1Mtima wanga umakhala chete
kuyembekezera Mulungu yekha,
pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
2Iye yekhayo ndiye thanthwe langa,
chipulumutso changa, ndi linga langa.
Sindidzagwedezeka konse.
3Kodi nonsenu mudzaukira munthu mpaka liti,
kuti mumgwetse pansi ngati khoma lopendekeka,
ngati mpanda wogwedezeka?
4Cholinga chao nchongofuna kumtsitsa
pa malo ake aulemu.
Amakonda kulankhula zonama.
Amadalitsa ndi pakamwa pao,
koma mumtima mwao amatemberera.
5Mtima wanga umakhala chete
kuyembekezera Mulungu yekha,
pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye.
6Iye yekhayo ndiye thanthwe langa
ndi chipulumutso changa,
ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
7Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga,
zonsezo zili kwa Mulungu.
Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu,
ndiye kothaŵira kwanga.
8Anthu inu, ikani mtima wanu pa Iye nthaŵi zonse.
Muuzeni zonse za kukhosi kwanu.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu.
9Anthu otsika ndi mpweya chabe,
ngakhale anthu okwera ndi nthunzi chabe,
onsewo ndi oluluka pa sikelo,
ndi opepuka kupambana mpweya.
10Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni.
Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni.
Chuma chikachuluka musaikepo mtima.
11Mulungu adalankhula kamodzi,
ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri,
china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,
12 Yob. 34.11; Yer. 17.10; Mt. 16.27; Aro. 2.6; Chiv. 2.23 chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye;
china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu
molingana ndi ntchito zake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.