Mk. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu adyetsa anthu oposa zikwi zinai(Mt. 15.32-39)

1Pasanapite nthaŵi yaitali anthu ambirimbiri adasonkhananso. Pamene Yesu adaona kuti anthuwo alibe chakudya, adaitana ophunzira ake naŵauza kuti,

2“Ndikuŵamvera chifundo anthuŵa, chifukwa akhala nane masiku atatu tsopano, ndipo alibe chakudya.

3Ndikangoŵabweza kwao ali ndi njala chonchi, alefuka pa njira, chifukwa ena achokera kutali.”

4Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Anthu ochuluka chotereŵa munthu angaŵapezere bwanji chakudya chokwanira, kuthengo ngati kuno?”

5Yesu adaŵafunsa kuti, “Buledi ndiye muli naye mngati?” Iwo aja adati, “Msanu ndi muŵiri.”

6Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi. Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, adathokoza Mulungu, namunyemanyema nkumupereka kwa ophunzira ake kuti akagaŵire anthu aja. Ophunzira aja adaŵagaŵiradi anthuwo.

7Adaalinso ndi tinsomba toŵerengeka. Yesu adathokoza Mulungu chifukwa cha tinsombato, nalamula ophunzira ake kuti atiperekenso kwa anthu aja.

8Anthu adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nadzaza madengu asanu ndi aŵiri.

9Anthu amene adaali pamenepo, amuna okha adaalipo ngati zikwi zinai.

10Pambuyo pake Yesu adatsazikana nawo anthu aja, kenaka Iye ndi ophunzira ake adaloŵa m'chombo napita ku dera la Dalamanuta.

Afarisi apempha chizindikiro chozizwitsa(Mt. 16.1-4; Lk. 11.16, 29)

11 Pakutero ankangofuna kumutchera msampha.

12Mt. 12.39; Lk. 11.29Yesu adadzumira mu mtima nati, “Kodi bwanji anthu a mbadwo uno amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa? Ndithu ndikunenetsa kuti anthu a mbadwo unowu sadzachiwona chizindikiro akufunacho.”

13Atatero, Yesu adaŵasiya, naloŵanso m'chombo kuwolokera ku tsidya lina.

Za zophunzitsa zonama za Afarisi ndi za Herode(Mt. 16.5-12; Lk. 12.1)

14Ophunzira a Yesu anali ataiŵala kutenga buledi, kotero kuti m'chombomo adaali ndi buledi mmodzi yekha.

15Lk. 12.1Tsono Yesu adayamba kuŵalangiza kuti, “Muchenjere nacho chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi cha Herode.”

16Apo ophunzirawo adayamba kukambirana nkumati, “Akuterotu chifukwa tilibe buledi.”

17Yesu adaadziŵa zimene iwo ankanena. Ndiye adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukukambirana zakuti mulibe buledi? Kodi mpaka pano simunazindikirebe kapena kumvetsa? Kani mitu yanu ndi youma, eti?

18Yer. 5.21; Ezek. 12.2; Mk. 4.12Maso muli nawo, kodi simuwona? Ndipo makutu muli nawo, kodi simumva? Kodi inu simukukumbukira zijazi?

19Muja ndidaanyemanyema buledi msanu kuti ndidyetse anthu zikwi zisanumu, kodi mudaadzaza madengu angati a zotsala?” Ophunzirawo adati, “Madengu khumi ndi aŵiri.”

20Yesu adaŵafunsanso kuti, “Nanga muja ndidaanyemanyema buledi msanu ndi muŵiri ndi kudyetsa anthu zikwi zinaimu, mudaatola madengu angati a zotsala?” Iwo adati, “Madengu asanu ndi aŵiri.”

21Apo Yesu adati, “Nanga ndiye simunamvetsebe?”

Yesu achiritsa wakhungu ku Betsaida

22Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Betsaida. Kumeneko anthu adabwera ndi munthu wakhungu, napempha Yesu kuti amchiritse pomkhudza.

23Yesu adamgwira dzanja, natuluka naye kunja kwa mudzi. Adapaka malovu m'maso mwa munthuyo, namsanjika manja nkumufunsa kuti, “Kodi ukuwona kanthu?”

24Munthu uja adaŵeramuka nati, “Ndikuwona anthu akuyenda, koma akuwoneka ngati mitengo.”

25Yesu adamuikanso manja kumaso kwake. Munthu uja adayang'anitsitsa ndipo adachira, nayamba kumapenya zonse bwino lomwe.

26Yesu adamuuza kuti apite kwao, namlamula kuti, “Usaloŵe ndi m'mudzi momwemu.”

Zimene Petro adanena za Yesu(Mt. 16.13-20; Lk. 9.18-21)

27Yesu ndi ophunzira ake adapita ku midzi ya ku Kesareya-Filipi. Pa njira Yesu adafunsa ophunzira akewo kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?”

28Mk. 6.14, 15; Lk. 9.7, 8Iwo adayankha kuti, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu mmodzi mwa aneneri.”

29Yoh. 6.68, 69Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Petro adamuyankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja.”

30Yesu adaŵalamula kuti asauze munthu wina aliyense za Iye.

Yesu aneneratu za kufa ndi kuuka kwake(Mt. 16.21-23; Lk. 9.22-27)

31Yesu adayamba kuphunzitsa ophunzira ake kuti, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda, ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma patapita masiku atatu adzauka.”

32Zimenezi adazinena mosabisa konse. Apo Petro adamtengera pambali, nayamba kumdzudzula.

33Koma Yesu adacheuka, nayang'ana ophunzira ake ena aja, ndipo adadzudzula Petro. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.”

Za kusenza mtanda ndi kutsata Yesu(Mt. 16.24-28; Lk. 9.23-27; Yoh. 12.25)

34 Mt. 10.38; Lk. 14.27 Pambuyo pake Yesu adaitana khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira aja kuti adze pafupi naye, ndipo adaŵauza kuti, “Munthu wofuna kutsana Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata.

35Mt. 10.39; Lk. 17.33; Yoh. 12.25Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.

36Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse za pansi pano, iyeyo nkutaya moyo wake?

37Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?

38Tsono ngati munthu achita manyazi ndi Ine ndiponso ndi mau anga pamaso pa anthu ochimwa a makonoŵa amene ali osakhulupirika, ameneyo nanenso Mwana wa Munthune ndidzachita naye manyazi pamene ndidzabwera pamodzi ndi angelo oyera, ndili ndi ulemerero wa Atate anga.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help