1Koma pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, wansembe Yehoyada adalimba mtima, naitana anthu aŵa, amene anali atsogoleri a anthu mazana: Azariya, mwana wa Yerohamu, Ismaele mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseiya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri.
2Iwoŵa adayendera dziko la Yuda, nasonkhanitsa Alevi onse a ku mizinda yonse ya ku Yuda ndi atsogoleri a mabanja a Aisraele, nabwera onse ku Yerusalemu.
32Sam. 7.12 Msonkhano wonsewo udachita chipangano ndi mfumu m'Nyumba ya Mulungu. Yehoyada adaŵauza anthuwo kuti, “Nayu mwana wa mfumu. Iyeyu akhale mfumu monga Chauta adanenera za ana a Davide.
4Zimene mudzachite ndi izi: mwa inu ansembe ndi Alevi amene mukudzatumikira pa sabata, mugaŵikane patatu: gulu limodzi lidzalonde pa makomo.
5Gulu lachiŵiri lidzalonde ku nyumba ya mfumu, gulu lachitatu lidzalonde pa khomo lakuchipata. Ndipo anthu onse adzakhale m'mabwalo a Nyumba ya Chauta.
6Musalole aliyense kuti aloŵe m'Nyumba ya Chauta, koma ansembe ndi Alevi okha amene amatumikira. Iwo angathe kuloŵa poti ngoyeretsedwa. Anthu onse azimvera lamulo la Chauta.
7Alevi akhale moizungulira mfumu, aliyense atatenga zida m'manja. Wina aliyense amene ati aloŵe m'Nyumbamo aphedwe. Muzikhala nayo mfumu kulikonse kumene iziyenda.”
8Alevi ndi anthu onse a ku Yuda adachitadi zonse monga m'mene wansembe Yehoyada adaŵalamulira. Aliyense adabwera ndi anthu ake amene ankadzayamba ntchito yao yotumikira pa sabata, pamodzinso ndi anthu amene ankasiya ntchito yao yotumikira pa sabata. Pakuti wansembe Yehoyada sadaŵaloleze kuchokapo.
9Tsono Yehoyadayo adapatsa atsogoleri aja mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazing'ono, zimene zidaali za mfumu Davide. Zimenezi zinkasungidwa mu Nyumba ya Chauta.
10Adandanditsa anthu onsewo kuti aziteteza mfumu, aliyense ali ndi mkondo m'manja, kuyambira kumwera kwa Nyumbayo mpaka kumpoto kwake, pafupi ndi guwa mpaka pa khomo la Nyumba kuti azizungulira mfumu.
11Kenaka adaŵatulutsira mwana wa mfumu, namuveka chisoti chaufumu, nkumupatsa buku la malamulo, ndipo adamlonga ufumu. Tsono Yehoyada pamodzi ndi ana ake adamdzoza, anthu nafuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali.”
12Tsono Ataliya atamva phokoso la anthu othamangira komweko akutamanda mfumu, adapita ku Nyumba ya Chauta kukaŵapeza anthuwo.
13Atayang'ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake pa khomo, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse am'deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Anthu oimba nyimbo ali ndi zipangizo zao zoimbira, ndiwo amene ankatsogolera chikondwererocho. Pamenepo Ataliyayo adang'amba zovala zake ndipo mofuula adati, “Akundiwukira! Akundiwukira!”
14Tsono wansembe Yehoyada adabwera nawo atsogoleri a gulu lankhondo aja naŵauza kuti, “Mtulutseni ameneyu pakati pa mizere mwandandayo. Ndipo aliyense amene amtsate, mumuphe ndi lupanga.” Wansembeyo adaanenadi kuti, “Musamphere m'Nyumba ya Chauta ai.”
15Choncho anthuwo adamgwira Ataliya uja, ndipo atafika naye ku nyumba ya mfumu, pa khomo lotchedwa la Akavalo, adamuphera pamenepo.
Wansembe Yehoyada achita chipangano ndi anthu(2 Maf. 11.17-20)16Tsono Yehoyada adachititsa chipangano pakati pa iye mwini, ndi anthu onse ndi mfumunso, kuti iwowo akhale anthu akeake a Chauta.
17Choncho anthu onsewo adapita ku nyumba ya Baala, nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenaka anthuwo adaphanso Matani, wansembe wa Baala, patsogolo pa maguwawo pomwepo.
18Tsono Yehoyada adaika ansembe a fuko la Levi kuti azilonda Nyumba ya Chauta. Paja Aleviwo Davide adaaŵaika kuti aziyang'anira Nyumba ya Chauta, ndi kumapereka nsembe zopsereza kwa Chauta, monga zidalembedwa m'malamulo a Mose kuti azipereka akukondwa ndipo akumaimba, potsata lamulo la Davide.
19Iyeyo adaika alonda pa makomo a Nyumba ya Chauta, kuti wina aliyense woipitsidwa pa zachipembedzo asaloŵe.
20Pambuyo pake adandanditsa atsogoleri, nduna, akazembe a anthu ndi anthu onse am'dzikomo. Onsewo adaperekeza mfumu kuchokera ku Nyumba ya Chauta, nakalowa m'nyumba ya mfumu podzera pa khomo lake lapamwamba; ndipo kumeneko adaikhazika mfumuyo pa mpando waufumu.
21Motero anthu onse am'dzikomo adakondwa. Ndipo mumzindamo mudakhala bata, Ataliya ataphedwa ndi lupanga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.