Yud. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Akiyore mfumu ya Aamoni

1Ena adadziŵitsa Holofernesi, mtsogoleri wamkulu wa gulu lankhondo la Aasiriya, kuti Aisraele akonzekera kumenyana naye nkhondo ndipo kuti atseka mipata ya pakati pa mapiri, amanga malinga pa magomo, ndi kukumba machemba m'zigwa.

2Pamenepo Holofernesi adapsa mtima kwambiri. Adaitana akuluakulu onse a Amowabu ndi a Aamoni ndi abwanamkubwa onse a m'mbali mwa nyanja.

3Adaŵafunsa kuti, “Tandiwuzani inu Akanani, kodi anthu amene ali pa mapiriŵa ndi ayani? Akhala m'mizinda iti? Gulu lao lankhondo nlalikulu chotani? Kodi mphamvu kapena nyonga zao zagona pati? Nanga mfumu yotsogolera ankhondo ao ndani?

4Chifukwa chiyani iwo okhawo sadadzatilonjere monga adachitira anthu onse okhala ku maiko akuzambwe?”

5Tsono Akiyore, mfumu ya Aamoni, adayankha kuti, “Pepani, Mbuye wanga, mundimvere, ndikuuzeni zoona za anthu okhala m'dera lamapiri pafupi ndi kwathu kuno. Sindilankhula zonama.

6Anthuwo ndi zidzukulu za Ababiloni.

7Poyamba adaakakhala ku Mesopotamiya, chifukwa ankakana kutsata milungu ya makolo ao amene anali ku Kalidea.

8Adaasiya miyambo ya makolo ao nkuyamba kupembedza Mulungu wakumwamba yekha, amene ankamudziŵa. Ababiloni ataŵapirikitsa pamaso pa milungu yao, iwowo adathaŵira ku Mesopotamiya kumene adakhalako nthaŵi yaitali.

9Gen. 11.31—12.5Pambuyo pake Mulungu wao uja adaŵalamula kuti achoke kumeneko, apite ku Kanani. Motero adakhazikika kumeneko, napeza chuma chambiri monga golide, siliva ndi ziŵeto.

10 Gen. 42.1-5; Eks. 1.7 “Kenaka adapita ku Ejipito chifukwa cha njala imene idaafalikira ku Kanani konse. Adakhala kumeneko nthaŵi yaitali chifukwa ankapezako chakudya. Adachulukana kwambiri ku Ejipitoko kotero kuti kunali kosatheka kuŵaŵerenga.

11Eks. 1.8-14Pamenepo mfumu ya ku Ejipito idayamba kudana nawo. Idaŵapezera nkuyamba kuŵagwiritsa ntchito yakalavulagaga youmba njerwa, niŵasandutsa akapolo.

12Eks. 7.1—12.46Tsono iwo adalira kwa Mulungu wao, ndipo Mulunguyu adazunza Aejipito kwambiri ndi nthenda zosachizika. Motero Aejipitowo adaŵapirikitsira kutali.

13Eks. 14.21, 22Mulungu waoyo adaŵaumitsira Nyanja Yofiira.

14Adaŵaperekeza poŵadzeretsa ku Sinai ndi ku Kadesi-baranea, napirikitsa anthu onse okhala ku chipululu.

15Motero iwowo adakhazikika m'dziko la Aamori, ndipo ndi mphamvu zao adapheratu anthu onse a ku Hesiboni. Pambuyo pake adaoloka Yordani nakalanda dziko lonse lamapiri.

16Adapirikitsa Akanani, Aperezi, Ayebusi, Asekemu ndi Agirigasi onse. Adakhala nthaŵi yaitali kumeneko.

17 Deut. 28.1-68 “Nthaŵi yonse akapanda kuchimwira Mulungu wao, ankapeza bwino, popeza kuti Mulungu waoyo amadana ndi zoipa.

18Koma pamene adaleka kutsata zimene Mulungu wao adaŵalamula, hafu lina la fuko lao lidaferatu pa nkhondo zosiyanasiyana, ndipo hafu lina lidatengedwa ukapolo kupita ku dziko lachilendo. Nyumba ya Mulungu wao idapasulidwa ndipo mizinda yao idagwa m'manja mwa adani ao.

19Popeza kuti tsopano abwerera kwa Mulungu wao, adabwerako kumene adaabalalikira kuja, ndipo adalandanso mzinda wa Yerusalemu m'mene muli Nyumba ya Mulungu wao, nkukhazikikanso m'dziko lamapiri lija, poti munalibe anthu.

20“Tsopano mbuyanga, ngati anthu ameneŵa ali ndi zolakwa, ngati adachimwira Mulungu wao, ife nkutsimikiza kuti achimwadi, tingathe kukamenyana nawo nkhondo mpaka kuŵagonjetsa.

21Koma ngati anthu ameneŵa sadalakwe, ingoŵalekani mbuyanga, chifukwa Mulungu wao adzaŵapulumutsa nkuŵateteza, ifeyo anthu nkudzatiseka pa dziko lonse lapansi.”

Anthu akhumudwa

22Akiyore atatha kulankhula, anthu onse amene adazungulira hema, adayamba kuŵiringula. Akuluakulu ankhondo a Holofernesi, pamodzi ndi anthu onse a m'mbali mwa nyanja ndi a ku Mowabu, adaumirira kuti iyeyo aphedwe.

23Anthu adati, “Ife sitingaŵaope Aisraele. Amene aja ndi anthu opanda mphamvu, alibe nyonga zomenyera nkhondo kolimba.

24Mbuyathu Holofernesi, tiyeni tinyamuke, gulu lanu lankhondo lino lidzaŵatheratu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help