1Solomoni mwana wa Davide adakhazikika molimbika mu ufumu wake, ndipo Chauta, Mulungu wake, anali naye, namkweza kwambiri.
2Solomoni adalankhula ndi Aisraele onse, atsogoleri a anthu zikwi ndiponso atsogoleri a anthu mazana, aweruzi, atsogoleri a Aisraele onse, ndiponso akulu a mabanja.
3Solomoni pamodzi ndi anthu onse amene adasonkhana nawo, adapita ku kachisi wa ku Gibiyoni. Paja chihema chamsonkhano cha Mulungu chimene Mose, mtumiki wa Chauta, adaamanga ku chipululu chinali kumeneko.
42Sam. 6.1-17; 1Mbi. 13.5-14; 15.25—16.1(Davide anali atabwera nalo bokosi lachipangano la Chauta kuchokera ku Kiriyati-Yearimu, ndi kulikhazika ku malo amene iye adaakonza, poti adaalimangira hema ku Yerusalemu.)
5Eks. 38.1-7 Kuwonjezera pamenepo, guwa lamkuŵa limene adaapanga Bazalele mwana wa Uri, mwana wa Huri, linali komweko kumaso kwa chihema cha Chauta. Ndipo Solomoni adakapembedza kumeneko pamodzi ndi msonkhano wonse.
6Solomoni adakwera komweko ku guwa lamkuŵa lopembedzerapo Chauta, limene linali ku chihema chamsonkhano, naperekapo nsembe zopsereza zokwanira 1,000.
7Usiku umenewo Mulungu adamuwonekera Solomoni namuuza kuti, “Upemphe chilichonse chimene ufuna kuti ndikupatse.”
8Solomoni adati, “Inu Mulungu, mudaonetsa chikondi chanu chachikulu ndi chosasinthika kwa bambo wanga Davide, ndipo tsono mwandiika ine kuti ndikhale mfumu m'malo mwake.
9Gen. 13.16; 28.14 Inu Chauta, zimene mudalonjeza kwa bambo wanga Davide zichitikedi, pakuti mwandiika kuti ndikhale mfumu yolamulira anthu ochuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi.
10Tsono mundipatse nzeru ndi luntha, kuti ndiŵatsogolere bwino anthu anuŵa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu wa anthu anu?”
11Mulungu adamuyankha kuti, “Chifukwa chakuti waganiza zimenezi mumtima mwako, ndipo sudapemphe katundu, chuma, ulemu, kapena imfa ya adani ako, sudadzipempherenso moyo wautali, koma wapempha nzeru ndi luntha, kuti uzilamulira anthu anga amene ndakulongera ufumu, chabwino
12nzeruzo ndi luntha ndikupatsa. Ndidzakupatsanso chuma, katundu ndi ulemu, zinthu zoti panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali nazo mwa mafumu amene analipo iwe usanabadwe, ndipo sipadzaonekanso wokhala nazo iweyo utafa.”
Chuma ndi mphamvu za Mfumu Solomoni(1 Maf. 10.26-29)13Motero Solomoni adachoka ku kachisi wa ku Gibiyoni pafupi ndi chihema chamsonkhano, nabwera ku Yerusalemu. Ndipo adalamulira Aisraele onse.
14 1Maf. 4.26 Adasonkhanitsa magaleta ndiponso anthu okwera pa akavalo. Magaletawo anali nawo 1,400, anthu okwera pa akavalo analipo 12,000. Adaŵakhazika ena ku mizinda yokhalako ankhondo ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu.
15Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva ndi golide kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.
16Deut. 17.16 Solomoni ankagula akavalo ku Ejipito ndi ku Kuwe. Anthu amalonda a mfumu ankalandira akavalowo ku Kuwe, atapereka ndalama.
17Anthuwo ankagula galeta ku Ejipito pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Momwemonso mafumu onse a Ahiti ndi a ku Siriya nawonso ankagula zinthu kudzera mwa anthu amalonda omwewo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.