1Inu Chauta, mukumbukire Davide
ndi mavuto onse amene adaŵapirira.
2Adalumbira kwa Inu Chauta,
nalonjeza kwa Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe kuti,
3“Ndithu sindidzaloŵa m'nyumba mwanga,
kapena kukagona pabedi panga,
4sindidzalola kuti ndikhale m'tulo
kapena kuti zikope zanga ziwodzere,
5mpaka nditapezera Chauta malo,
malo oti Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe azikhalamo.”
6 2Mbi. 6.41, 42 Tidamva za bokosi lachipangano ku Efurata,
tidalipeza m'minda ya ku Yaara.
7“Tiyeni tipite kumalo kumene Chauta amakhala.
Tiyeni tikapembedze ku mpando wake wachifumu.”
8Dzambatukani, Inu Chauta,
ndi kupita ku malo anu kumene mumakhala,
Inuyo pamodzi ndi bokosi lachipangano
lofanizira mphamvu zanu.
9Ansembe anu avale chilungamo ngati nsalu,
anthu anu oyera mtima afuule ndi chimwemwe.
10Chifukwa cha zimene mudalonjeza
kwa mtumiki wanu Davide,
musakane nkhope ya wodzozedwa wanu.
11 2Sam. 7.12-16; 1Mbi. 17.11-14; Mas. 89.3, 4; Ntc. 2.30 Chauta adalumbirira Davide momtsimikizira,
ndipo sadzasintha, adati,
“Ndidzakhazika pa mpando wachifumu
mmodzi mwa ana ako aamuna.
12Ngati ana ako aamuna asunga chipangano changa
ndi malamulo anga amene ndidzaŵaphunzitsa,
ana aonso adzakhala pa mpando wako wachifumu
mpaka muyaya.”
13Chauta wasankhula Ziyoni,
akufuna kuti akhale malo ake okhalamo.
14Akuti,
“Ameneŵa ndiwo malo anga opumuliramo mpaka muyaya.
Ndidzakhala kuno chifukwa ndakufunitsitsa.
15“Ndidzadalitsa kwambiri mzinda wa Ziyoni
poupatsa zosoŵa zake,
anthu ake osauka, ndidzaŵapatsa chakudya chokwanira.
16Ansembe ake ndidzaŵaveka chipulumutso,
anthu ake oyera mtima adzafuula ndi chimwemwe.
17 1Maf. 11.36 “Davide ndidzammeretsera chiphukira kumeneko.
Ndamkonzera nyale wodzozedwa wanga.
18Adani ake ndidzaŵaveka manyazi ngati nsalu,
koma iye yekhayo adzavala chisoti choŵala chachifumu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.