1 Pet. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za akazi ndi amuna apabanja

1 Aef. 5.22; Akol. 3.18 Chimodzimodzinso inu azimai, muzimvera amuna anu, kuti ngati ena mwa iwo samvera mau a Mulungu, azikopeka ndi makhalidwe a akazi aonu. Sipadzafunikanso kunenerera mau,

2popeza kuti adzadziwonera okha makhalidwe anu aulemu ndi angwiro.

31Tim. 2.9Kudzikongoletsa kwanu kusangokhala kwa maonekedwe akunja pakuluka tsitsi, ndi kuvala zamakaka zagolide ndi zovala zamtengowapatali.

4Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.

5Umu ndi m'mene kale lija azimai oyera mtima okhulupirira Mulungu ankadzikongoletsera, ndipo ankamvera amuna ao.

6Gen. 18.12Sara yemwe ankamvera Abrahamu, ndi kumutcha “Mbuyanga.” Motero inu azimai, ndinu ana ake a Sarayo, ngati muchita bwino, osalola kuwopsedwa ndi kanthu kalikonse.

7 Aef. 5.25; Akol. 3.19 Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.

Kumva zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo

8Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.

9Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.

10Mas. 34.12-16 Paja mau a Mulungu akuti.

“Yemwe afuna kukondwera ndi moyo,

ndi kuwona masiku abwino,

aletse lilime lake kulankhula zoipa,

ndiponso milomo yake kunena mabodza.

11Alewe zoipa, azichita zabwino.

Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuupeza.

12Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama

amatchera khutu ku mapemphero ao.

Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”

13Ndani angakuchiteni choipa ngati muchita changu pa zabwino?

14Mt. 5.10

Yes. 8.12, 13Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima,

15koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

16Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao.

17Nkwabwino kumva zoŵaŵa chifukwa chochita zabwino, ngati Mulungu wafuna choncho, koposa kumva zoŵaŵa chifukwa chochita zoipa.

18Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.

19Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m'ndende.

20Gen. 6.1—7.24 Mizimuyi ndi ya anthu amene kale lija sadamvere pamene Mulungu adaadikira moleza mtima, pa nthaŵi imene Nowa ankapanga chombo. M'chombomo anthu oŵerengeka okha, asanu ndi atatu, adapulumuka ndi madzi.

21Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kumeneku si kuchotsedwa litsiro la m'thupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi mtima woona, kudzera mwa Yesu Khristu

22amene adapita Kumwamba, ndipo ali ku dzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko angelo ndi maulamuliro ndi zimphamvu zimamvera Iye.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help