathu m'tsogolo muno kuti, ‘Inu mulibe gawo mwa Chauta.’

28Ameneŵa ndiwo anali maganizo athu kuti, ngati zimenezi zidzachitika, ife tidzanene kuti, ‘Onani, makolo athu adamanga guwa lofanafana ndi guwa la Chauta. Limeneli silinali loperekerapo nsembe zopsereza kapena lopherapo nyama za nsembe, koma linali chizindikiro pakati pa ife ndi inu.’

29Sitingathe kupandukira Chauta. Sitingathenso kuleka kumtsata tsopano lino, ndi kumanga guwa la zopereka zopsereza, kapena chopereka cha chakudya kapenanso la nsembe zina, loti lizipikisana ndi guwa la Chauta wathu lomwe lili patsogolo pa malo opatulika m'mene Chauta amakhalamo.”

30Wansembe Finehasi ndi akuluakulu amene anali naye, amene anali atsogoleri a mabanja a Aisraele, atamva zimene adanena anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi la Manase, adakondwa kwambiri.

31Ndipo Finehasi, mwana wa wansembe Eleazara, adauza anthu a mafuko aja kuti, “Tsopano tadziŵadi kuti Chauta ali nafe, poti simudapanduke ndi kutsutsana ndi Chauta. Mwapulumutsa Aisraele ku chilango cha Chauta.”

32Tsono Finehasi, pamodzi ndi mafumuwo adachoka ku Giliyadi nasiya anthu a fuko la Rubeni pamodzi ndi la Gadi, nabwerera ku Kanani kwa Aisraele anzao, ndipo adakafotokoza zonsezo.

33Mau adafotokozawo adakondwetsa Aisraele onse. Adatamanda Mulungu, ndipo sadakambenso za nkhondo yokaononga dziko limene anthu a mafuko a Rubeni ndi Gadi ankakhalamo.

34Choncho anthu a mafuko a Rubeni ndi Gadi adalitcha guwalo kuti Mboni, chifukwa iwowo adati, “Chimenechi ndi mboni kwa tonsefe kuti Chauta ndi Mulungudi.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help