2 Mbi. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aejipito athira nkhondo dziko la Yuda(1 Maf. 14.25-28)

1Rehobowamu atangokhazikitsa ulamuliro wake ndi kuulimbitsa, iyeyo pamodzi ndi Aisraele onse adayamba kusiya malamulo a Chauta.

2Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisake mfumu ya ku Ejipito adathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu chifukwa chakuti Aisraele adaakhala osakhulupirika kwa Chauta.

3Sisakeyo adabwera ndi magaleta ankhondo okwanira 1,200 ndi anthu okwera pa akavalo 60,000. Anthu ake anali osaŵerengeka amene adadza nawo kuchokera ku Ejipito, Libiya, Sukimu ndi Etiopiya.

4Adalanda mizinda yamalinga ya ku Yuda, nakafika mpaka ku Yerusalemu.

5Tsono mneneri Semaya adadza kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a ku Yuda, amene anali atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, ndipo adaŵauza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Inu mwandisiya Ine, ndiye nanenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisake.’ ”

6Apo atsogoleri a Aisraele pamodzi ndi mfumu yomwe adadzichepetsa, nati, “Chauta ndi wolungama.”

7Tsono Chauta ataona kuti anthuwo adzichepetsa, adauzanso Semaya kuti, “Anthuŵa adzichepetsa, sindidzaŵaononga ai, koma ndidzaŵapulumutsa. Sindidzaukwiyira mzinda wa Yerusalemu, motero Sisake sadzauwononga konse.

8Komabe adzakhala akapolo a Sisakeyo, kuti anthuwo adziŵe kusiyanitsa pakati pa kutumikira Ine ndi kutumikira mafumu a maiko achilendo.”

9 1Maf. 10.16, 17; 2Mbi. 9.15, 16 Tsono Sisake, mfumu ya ku Ejipito, adabwera kudzathira Yerusalemu nkhondo. Adalanda chuma cha ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi chuma cha ku nyumba ya mfumu. Adatenga zonse, ngakhalenso zishango zomwe zagolide zimene Solomoni adaapanga.

10Pambuyo pake mfumu Rehobowamu adapanga zishango zamkuŵa m'malo mwake, nazipereka kwa m'manja mwa akapitao a alonda amene ankalonda pakhomo pa nyumba ya mfumu.

11Tsono nthaŵi zonse mfumu ikamaloŵa m'Nyumba ya Chauta, alondawo ankatenga zishango, kenaka nkumazibwezera ku chipinda cha alonda.

12Tsono mfumuyo itadzichepetsa, Chauta adaleka kufuna kuŵaononga kwathunthu. Motero zinthu zinkayenda bwino ku Yuda.

Za ufumu wa Rehobowamu mwachidule

13Mfumu Rehobowamu adakhazikitsa ufumu wake ku Yerusalemu. Anali wa zaka 41 nthaŵi imene ankayamba kulamulira. Adalamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Chauta adausankha pakati pa mafuko onse a Israele kuti azimpembedza kumeneko. Mai wake anali Naama, Mwamoni.

14Koma Rehobowamuyo adachita zoipa, popeza kuti mtima wake sudafunitsitse Chauta.

15Tsono ntchito za Rehobowamu kuyambira poyamba mpaka pomaliza, paja zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Semaya ndiponso m'buku la mbiri ya mneneri Ido. Panali nkhondo zosakata pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu.

16Rehobowamu adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Tsono Abiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help