1Mvetsetsani zimene ndikukuphunzitsani,
inu anthu anga.
Tcherani khutu, mumve mau a pakamwa panga.
2 Mt. 13.35 Ndidzakusimbirani fanizo.
Ndidzalankhula nkhani zobisika zakalekale,
3zinthu zimene tidazimva ndi kuzidziŵa,
zomwe makolo athu adatifotokozera.
4Sitidzabisira ana ao,
koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo
ntchito zotamandika za Chauta,
tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa
zimene wakhala akuchita.
5Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe,
adakhazikitsa malamulo ake mu Israele.
Adalamula makolo athu
kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo.
6Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe,
udzaŵadziŵa,
ndipo nawonso udzafotokozera ana ake.
7Anawo aike chikhulupiriro chao pa Mulungu,
ndipo asaiŵale ntchito za Mulungu,
koma asunge malamulo ake.
8Asakhale ngati makolo ao,
anthu oukira ndi osamvera aja,
mbadwo wa anthu amene mitima yao inali yosakhazikika,
amene moyo wao unali wosakhulupirika kwa Mulungu.
9Ngakhale Aefuremu anali ndi mauta,
komabe adathaŵa pa tsiku la nkhondo,
10sadasunge chipangano cha Mulungu,
koma adakana kutsata malamulo ake.
11Iwo adaiŵala zimene Mulungu adachita,
ndiponso zozizwitsa zimene Iye adaŵaonetsa.
12 Eks. 7.8—12.32 Mulungu adachita zodabwitsa zake,
makolo ao akuwona,
m'dziko la Ejipito, ku dera la Zowani.
13 Eks. 14.21, 22 Adagaŵa nyanja pakati, kuti iwo apitepo,
ndipo adaimiritsa madzi ngati makoma.
14 Eks. 13.21, 22 Masana ankaŵatsogolera ndi mitambo,
usiku ankaŵatsogolera ndi kuŵala kwamoto.
15Adang'amba matanthwe am'chipululu,
naŵapatsa madzi ochuluka ngati amumtsinje,
kuti amwe.
16 Lun. 16.1—19.22 Eks. 17.1-7; Num. 20.2-13 Adatumphutsa mifuleni m'thanthwe,
nayendetsa madzi ngati mitsinje.
17Komabe iwo adapitiriza kumchimwira,
naukira Mulungu Wopambanazonse m'chipululu muja.
18 Eks. 16.2-15; Num. 11.4-23, 31-35 Iwo adayesa Mulungu m'mitima mwao,
pomuumiriza kuti aŵapatse chakudya chimene ankakhumba.
19Adalankhula motsutsana ndi Mulungu nati,
“Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya
m'chipululu muno?
20Paja adamenya thanthwe,
kotero kuti madzi adatumphuka,
ndipo mitsinje idadzaza.
Kodi angathenso kutipatsa ife anthu ake buledi
kapena kutipezera nyama?”
21Nchifukwa chake Chauta atamva zimenezi,
adapsa mtima kwambiri,
adayatsira moto Yakobe,
napambana kukwiyira Israeleyo,
22popeza kuti sadadalire Mulungu,
sadakhulupirire mphamvu zake zopulumutsa.
23Komabe Iye adalamula mitambo yamumlengalenga,
natsekula zitseko zakumwamba.
24 Lun. 16.20-29; Yoh. 6.31 Poŵagwetsera mana kuti adye,
adaŵapatsa tirigu wakumwamba.
25Motero anthu adadya buledi wa angelo,
ndipo Mulungu adaŵatumizira chakudya chochuluka.
26Adakunthitsa mphepo yakuvuma mu mlengalenga,
adatulutsa mphepo yakumwera ndi mphamvu zake.
27Adaŵagwetsera nyama yochuluka ngati fumbi,
mbalame zochuluka ngati mchenga wakunyanja.
28Adalola kuti zigwere pakati pa zithando zao,
konsekonse kumalo kumene ankakhalako.
29Motero adadya nakhuta kwambiri,
popeza kuti adaŵapatsa zakudya zimene ankakhumba.
30Koma nkhuli yao isanathe,
asanameze nkumeza komwe chakudya chaocho,
31mkwiyo wa Mulungu udaŵayakira,
ndipo adapha amphamvu onse pakati pao,
adapha anyamata abwinoabwino onse a mu Israele.
32Ngakhale zinali chomwecho,
iwo adapitirirabe kuchimwa,
sadakhulupirire ngakhale adaona zodabwitsa zake.
33Choncho Mulungu adadula masiku ao
kuti azimirire ngati mpweya,
adadula zaka zao
kuti zithere m'zoopsa.
34Pamene ankapha ena,
otsalira ankayamba kumufunafuna.
Ankalapa namafunafuna Mulungu ndi mtima wao wonse.
35Adakumbukira kuti Mulungu ndi thanthwe loŵateteza,
kuti Mulungu Wopambanazonse ndiye Mpulumutsi wao.
36Koma iwo adamthyasika ndi pakamwa pao,
adamnamiza ndi lilime lao.
37 Ntc. 8.21 Mtima wao sunali wokhulupirika kwa Iye.
Sadasunge chipangano chake.
38Komabe pakuti Mulungu ngwachifundo,
adaŵakhululukira machimo ao,
ndipo sadaŵaononge.
Kaŵirikaŵiri ankadziletsa kukwiya,
sadalole kuti mkwiyo wake wonse uyake.
39Ankakumbukira kuti iwo anali anthu chabe,
ngati mphepo yopita imene siibwereranso.
40Kaŵirikaŵiri ankamuukira m'chipululu,
ankamumvetsa chisoni.
41Kaŵirikaŵiri ankamuyesa,
ankamputa Woyera wa Israele.
42Sadakumbukire mphamvu zake
kapena tsiku limene adaŵaombola kwa adani ao,
43pamene Iye adachita zizindikiro zamphamvu ku Ejipito,
ndiponso zozizwitsa zake ku dera la ku Zowani.
44 Eks. 7.17-21 Paja Mulungu adasandutsa madzi a mitsinje yao
kuti akhale magazi,
kotero kuti Aejipito sadathe kumwa madziwo.
45 Eks. 8.20-24; Eks. 8.1-6 Adaŵatumira nthenje za ntchentche
zimene zidaŵazunza,
ndiponso achule amene adasakaza dziko lao.
46 Eks. 10.12-15 Adalola kuti kapuchi adye mbeu zao
ndiponso kuti dzombe lidye zonse za m'minda mwao.
47 Eks. 9.22-25 Adaononga mphesa zao ndi matalala
ndiponso mitengo yao yankhuyu ndi chisanu.
48Adalola kuti ng'ombe zao zife ndi matalala
ndi kuti nkhosa zao zife ndi zing'aning'ani.
49Adagwetsa moto wa ukali wake pa iwo:
adaŵapsera mtima naŵakwiyira
nkuŵagwetsera mavuto.
Zimenezi zinali ngati gulu la angelo oononga.
50Adalola kukwiya, osadziletsa,
sadaŵapulumutse ku imfa,
koma adapereka moyo wao ku miliri.
51 Eks. 12.29 Adapha ana achisamba onse a Aejipito,
ana oyamba a mphamvu zao,
m'zithando za zidzukulu za Hamu.
52 Eks. 13.17-22 Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa,
naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta.
53 Eks. 14.26-28 Adaŵatsogolera bwino lomwe
kotero kuti sanalikuwopa,
koma nyanja idamiza adani ao.
54 Eks. 15.17; Yos. 3.14-17 Adaŵafikitsa ku dziko lake loyera,
ku dziko lamapiri limene adaŵagonjetsera
ndi dzanja lake lamphamvu.
55 Yos. 11.16-23 Adapirikitsa mitundu ina ya anthu,
kuŵachotsa m'njira.
Adagaŵagaŵa dziko la anthuwo kuti likhale la anthu ake,
adakhazikitsa mafuko a Israele m'midzi ya anthuwo.
56 Owe. 2.11-15 Komabe Aisraele adamuputa
ndi kumuukira Mulungu Wopambanazonse,
sadasunge malamulo ake,
57koma iwo adakhala okanika ndi osakhulupirika
monga makolo ao.
Adapotoka ngati uta wosakhulupirika.
58Iwo adakwiyitsa Mulungu
ndi akachisi ao opembedzerako mafano ku mapiri.
Adamupsetsa mtima chifukwa cha mafano ao osemawo.
59Pamene Mulungu adamva zimenezi,
adakwiya kwambiri,
ndipo adakana Aisraele kotheratu.
60 Yos. 18.1; Yer. 7.12-14; 26.6 Adasiya malo ake a Silo kumene ankakhala,
adasiya hema limene ankakhalamo pakati pa anthu,
61 1Sam. 4.4-22 ndipo adalola adani athu
kuti alande Bokosi la Chipangano chake,
limene linali chizindikiro cha mphamvu zake
ndi ulemerero wake.
62Chifukwa adakwiyira anthu ake,
adalola kuti anthu akewo aphedwe pa nkhondo.
63Nkhondo yoyaka ngati moto idaononga anyamata ao,
ndipo atsikana ao adasoŵa oŵaimbira nyimbo zaukwati.
64Ansembe ao omwe adaphedwa ndi lupanga,
ndipo akazi ao amasiye sadaŵalole kulira maliro.
65Pomaliza Ambuye adachita ngati kudzuka kutulo,
ngati munthu wamphamvu wofuula chifukwa choledzera.
66Tsono Mulungu adaŵapirikitsa adani ake,
naŵachititsa manyazi anthaŵizonse.
67Adakana banja la Yosefe,
sadasankhule fuko la Efuremu.
68Koma adasankhula fuko la Yuda,
ndiponso phiri la Ziyoni limene amalikonda.
69Adamanga malo ake opatulika
ngati malo ake akumwamba,
okhazikika ngati dziko lapansi mpaka muyaya.
70 1Sam. 16.11, 12; 2Sam. 7.8; 1Mbi. 17.7 Mulungu adasankhula Davide mtumiki wake,
ndipo adakamtenga ku makola a nkhosa.
71Adamtenga kumene ankaŵeta nkhosa
zimene zinali ndi ana,
kuti adzakhale mbusa wa Yakobe, fuko lake,
wa Israele, choloŵa chake.
72Davide adaŵasamala ndi mtima wolungama,
naŵatsogolera ndi dzanja lake mwaluso.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.