Yes. 60 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ulemerero wa Yerusalemu watsopano

1Iwe Yerusalemu dzuka, ŵala,

kuŵala kwako kwayamba.

Ulemerero wa Chauta wakuŵalira.

2Mdima udzaphimba dziko lapansi,

mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina.

Koma iwe, Chauta adzakuŵalira,

ulemerero wake udzaoneka pa iwe.

3Anthu a mitundu ina adzatsata kuŵala kwako,

mafumu adzalondola kunyezimira kwako

konga dzuŵa limene likutuluka kumene.

4 Bar. 5.5, 6 Yang'ana pozungulira, uwone zimene zikuchitika.

Onse akusonkhana kuti abwere kwa iwe.

Ana ako aamuna adzabwera kuchokera kutali.

Ana ako aakazi adzatengedwa m'manja ngati ana.

5Udzaona zimenezi, ndipo udzakondwa,

mtima wako udzalumpha ndi chimwemwe.

Chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe.

Chuma cha maiko onse chidzabwera kwa iwe.

6Kudzafika mtindiri wa ngamira,

ngamira zing'onozing'ono,

kuchokera ku Midiyani ndi ku Efa.

Onse a ku Sheba adzabwera.

Adzakhala atatenga golide ndi lubani,

ndipo adzatamanda Chauta mokweza mau.

7Ziŵeto zonse za ku Kedara

adzazisonkhanitsa kwanu,

nkhosa zamphongo za ku Nabayoti

zidzakuthandizani pamene mudzazisoŵa.

Zidzaperekedwadi pa guwa ngati nsembe.

Choncho Ine Chauta ndidzapatsa

Nyumba yanga ulemerero waukulu kupambana kale.

8Kodi nzinthu zanji

zikuti yakaliyakali ngati mitambozi,

zikuchita ngati nkhunda zobwerera kumakomo kwakezi?

9Zimenezo ndi zombo zochokera ku maiko akutali,

za ku Tarisisi zili patsogolo.

Zikudzatula ana anu amene atenga siliva ndi golide,

kuti alemekeze dzina la Chauta,

Mulungu wanu, Woyera uja wa Israele,

chifukwa Iyeyo adakupatsani ulemerero.

10Chauta akuuza Yerusalemu kuti,

“Alendo adzamanganso malinga ako,

ndipo mafumu ao adzakutumikira.

Ndidakulanga pamene ndinali wokwiya,

koma tsopano ndidzakukomera mtima

ndi kukuchitira chifundo.

11 Chiv. 21.25, 26 Zipata zako zidzakhala zotsekula nthaŵi zonse.

Usana ndi usiku womwe sadzazitseka,

kuti choncho anthu a mitundu yonse

adzabwere ndi chuma chao kwa iwe,

akuyenda pa mdipiti,

mafumu ao ali patsogolo.

12Koma maiko ndi mafumu amene sakutumikira,

adzaonongekeratu.

Anthu a mitundu imeneyo adzaonongeka kotheratu.”

13“Mitundu itatu ija ya mitengo ya paini,

imene ili yabwino kwambiri m'nkhalango ya ku Lebanoni,

adzabwera nayo kuti akongoletsere Nyumba yanga.

Motero m'Nyumba m'mene ndimakhala Ine mudzalemekezeka.

14 Chiv. 3.9 Ana a amene adaakuzunzapo adzabwera

ndipo adzakugwadira kuwonetsa ulemu.

Onse amene adaakunyozapo adzakuŵeramira mpaka pansi.

Adzakutchula kuti Mzinda wa Chauta,

ndiye kuti Ziyoni,

mzinda wa Woyera uja wa Israele.”

15“Ngakhale anthu adakusiya nadana nawe,

osadutsanso mwa iwe,

ndidzakukuza mpaka muyaya,

ndipo udzakhala malo a chimwemwe

pa mibadwo ndi mibadwo.

16Monga mwana woyamwa

udzadya chuma cha anthu a mitundu ina,

ndipo mafumu ao omwe adzakusamala.

Motero udzadziŵa kuti Ine Chauta ndine Mpulumutsi wako,

ndipo kuti ndine Momboli wako, Wamphamvu uja wa Yakobe.”

17“Ndidzakupatsa golide m'malo mwa mkuŵa,

m'malo mwa chitsulo ndidzakupatsa siliva,

mkuŵa m'malo mwa mtengo,

chitsulo m'malo mwa mwala.

Okuyang'anira ndidzaŵasandutsa amtendere,

okulamulira ndidzaŵasandutsa olungama.

18Ziwawa sizidzamvekanso.

Dziko lako silidzaonongekanso.

Ndidzakhala ngati linga lokuteteza,

ndipo udzanditamanda chifukwa chokupulumutsa.”

19 Chiv. 21.23; 22.5 “Sipadzafikanso dzuŵa loti likuŵalire masana,

kapena mwezi wokuŵalira usiku.

Koma Ine Chauta ndiye ndidzakuŵalire mpaka muyaya.

Ine Mulungu wako ndiye ndidzakhale ulemerero wako.

20Chokuunikira ngati dzuŵa sichidzaloŵanso,

ndipo chokuunikira ngati mwezi sichidzazimiriranso,

chifukwa ndi Chauta amene adzakhala kuŵala kwako

mpaka muyaya. Choncho masiku ako olira adzatha.

21Anthu ako onse adzayenda m'njira zoyenera,

ndipo dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya.

Anthuwo ndidaŵaika ndine,

ndidaŵalenga ndine,

kuti aonetse ulemerero wanga kwa onse.

22Ngakhale kabanja kakang'onong'ono kadzasanduka fuko,

ndipo kafuko kakang'onong'ono

kadzasanduka mtundu wamphamvu.

Ndidzachita zimenezi mofulumira nthaŵi yake itafika.

Ine ndine Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help