Aga. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chikhulupiriro chokha chimapatsa moyo

1Agalatiya opusa inu, adakulodzani ndani? Pamene tidakulalikirani Yesu Khristu, tidamuwonetsa poyera pamaso panu ngati wopachikidwa pa mtanda.

2Ndikufunseni chinthu chimodzi chokha: Kodi mudalandira Mzimu Woyera pakutsata Malamulo, kapena pakumva ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino?

3Kani ndinu opusa chotere? Kodi zimene Mzimu Woyera adayamba kuchita mwa inu, mukufuna kuzifikitsa pake penipeni tsopano ndi mphamvu zanuzanu?

4Kodi mudalandira zonse zija pachabe? Sindikukhulupirira kuti mpachabe.

5Kodi Mulungu amene amakupatsani Mzimu Woyera, nachita zozizwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumatsata Malamulo, kapena chifukwa mudamva ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino?

6Gen. 15.6; Aro. 4.3 Paja ponena za Abrahamu Malembo akuti, “Iye adaakhulupirira Mulungu, motero Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.”

7 Aro. 4.16 Muzindikire tsono kuti ndi anthu amene amakhulupirira omwe ali ana enieni a Abrahamu.

8Gen. 12.3 Koma Malembo adaoneratu kuti anthu a mitundu ina pakukhulupirira, Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama pamaso pake. Nchifukwa chake Malembowo adaauziratu Abrahamu Uthenga Wabwinowu wakuti, “Mwa iwe Mulungu adzadalitsa anthu a mitundu yonse.”

9Abrahamu adakhulupirira, ndipo Mulungu adamdalitsa. Motero pamodzi ndi Abrahamuyo Mulungu amadalitsanso onse okhulupirira.

10 Deut. 27.26 Onse amene amadalira ntchito za Malamulo ndi otembereredwa. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene satsata zonse zolembedwa m'buku la Malamulo.”

11Hab. 2.4 Komatu nchodziŵikiratu kuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Paja Malembo akuti, “Munthu amene ali wolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, adzakhaladi ndi moyo.”

12Lev. 18.5 Koma Malamulo akusiyana ndi chikhulupiriro, chifukwa Malembo akuti, “Munthu amene amachita zonse zolamulidwa ndi Malamulo, adzakhala ndi moyo pakutero.”

13 Deut. 21.23 Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.”

14Khristu adachita zimenezi, kuti dalitso limene Mulungu adaalonjeza Abrahamu, lipatsidwe kwa anthu a mitundu yonse kudzera mwa Khristu Yesu, ndipo kuti pakukhulupirira tilandire Mzimu Woyera amene Mulungu adaatilonjeza.

Za Malamulo ndi lonjezo

15Abale, ndikufotokozereni zimenezi pokupatsani chitsanzo cha zimene zimachitika tsiku ndi tsiku. Anthu aŵiri akapangana natsimikiza chimodzi, palibe munthu angaphwanye panganolo kapena kuwonjezapo mau.

16Tsono Mulungu adapatsa malonjezo ake kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sakunena kuti, “Ndi kwa mbeu zake” ai, ngati kuti akunena za anthu ambiri. Koma akunena kuti, “Ndi kwa mbeu yake”, popeza kuti akukamba za munthu mmodzi yekha. Ameneyu ndi Khristu.

17Eks. 12.40 Chimene ndikunena ndi ichi: Mulungu adachita chipangano, nalonjeza kuchisunga. Malamulo a Mose, amene adadza patapita zaka 430, sangathe kuchiphwanya chipanganocho ndi kuwononga lonjezo la Mulungu lija.

18Aro. 4.14Mulungu akapatsa munthu madalitso chifukwa munthuyo ndi wotsata Malamulo, ndiye kuti madalitsowo sapatsidwanso chifukwa cha lonjezo ai. Koma Mulungu adadalitsa Abrahamu chifukwa adaalonjeza kutero.

19Nanga tsono cholinga cha Malamulo chinali chiyani? Mulungu adaonjezapo Malamulo kuti azindikiritse anthu machimo, mpaka mbeu ija ya Abrahamu, imene Mulungu adaaipatsa lonjezo lija, itabwera. Mulungu adapereka Malamulowo kudzera mwa angelo, ndiponso kudzera mwa munthu wochita ntchito ya mkhalapakati.

20Tsono tikati mkhalapakati, ndiye kuti pali anthu aŵiri. Koma Mulungu ali yekha.

Za cholinga cha Malamulo

21Kodi ndiye kuti Malamulo a Mose amatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Mpang'ono pomwe. Anthu akadalandira malamulo otha kuŵapatsa moyo, pamenepo bwenzi atasanduka olungama kudzera mwa malamulowo.

22Koma Malembo akunenetsa kuti zinthu zonse zili mu ulamuliro wa uchimo, kuti pakukhulupirira Yesu Khristu, anthu okhulupirira alandiredi zimene Mulungu adalonjeza.

23Chisanafike chikhulupirirochi, tinali ngati akaidi m'manja mwa Malamulo, kudikira kuti chikhulupiriro chimene chidaati chifikecho, chiwululidwe.

24Motero Malamulowo anali ngati namkungwi wathu, mpaka atabwera Khristu, kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira.

25Popeza kuti tsopano chikhulupiriro chafika, namkungwiyo satilamuliranso.

26Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu.

27Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.

28Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.

29Aro. 4.13Ngati ndinu ake a Khristu, ndiye kuti ndinu ana a Abrahamu, oyenera kulandira zimene Mulungu adalonjeza.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help