1Inu Mulungu, mundichitire chifundo,
pakuti anthu akundizunza.
Adani akundithira nkhondo ndi kundipsinja tsiku lonse.
2Adani akundizunza tsiku lonse,
pali ambiri amene akumenyana nane monyada.
3Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu.
4Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza.
Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha.
Kodi munthu angandichite chiyani?
5Tsiku lonse adaniwo amafunafuna
kulepheretsa zolinga zanga.
Zonse zimene amaganiza ndi zoti andichite zoipa.
6Amasonkhana okhaokha namabisalira,
amalonda mayendedwe anga,
amafuna kundipha.
7Muŵalange chifukwa cha zoipa zao.
Inu Mulungu, muŵakwiyire anthuwo ndi kuŵaononga.
8Inu mwaona kupiripita kwanga,
mudziŵa kuchuluka kwa misozi yanga.
Kodi zonsezi sizidalembedwe m'buku lanu?
9Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo
pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu.
Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga.
10Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha mau ake.
Ndimatamanda Chauta chifukwa cha zimene wandilonjeza.
11Ndimadalira Mulungu, sindidzachita mantha konse.
Kodi munthu angandichite chiyani?
12Ndiyenera kuchita zimene ndidalumbira kwa Inu Mulungu.
Ndidzapereka kwa Inu nsembe zothokozera.
13Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa.
Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe,
kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu
m'kuŵala kwa amoyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.