Daniel Greek 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Daniele ndi anzake ku bwalo la Nebukadinezara

1Chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadzazinga mzinda wa Yerusalemu, ndipo adauthira nkhondo.

2Ambuye adamthandiza kugonjetsa Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, ndi kulanda ziŵiya zina za ku Nyumba ya Mulungu. Ndipo adapita nazo ku nyumba ya milungu yake ku Babiloni, nakaziika m'zipinda mosungira chuma.

3Tsono mfumu idalamula Asipenazi, nduna yake yaikulu, kuti atengeko akapolo ena achinyamata Achiisraele, a m'banja lachifumu ndiponso a m'mabanja a akuluakulu.

4Anyamata ameneŵa adayenera kukhala okongola, opanda chilema, aluso pa nzeru zonse, achangu pophunzira, ochenjera ndiponso okhoza pa ntchito yotumikira ku bwalo la mfumu. Adayeneranso kuŵaphunzitsa kulemba ndi kuŵerenga chilankhulo cha Chibabiloni.

5Mfumu idalamula kuti masiku onse aziŵapatsa chakudya chimene mfumu inkadya ndiponso vinyo amene mfumu inkamwa. Idalamulanso kuti aziŵaphunzitsa zaka zitatu, ndipo pakutha pa nthaŵi imeneyo, azidzatha kukatumikira ku nyumba ya mfumu.

6Mwa ameneŵa panali anyamata ena a ku Yuda. Maina ao anali aŵa: Daniele, Hananiya, Misaele ndi Azariya.

7Koma nduna yaikulu ija idaŵatcha maina atsopano: Daniele adamutcha Belitesazara, Hananiya adamutcha Sadrake, Misaele adamutcha Mesaki ndipo Azariya adamutcha Abedenego.

8Koma Daniele adatsimikiza mtima kuti sadzadzidetsa nacho chakudya chimene mfumu inkadya ndi vinyo amene mfumu inkamwa. Nchifukwa chake adapempha nduna yaikulu kuti imthandize pamenepa.

9Tsono Mulungu adafeŵetsa mtima wa ndunayo kuti imkomere mtima Daniele.

10Ndipo nduna ija idauza Daniele kuti, “Ndikuwopa mbuye wanga mfumu. Walamula ndiye chakudya ndi chakumwa chimenechi. Ndipo akakuwona kuti ndiwe woonda, kusiyana ndi anyamata a msinkhu wako, adzandidula mutu.”

11Nduna ija idaika kapitao woti aziyang'anira Daniele, Hananiya, Misaele ndi Azariya. Tsono Daniele adauza kapitaoyo kuti,

12“Mutiyeseko masiku khumi anyamata anufe. Mutipatse ndiwo zamasamba kuti tizidya ndiponso madzi kuti tizimwa.

13Tsono mudzayerekeze m'mene ife tizikaonekera ndi m'mene azikaonekera anyamata ena aja, odya chakudya chimene imadya mfumu. Ndipo anyamata anufe mudzachite nafe monga m'mene mudzaonere.”

14Kapitao uja adaŵamvera, naŵayesa masiku khumi.

15Tsono masiku khumi atatha, Daniele ndi anzake adaoneka amphamvu ndiponso athanzi kupambana anyamata ena onse amene ankadya chakudya cha kwa mfumu.

16Motero kapitao adachotsa chakudya cha kwa mfumu, pamodzi ndi vinyo amene akadayenera kumwa. Ndipo adangoŵapatsa ndiwo zamasamba chabe.

17Kunena za anyamata anai aja, Mulungu adaŵapatsa nzeru zomvetsera mau onse am'mabuku, ndiponso maphunziro ozama. Daniele analinso ndi luso lotanthauzira zinthu zoonekera anthu m'masomphenya, ndiponso maloto.

18Tsono nthaŵi idakwana imene mfumu idaika kuti akaloŵetse anyamata ku nyumba yake. Ndipo nduna ija idabwera nawo kwa Nebukadinezara.

19Mfumu idalankhula nawo, ndipo idaona kuti panalibe wina wolingana ndi Daniele, Hananiya, Misaele ndi Azariya. Motero anyamatawo adayamba kutumikira ku nyumba ya mfumu.

20Nthaŵi zonse mfumu ikaŵafunsa zinthu zolira nzeru ndi luntha, inkapeza kuti iwowo ndi opambana kwambiri amatsenga ndi oombeza a mu ufumu wake wonse.

21Daniele anali kumeneko mpaka chaka choyamba cha ufumu wa Kirusi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help