1Tamanda Chauta, iwe mtima wanga.
Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri.
Mumavala ulemu ndi ufumu.
2Mumadzifunditsa ndi kuŵala ngati chovala,
mwatambasula mlengalenga ngati hema.
3Mwamanga Nyumba yanu pa madzi akumwamba,
mitambo yaliŵiro ili ngati galeta lanu,
mumayenda pa mapiko a mphepo,
4 Ahe. 1.7 Mphepo mumazisandutsa amithenga anu,
malaŵi amoto mumaŵasandutsa atumiki anu.
5Mudakhazika dziko lapansi pa maziko ake,
kuti lisagwedezeke konse.
6Mudaliphimba ndi nyanja yozama ngati ndi chovala,
ndipo madzi adakwera mpaka pamwamba pa mapiri.
7Mutaŵadzudzula, madziwo adathaŵa,
atamva mkokomo wa bingu lanu, adamwazika.
8Mapiri adatumphuka, zigwa zidatsika,
mpaka kumene Inu mudaakonzeratu.
9Madziwo Inu mudaŵaikira malire oti asabzole,
kuti asaphimbenso dziko lapansi.
10Inu mumatumphutsa akasupe m'zigwa,
mitsinje imayenda pakati pa mapiri.
11Imapatsa nyama zonse zakuthengo madzi akumwa,
mbidzi zimapherapo ludzu.
12Mbalame zimamanga zisa pafupi ndi mitsinjeyo,
zimaimba m'nthambi za mitengo.
13Inu mumathirira mapiri
ndi madzi ochokera ku malo anu akumwamba.
Dziko lapansi ladzaza ndi madalitso anu.
14Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye,
ndi zomera kuti munthu azilima
ndi kupeza chakudya m'nthaka.
15Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake,
mafuta odzola kuti thupi lake lisisire,
ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.
16Mitengo ya Chauta amaithirira ndi madzi ambiri,
mikungudza ya ku Lebanoni imene adaibzala.
17Mbalame zimamanga zisa m'menemo,
dokowe amamanga chisa m'mikungudzamo.
18M'mapiri aatali ndimo m'mene mumakhala mbalale,
m'matanthwe ndimo m'mene mumathaŵira mbira.
19Inu mudapanga mwezi kuti uzisiyanitsa nyengo,
ndipo dzuŵa limadziŵa nthaŵi yake yoloŵera.
20Mumapanga mdima nukhala usiku,
ndipo nyama zam'nkhalango zimatuluka.
21Misona ya mikango imabangula pofunafuna nyama,
kupempha chakudya kwa Mulungu.
22Dzuŵa likamatuluka,
imabwerera nkukagona m'mapanga mwake.
23Munthu amapita ku ntchito yake,
amakagwira ntchito mpaka madzulo.
24Inu Chauta ntchito zanu nzambiri,
zonse mwazipanga mwanzeru,
ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
25Kuli nyanja yaikulu ndi yotambalala,
yodzaza ndi zinthu zosaŵerengeka,
zinthu zamoyo, zazing'ono ndi zazikulu zomwe.
26 Yob. 41.1; Mas. 74.14; Yes. 27.1 Zombo zimayendamo pamodzi ndi Leviyatani,
chilombo chija chimene mudachilenga
kuti chiziseŵera m'madzimo.
27Zonse zolengedwa zimayang'anira kwa Inu,
kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake.
28Mukazipatsa zimachilandira;
mukafumbatula dzanja lanu, zimakhuta.
29Mukazibisira nkhope yanu,
zimachita mantha ndi kutaya mtima.
Mukazichotsera mpweya,
zimafa nkubwerera ku fumbi.
30Mukatumiza mpweya wanu zimalengedwa,
ndipo mumakonzanso maonekedwe a dziko lapansi.
31Ulemerero wa Chauta ukhalebe mpaka muyaya,
Chauta akondwe nazo ntchito zakezo,
32Iye amati akayang'ana dziko lapansi, limanjenjemera,
akakhudza mapiri, mapiriwo amafuka nthunzi.
33Ndidzaimbira Chauta moyo wanga wonse.
Ndidzaimba nyimbo zotamanda Chauta,
nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
34Mapemphero anga amkomere Chauta,
popeza kuti ndimakondwa mwa Iye.
35Anthu ochimwa aonongeke pa dziko lapansi,
anthu oipa asakhaleponso.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga.
Tamanda Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.