1Chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Yehu, Yowasi adaloŵa ufumu ndipo adalamulira zaka makumi anai ku Yerusalemu. Mai wake anali Zibiya wa ku Beereseba.
2Tsono Yowasiyo adachita zolungama pamaso pa Chauta masiku onse a moyo wake, chifukwa choti Yehoyada, wansembe uja, ankamlangiza.
3Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu adapitirirabe kupereka nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo.
4 Eks. 30.11-16 Nthaŵi ina mfumu Yowasi adauza ansembe kuti, “Musunge bwino ndalama zonse zimene zimaperekedwa ngati zopereka zopatulika ku Nyumba ya Chauta, ndiye kuti ndalama za msonkho wa munthu aliyense, ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Chauta.
5Wansembe aliyense aziyang'anira ndalama zopereka anthu amene iye amaŵatumikira, ndipo azigwiritse ntchito pokonza Nyumba paliponse pamene pafunika kukonza.”
6Koma pomafika chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, ansembewo anali asanakonzebe Nyumbayo.
7Nchifukwa chake mfumu Yowasi adaitana wansembe Yehoyada ndi ansembe ena, naŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza Nyumbayi? Kuyambira tsopano, musasungenso ndalama za anthu amene mumaŵatumikira, koma muzipereke kuti akonzere Nyumbayi.”
8Motero ansembe aja adavomera kuti sadzatenganso ndalama kwa anthu, ndipo kuti sindiwo adzakonza Nyumbayo, koma ena.
9Tsono wansembe Yehoyada adatenga bokosi, ndipo adaboola chivundikiro chake, naika bokosilo pambali pa guwa cha ku dzanja lamanja kwa aliyense woloŵa m'Nyumba ya Chauta. Ansembe amene anali pa khomo ankaponyamo ndalama zonse zimene anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Chauta.
10Nthaŵi zonse ankati akaona kuti m'bokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera kudzaŵerenga ndi kumanga m'matumba ndalama zimene zinali m'Nyumba ya Chauta.
11Tsono ndalamazo ataziyesa, ankazipereka kwa akapitao okonzetsa Nyumba ya Chauta aja. Iwowo ankalipira amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba, amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Chautayo.
12Ankalipiranso amisiri omanga ndi miyala ndi osema miyala, ndiponso ankagula mitengo ndi miyala yokumba yokonzera Nyumba ya Chauta, kudzanso zinthu zina zilizonse zofunikira poikonza.
13Koma mabeseni asiliva a ku Nyumba ya Chauta, ngakhale mbano, mbale, malipenga, ziŵiya zagolide ndi zasiliva, sadagule ndi ndalama zimene zinkabwera ku Nyumba ya Chauta,
14pakuti zimenezo ankalipirira antchito okonza Nyumba ya Chauta.
152Maf. 22.7 Anthu amene ankaŵapatsa ndalama zolipirira antchito okonza Nyumbawo, sankaŵafunsa kuti afotokoze za kamwazidwe ka ndalamazo, popeza kuti anali anthu okhulupirika.
16Lev. 7.7 Ndalama zoperekera nsembe zolipira mlandu ndiponso ndalama zoperekera nsembe zopepesera machimo, sankaziponya m'bokosi la m'Nyumba ya Chauta. Zimenezo zinali za ansembe.
17Nthaŵi imeneyo Hazaele, mfumu ya ku Siriya, adathira nkhondo mzinda wa Gati, ndipo adaulanda mzindawo. Kenaka Hazaele adatsimikiza mtima kuti akathire nkhondo ku Yerusalemu.
18Koma Yowasi mfumu ya ku Yuda adatenga zopereka zonse zopatulika zimene Yehosafati, Yehoramu ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a ku Yuda, adazipereka kwa Mulungu pamodzi ndi mphatso zakezake zopatulika, kudzanso golide yense amene adampeza m'nyumba zosungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndi cha ku nyumba ya mfumu. Zonsezo adazitumiza ngati mphatso zopepesera Hazaele mfumu ya ku Siriya. Tsono Hazaele adazilandira nachokako ku Yerusalemu.
19Tsono ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
20Nduna zake zidamchita chiwembu, ndipo zidamupha ku linga la Milo limene lili pa njira yotsikira ku Sila.
21Yosakara, mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi, mwana wa Somere, ndiwo amene adachita zimenezi. Ndipo adakamuika m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide. Tsono Amaziya, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.