1Chauta adauza Mose kuti,
2“Lamula Aisraele, ndipo uŵauze kuti, ‘Muzisamala kupereka kwa Ine pa nthaŵi yake zopereka zanga, chakudya changa cha nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo londikomera.’
3Ndipo uŵauzenso kuti, nsembe yotentha pa moto, yoti muzipereka kwa Chauta ndi iyi: Muzipereka anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, kuti akhale nsembe yosalekeza.
4Mwanawankhosa mmodzi muzimpereka m'maŵa, winayo muzimpereka madzulo.
5Muziperekanso kilogaramu limodzi la ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta aolivi oyenga bwino okwanira lita limodzi.
6Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza imene idalamulidwa pa phiri la Sinai, kuti itulutse fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
7Chopereka cha chakumwa pa nkhosa iliyonse chikhale yokwanira lita limodzi. Muzithira vinyo waukaliyo m'malo opatulika, kuchipereka kwa Chauta.
8Mwanawankhosa wina uja muzimpereka madzulo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa zonga zam'maŵa zija. Imeneyi ikhalenso nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.
Zopereka za pa Sabata9“Pa tsiku la Sabata muzipereka anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema. Muziperekanso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka cha chakudya, ndipo muziperekanso chopereka cha chakumwa.
10Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata lililonse, kuwonjezera pa nsembe zopsereza ndi pa zopereka za chakumwa za tsiku ndi tsiku zija.
Zopereka za tsiku loyamba la mwezi11“Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse, muzipereka nsembe yopsereza kwa Chauta. Nsembeyo ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa imodzi yamphongo, anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi, opanda chilema.
12Chopereka cha chakudya ikhale ya ufa wosalala wa makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, pa ng'ombe yamphongo iliyonse. Muperekenso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yamphongoyo,
13ndiponso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza yotulutsa fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.
14Chopereka cha chakumwa chikhale cha vinyo wokwanira malita aŵiri pa ng'ombe yamphongo iliyonse, ya vinyo wokwanira lita limodzi ndi theka pa nkhosa yamphongoyo, ndi ya vinyo wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse, pa miyezi yonse ya chaka.
15Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta. Aipereke kuwonjezera pa nsembe zopsereza ndi zopereka za zakumwa za tsiku ndi tsiku.
Zopereka za pa tsiku la chikondwerero cha buledi wosafufumitsa(Lev. 23.5-14)16 Eks. 12.1-13; Deut. 16.1, 2 “Tsiku la 14 la mwezi woyamba, ndi la Paska ya Chauta.
17Eks. 12.14-20; 23.15; 34.18; Deut. 16.3-8 Ndipo pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, ndi tsiku lachikondwerero. Azidya buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri.
18Pa tsiku loyamba pazikhala msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito yotopetsa,
19koma mupereke nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya Chauta. Ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa yamphongo imodzi ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri a chaka chimodzi, opanda chilema.
20Muperekenso chopereka cha chakudya wosakaniza ndi mafuta. Ufa wake ukhale wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo,
21ndiponso wa makilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense.
22Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yochitira mwambo wopepesera machimo anu.
23Muzipereka zimenezi kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zopereka nthaŵi yam'maŵa.
24Motero pa masiku asanu ndi aŵiri muzipereka tsiku lililonse chakudya cha nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Muchipereke kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija pamodzi ndi zopereka za chakumwa.
25Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa.
Zopereka za tsiku la chikondwerero cha kholola(Lev. 23.15-22)26 Eks. 23.16; 34.22; Deut. 16.9-12 “Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Chauta, pa tsiku la chikondwerero cha masabata, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa,
27koma mupereke nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi.
28Muperekenso chopereka cha chakudya wosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo,
29ndiponso wa kilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense.
30Muperekenso tonde mmodzi wochitira mwambo wopepesera machimo anu.
31Mupereke zimenezi pamodzi ndi zopereka za chakumwa, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija ndi chopereka cha chakudya. Musamale kuti nyamazo zikhale zopanda chilema.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.