1M'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani kuti likhale lanulanu mwina mwake mungathe kupeza munthu wakufa m'munda, inu osadziŵa amene wamupha.
2Akuluakulu anu ndi aweruzi anu apiteko, ndipo akayese kutalika kwake kuchokera pamalo pamene pali munthu wakufayo mpaka ku mizinda yoyandikana ndi malowo.
3Pamenepo akuluakulu a mudzi woyandikana kwambiri ndi pamene pali mtembopo, asankhe ng'ombe imene sidagwirepo ntchito, ndipo sidakokepo galeta.
4Ng'ombeyo apite nayo kudambo kumene kuli madzi oyenda. Malowo akhale akuti munthu sadalimepo nkale lonse kapena kubzalapo kanthu. Kumeneko akaithyole khosi ng'ombeyo.
5Ansembe Achilevi apitekonso kumeneko, chifukwa ndiwo amene ayenera kumaweruza milandu yonse ya ndeu ndi ya kupha. Chauta, Mulungu wanu, wasankha iwowo kuti akhale atumiki ake, ndiponso kuti azidalitsa m'dzina lake.
6Tsono atsogoleri onse ochokera ku mudzi wa pafupi ndi pamene panali munthu wophedwayo, asambe m'manja pamwamba pa ng'ombe ija imene adaithyola khosi m'dambo muja.
7Ndipo anene kuti, “Sindife tidamupha munthuyu, ndipo amene adamupha sitidamuwone.
8Inu Chauta, khululukirani anthu anu Aisraele amene mudaŵaombola. Tikhululukireni ndipo musaike pa ife tchimo la kupha munthu wosalakwayu.”
9Mukachita zimene Chauta afuna, Iyeyo sadzakuzengani mlandu woti mwapha munthu wosalakwa.
Za akazi ogwidwa ku nkhondo10Chauta, Mulungu wanu, akakupambanitsani pa nkhondo, mungathe kugwirapo akapolo kunkhondoko.
11Mwina pakati pa akapolowo inu nkuwona mkazi wokongola amene mwamkonda, ndipo mufuna kumkwatira.
12Pita nayeni kwanu, ndipo mkaziyo amete kumutu, ndi kutseteka makadabo ake,
13ndipo asinthe zovala. Akhale m'mudzi mwanu mwezi wathunthu, ndipo alire maliro kulira makolo ake. Tsono atatha zimenezi, mumkwatire.
14Pambuyo pake mutaona kuti simukumfunanso, mumleke, apite mwaufulu kumene akufuna. Simungathe kumuyesanso kapolo kapena kumgulitsa, chifukwa mudakhala naye malo amodzi.
Choloŵa cha mwana wachisamba15Tiyese kuti munthu ali ndi akazi aŵiri, wina wokondedwa kwambiri wina pang'ono, onsewo nkubala ana aamuna, mwana woyamba kubadwa nakhala wa mkazi amene amamkonda pang'ono.
16Munthuyo akatsimikiza zoti agaŵire ana akewo chuma chake, asakondere mwana wa mkazi wokondedwa koposayo, pakumpatsa gawo la mwana woyamba.
17Mwana wake woyamba kubadwa uja ampatse moŵirikiza, ngakhale kuti ndi mwana amene mai wake ndi wokondedwa pang'ono. Munthu ayenera kuvomera mwana wake woyamba, ndi kumpatsa gawo limene lili lake potsata lamulo.
Za mwana wosamvera18Tiyese kuti wina ali ndi mwana wokanika ndiponso wachipongwe, mwana woti bambo ndi mai ake saŵamvera konse, ngakhale amlange chotani.
19Makolo ake a mwanayo amgwire ndi kupita naye kwa akuluakulu amumzinda ku chipata cha mzindawo.
20Makolowo auze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu ndi wokanika ndipo ndi wachipongwe safuna kutimvera, ndi wadyera ndiponso chidakwa.
21Pamenepo anthu amumzindawo amuphe pakumponya miyala, motero mudzachotsa choipa pakati panu. Anthu onse a mu Israele muno akadzamva zimene zachitikazi, adzakhala ndi mantha.”
Za malamulo osiyanasiyana22Munthu akaphedwa chifukwa cha mlandu, ndipo mtembo wake ndi wopachikidwa pa mtengo,
23Aga. 3.13 mtembowo usagonere pamtengopo. Uikidwe tsiku lomwelo, chifukwa kuti mtembo ugonerere pamtengo ndi chinthu chobweretsa matemberero a Mulungu. Kwirirani mtembowo, kuwopa kuti mungaipitse dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.