Yoh. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Abale ake a Yesu sadamkhulupirire

1Pambuyo pake Yesu ankayendera dera la Galileya. Sadafune kukayendera dera la Yudeya, chifukwa akuluakulu a Ayuda ankafuna kumupha.

2 chili pafupi.

3Tsono abale ake a Yesu adamuuza kuti, “Bwanji muchokeko kuno, mupite ku Yudeya kuti ophunzira anu kumeneko nawonso akaone ntchito zamphamvu zimene mukuchitazi.

4Munthu sachita kanthu m'seri akafuna kudziŵika ndi anthu. Popeza kuti Inu mukuchita ntchito zoterezi, mudziwonetse poyera pamaso pa anthu onse.”

5(Ndiye kuti abale akewo ankatero chifukwa ngakhale iwo omwe sankamukhulupirira.)

6Yesu adaŵauza kuti, “Nthaŵi yanga siinafikebe, koma yanu ndi nthaŵi iliyonse.

7Anthu ongokonda zapansipano sangadane nanu, koma amadana ndi Ine, chifukwa ndimapereka umboni wosonyeza kuti ntchito zao nzoipa.

8Inuyo pitani kuchikondwereroko. Ine sindipitako ku chikondwerero chimenechi, chifukwa nthaŵi yanga yoyenera siinafike.”

9Yesu atanena zimenezo, adatsalira m'Galileya.

Yesu apita ku chikondwerero cha Misasa

10Koma abale ake atapita ku chikondwerero cha Misasa chija, Yesu nayenso adapitako. Sadapite moonekera, koma mobisika.

11Akulu a Ayuda ankamufunafuna kuchikondwereroko, nkumafunsana kuti, “Kodi amene uja ali kuti?”

12Ndipo panali manong'onong'o ambiri okamba za Iye pakati pa khamu la anthu. Ena ankanena kuti, “Ndi munthutu wabwino.” Koma ena ankati, “Iyai, amangosokeza anthu ameneyu.”

13Komabe panalibe munthu wolankhula poyera za Iye, chifukwa choopa akulu a Ayuda.

14Chikondwerero chija chikali pakati, Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu nayamba kuphunzitsa.

15Akulu a Ayuda adadabwa nati, “Bwanji munthu ameneyu ali ndi nzeru zotere, pamene sadaphunzire konse?”

16Yesu adati, “Zimene ndimaphunzitsa si zangatu ai, ndi za Atate amene adandituma.

17Aliyense wofuna kuchita kufuna kwa Mulungu, adzadziŵa ngati zimene Ine ndimalankhula nzochokera kwa Mulungu kapena kwa Ine ndekha.

18Amene amangolankhula zakezake, amadzifunira yekha ulemu. Koma yemwe amafunira ulemu amene adamtuma, ameneyo ndiye woona, ndipo mumtima mwake mulibe chinyengo.

19Kodi suja Mose adakupatsani Malamulo a Mulungu? Komabe palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akuŵatsata. Nanga mukufuniranji kundipha?”

20Koma khamu la anthu lidamuyankha kuti, “Wagwidwa ndi mizimu yoipa Iwe. Akufuna kukupha ndani?”

21Yesu adati, “Ndinangochita ntchito yozizwitsa imodzi yokha, nonsenu nkumadabwa.

22

41Ena ankanena kuti, “Ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.” Koma ena ankanena kuti, “Kodi Mpulumutsiyo nkuchokera ku Galileya ngati?

422Sam. 7.12; Mik. 5.2 Suja Malembo akuti kholo lake ndi mfumu Davide? Ndipo sujanso akuti adzachokera ku mudzi wa Betelehemu kumene Davideyo anali?”

43Choncho khamu la anthu lidagaŵikana chifukwa cha Iye.

44Ena ankafuna kumgwira, koma panalibe amene adamkhudza.

Kusakhulupirira kwa akulu a Ayuda

45Asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja adabwerera kwa akulu a ansembe ndi kwa Afarisi aja. Iwo adafunsa asilikaliwo kuti, “Bwanji simudabwere naye?”

46Asilikali aja adayankha kuti, “Palibenso wina amene adalankhulapo ngati munthu ameneyo nkale lonse.”

47Apo Afarisi adati, “Kani inunso wakunyengani?

48Kodi mudamvapo kuti pakati pa akuluakulu kapena pakati pa Afarisi alipo wokhulupirira amene uja?

49Koma anthu wambaŵa sadziŵa Malamulo a Mose; ngotembereredwa basi!”

50 Yoh. 3.1, 2 Tsono Nikodemo, mmodzi mwa Afarisi, yemwe uja amene kale adaapita kwa Yesu, adafunsa anzakewo kuti,

51“Kodi Malamulo athu amatilola kuweruza munthu tisanamve mau ake kuti tidziŵe zimene wachita?”

52Iwo adati, “Kani iwenso ndiwe wa ku Galileya? Kafunefune m'Malembo ndipo udzaona kuti palibe mneneri wochokera ku Galileya.”

[

53Pamenepo anthu onse adabwerera kwao.]

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help