2 Tim. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za msilikali wabwino wa Yesu Khristu

1Tsono iwe, mwana wanga, limbika pakugwiritsa ntchito mphatso zaulere zimene uli nazo mwa Khristu Yesu.

2Mau amene udamva kwa ine pamaso pa mboni zambiri, uŵasungitse anthu okhulupirika amene adzathe kuŵaphunzitsanso kwa ena.

3Umve nao zoŵaŵa monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.

4Msilikali amene akumenya nkhondo sasamalako ntchito zakumudzi, chifukwa iye amangofuna kukondweretsa mkulu wa ankhondo.

5Munthu wothamanga pa mpikisano wa liŵiro, sangalandire mphotho ngati sathamanga motsata malamulo a mpikisanowo.

6Mlimi wogwira ntchitoyo molimbika, ndiye ayenera kukhala woyamba kulandira nao zipatso.

7Uganizire bwino zimene ndikunenazi, Ambuye adzakuthandiza kumvetsa zonse.

8Kumbukira Yesu Khristu amene adauka kwa akufa, ndiponso anali mmodzi mwa zidzukulu za Davide, monga umaphunzitsira Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika.

9Chifukwa cha Uthenga Wabwinowu ndimamva zoŵaŵa, mpakanso kumangidwa m'ndende, ngati chigaŵenga. Koma mau a Mulungu sangathe kumangidwa.

10Motero tsono ndimapirira zonsezi chifukwa cha anthu amene Mulungu adaŵasankha, kuti iwonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu, ndi kulandira ulemerero wamuyaya.

11Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu:

“Ngati tidafa pamodzi naye,

tidzakhala moyonso pamodzi naye.

12 Mt. 10.33; Lk. 12.9 Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye.

Ngati ife timkana, Iyenso adzatikana.

13Ngati ndife osakhulupirika,

Iye amakhalabe wokhulupirika,

pakuti sangathe kudzitsutsa.”

Za wantchito wovomerezedwa ndi Mulungu

14Uziŵakumbutsa zimenezi anthu, ndipo uŵachenjeze kolimba pamaso pa Mulungu kuti asamakangana pa za mau. Kutero kulibe phindu, koma kumangotayikitsa anthu amene akumva kukanganako.

15Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

16Koma nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, uzipewe, pakuti anthu olankhula zotere adzanka nanyozeranyozera Mulungu.

17Ndipo zophunzitsa zao zidzaloŵerera mu anthu ngati kunyeka kwa chilonda. Mwa anthu ameneŵa wina ndi Himeneo, wina ndi Fileto.

18Iwowo adasokera nkusiya choona. Amaphunzitsa kuti kuuka kwa akufa kudachitika kale. Motero amasokoneza chikhulupiriro cha anthu ena.

19Num. 16.5 Komabe maziko olimba, amene Mulungu adaŵaika, ngokhazikika, ndipo mau olembedwapo ndi aŵa: “Ambuye amadziŵa amene ali ao”, ndiponso, “Aliyense wotamanda dzina la Ambuye, asiye zosalungama.”

20M'nyumba yaikulu simukhala ziŵiya zagolide kapena zasiliva zokhazokha; mumakhalanso zamtengo kapena zadothi. Zina zimakhala za ntchito zolemerera, zina za ntchito wamba.

21Tsono munthu akadziyeretsa nkusiya zotsikazi, adzakhala ngati chiŵiya cha ntchito zolemerera. Adzakhala wopatulika ndi wofunika zedi kwa Ambuye ake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.

22Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.

23Uzikana matsutsano opusa ndi opanda nzeru, paja ukudziŵa kuti zotere zimautsa mikangano.

24Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.

25Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.

26Pamenepo nzeru zao zidzabweramo, ndipo adzapulumuka mu msampha wa Satana, amene adaaŵagwira kuti azichita zofuna zake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help