Ezek. 44 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ntchito ya chipata chakuvuma

1Munthu uja adapita nane ku chipata cha kunja kwa malo opatulika choyang'ana kuvuma. Chinali chotseka.

2Tsono adandiwuza kuti, “Chipata ichi chikhale chotseka, osachitsekula. Wina asaloŵerepo ai, poti Ambuye, Mulungu wa Israele, waloŵerapo. Nchifukwa chake chizikhala chotseka.

3Kalonga yekha angathe kukhala pamenepo ndi kumadya chakudya pamaso pa Chauta. Adzaloŵa ndi kutuluka kudzera m'khonde lam'kati la chipata chimenecho.”

Malamulo oloŵera m'Nyumba ya Mulungu

4Pambuyo pake munthuyo adandidzeretsa pa chipata chakumpoto ndipo tidafika kumaso kwa Nyumba ya Mulungu. Kumeneko ndidaona ulemerero wa Chauta utadzaza Nyumba yakeyo. Pamenepo ndidadzigwetsa chafufumimba.

5Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, samala bwino, uyang'anitsitse ndipo umvetse bwino zonse zimene ndikuuze za malamulo ndi malangizo okhudza za Nyumba yangayi. Uzindikire bwino amene angaloledwe kuloŵa m'Nyumba ino ndiponso amene sayenera kuloŵamo.

6Anthu a mtundu waupandu wa Israele uŵauze mau anga akuti, Aisraele inu, lekani zonyansa zanu zonse.

7Mudaloŵetsa m'malo anga opatulika alendo osaumbalidwa mu mtima ndi m'thupi momwe. Anthuwo adaipitsa Nyumba yanga pamene inu munkandipatsa chakudya, mafuta ndi magazi omwe. Pochita zoipa zoterezi mudaphwanya chipangano changa.

8M'malo moti muzisamala ndinu zinthu zanga zopatulika, mwasankha alendoŵa kuti aziyang'anira malo anga opatulika.

9“Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Mwa alendo amene ali osaumbalidwa mu mtima ndi m'thupi, pasapezeke ndi mmodzi yemwe woloŵa m'malo anga opatulika, ngakhalenso alendo amene amakhala pakati pa Aisraele.

Alevi achotsedwa pa Unsembe

10“Tsono Alevi amene adaandisiya kutali pa nthaŵi imene Aisraele adaasokera potsata mafano, adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwao.

11Adzangokhala atumiki chabe ku malo anga opatulika. Adzayang'anira zipata za Nyumba ya Mulungu ndi kugwira ntchito zina zake kumeneko. Adzapha nyama za nsembe zopsereza, ndi za nsembe zina za anthu. Motero adzidzaimirira anthuwo ndi kumaŵatumikira.

12Iwowo ankatumikira anthu popembedza mafano, ndipo adasokeretsa Aisraele potero. Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikulumbira ndithu kuti ameneŵa ayenera kulangidwa chifukwa cha zolakwa zao.

13Saloledwa kudzafika pafupi ndi Ine, kuti anditumikire ngati ansembe. Sadzayandikira zinthu zanga zopatulika ndi zopereka zoyera kwambiri. Adzachititsidwa manyazi chifukwa cha ntchito zao zonyansa.

14Komabe ndidzaŵaika kuti aziyang'anira Nyumba yanga ndi kutumikira pa ntchito zonse zoyenera kuchitika kumeneko.

Za ansembe

15“Koma ansembe a fuko la Levi a m'banja la Zadoki, amene adakhalabe okhulupirika pa ntchito zosamala malo anga opatulika nthaŵi imene Aisraele adaasokera ndi kundisiya Ine, okhawo adzasendera kwa Ine kuti anditumikire. Adzabwera kwa Ine kudzapereka nsembe za mafuta ndi magazi. Ndatero Ine Ambuye Chauta.

16Iwo okhawo ndiwo adzaloŵe ku malo anga opatulika ndi kudzayandikira tebulo langa kuti anditumikire. Ndiwo amene adzasamalire zinthu zanga.

17Eks. 28.39-43; Lev. 16.4 Pamene aloŵa ku chipata cham'kati, azivala bafuta. Asavale chovala chilichonse cha ubweya wankhosa ponditumikira pa zipata za bwalo lam'kati ndiponso m'kati mwa Nyumba yanga.

18Azivala nduŵira zabafuta kumutu, ndi akabudula abafuta. Asavale chilichonse choŵachititsa thukuta.

19Lev. 16.23 Potulukira ku anthu a ku bwalo lakunja, azivula zovala zimene anavala potumikira m'kati, ndi kuzisiya m'zipinda zopatulika. Ndipo avale zovala zina, kuwopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo ndi zovala zaozo.

20 Lev. 21.5 “Ansembewo asamete mpala kapena kuŵeta tsitsi lalitali kwambiri, koma azingoliyepula.

21Lev. 10.9 Wansembe asamwe vinyo pamene ali pafupi kuloŵa m'bwalo lam'kati.

22Lev. 21.7, 13, 14 Asakwatire mkazi wamasiye wamba kapena mkazi wosudzulidwa. Azikwatira namwali wosadziŵa mwamuna, ŵa fuko la Israele, kapena mkazi wamasiye wa wansembe mnzake.

23 Lev. 10.10 “Ansembe aziphunzitsa anthu anga kusiyanitsa pakati pa zinthu zoyera ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zoyenera ndi zosayenera kuperekera nsembe.

24Pakakhala milandu, ansembe adzakhala oweruza, ndipo adzayenera kugamula milanduyo potsata malamulo anga. Atsate malamulo anga ndi malangizo anga pa za masiku anga onse achikondwerero. Adzasamalenso kuti masiku anga a Sabata akhale oyera.

25 Lev. 21.1-4 “Wansembe asadziipitse pokhudza munthu wakufa, kupatula ngati ndi bambo wake kapena mai wake, mwana wake wamwamuna kapena wamkazi, mbale wake kapena mlongo wake wosakwatiwa.

26Ngati aipitsidwa kenaka nkuyeretsedwa, adikire masiku asanu ndi aŵiri, kuti akhale woyeretsedwa kotheratu.

27Tsono pa tsiku loti aloŵe m'bwalo lam'kati kuti akatumikire m'malo opatulika, apereke nsembe yopepesera machimo. Ndatero Ine Ambuye Chauta.

28 Num. 18.20 “Ansembe asadzakhale ndi choloŵa chilichonse ai. Choloŵa chao ndine. Ndipo musadzaŵapatse chuma mu Israele. Chuma chao ndine.

29Num. 18.8-19 Iwo azidzadyako za chopereka cha zakudya, za nsembe zopepesera machimo, ndi za nsembe zopepesera kupalamula. Ndipo zonse zoperekedwa kwa Mulungu mu Israele zidzakhala zao.

30Zopambana pa zonse zoyambirira kucha ndi pa zopereka zina zonse, zidzakhale za ansembe. Muzidzaŵapatsa ufa wanu umene mwayambirira kusinja, kuti choncho m'nyumba mwanu mukhale madalitso.

31Lev. 22.8 Kaya ndi mbalame kaya ndi nyama, ansembe asadye yofa yokha kapena yochita kujiwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help