1Nawu uthenga wa Chauta kwa Aisraele kudzera mwa Malaki.
2Aro. 9.13
Yes. 34.5-17; 63.1-6; Yer. 49.7-22; Ezek. 25.12-14; 35.1-15; Amo. 1.11, 12; Oba. 1.1-14 Chauta akuti, “Ndakukondani inu.” Koma inu mumati. “Kodi mwatikonda motani?” Chauta akunena kuti, “Kodi suja Esau ndi mbale wake wa Yakobe?3Komabe ndakonda Yakobe, koma Esau ndadana naye. Dziko lake lamapiri ndalisandutsa chipululu, dziko limene ndidampatsa ndalisandutsa la nkhandwe zam'chipululu.”
4Mwina Aedomu adzanena kuti, “Mulungu adapasula nyumba zathu, komabe ife tidzazimanganso.” Koma Chauta Wamphamvuzonse adzati, “Alekeni amangenso, Ine ndidzazigwetsanso. Anthu adzalitchula dziko loipa, la anthu amene Chauta adaŵatemberera mpaka muyaya.”
5Inu, Aisraele, mudzaziwona zimenezi ndi maso anu. Inu nomwe mudzati, “Ukulu wa Chauta umafika ngakhale kunja kwa malire a Aisraele.”
Chauta adzudzula ansembe6Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Mwana amapatsa ulemu bambo wake ndipo kapolo amaopa mbuye wake. Ngati Ine ndine bambo wanu, nanga ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiwopa kuli kuti, Ansembe inu, amene mumanyoza dzina langa. Komabe mumanena kuti, kodi dzina lanu timalinyoza bwanji?
7Mumalinyoza pakupereka chakudya chosayenera pa guwa langa lansembe. Inu mumafunsabe kuti, kodi ife takunyozani bwanji? Mwandinyoza pakuganiza kuti tebulo la Chauta nlonyozeka.”
8Deut. 15.21Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Mukaperekera nsembe nyama zakhungu, kodi si cholakwa? Mukaperekera nsembe nyama zopunduka kapena zodwala, kodi si cholakwa? Bwanamkubwa wanu mutampatsa mphatso zotero, kodi angazilandire? Kodi inuyo angakukomereni mtima?”
9Tsopano tayesani kupempha Mulungu kuti akuchitireni chifundo. Ndi mphatso zotere m'manja mwanu, kodi angakomere mtima aliyense mwa inu? Tsono Chauta Wamphamvuzonse akupitiriza kunena kuti,
10“Kudakakhala bwino kwambiri kuti wina mwa inu atsekeretu zitseko za Nyumba yanga, kuti mungayatse moto pachabe pa guwa langa. Sindikukondwera nanu, sindidzazilandira zopereka zanu.
11Dzina langa nlalikulu pakati pa mitundu ya anthu kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Kulikonse anthu amapereka nsembe zofukiza ndi mphatso zangwiro m'dzina langa. Pajatu dzina langa nlalikulu pakati pa mitundu ya anthu.
12“Koma inuyo mumalinyoza ponena kuti tebulo la Chauta nlachabechabe, ndipo chakudya chopereka pamenepo nchonyozeka.”
13Chauta Wamphamvuzonse akunenanso kuti, “Inu mumati, ‘Ha, kutopetsa zimenezi!’ Kenakanso nkumandinyodola. Mumabwera ndi nyama zakuba kapena zopunduka kapena zodwala ngati nsembe zanu, kodi Ine ndidzazilandira?
14Atembereredwe munthu wonyenga amene amayesa kuchita zimene adalumbirira popereka nsembe yoipa kwa Chauta, pamene ali nayo nkhosa yamphongo yabwino m'khola.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ine ndine Mfumu yaikulu, ndipo dzina langa nlochititsa mantha pakati pa anthu a mitundu yonse.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.