1Makabeo ndi anzake adalandanso Nyumba ya Mulungu ndi mzinda wa Yerusalemu, Ambuye akuŵatsogolera.
2Adagumula maguwa amene alendo adaamanga pa bwalo la mzinda; adaononganso malo ao ena achipembedzo.
3Atayeretsa Nyumba ya Mulungu, adamanga guwa lina lansembe. Tsono adayatsa moto popekesa mwala, naperekanso nsembe, chinthu chimene sichidachitike pa zaka ziŵiri. Kenaka adafukiza lubani, nayatsa nyale nkuikanso mitanda ya buledi pamaso pa Ambuye.
4Atatero, adadzigwetsa chafufumimba, napempha Ambuye kuti asaŵagwetserenso mazunzo otereŵa, koma akadzachimwanso adzaŵalange mwachifundo, osaŵaperekanso kwa mitundu ina ya anthu onyoza Mulungu ndi ankhalwe.
5Tsiku limene adayeretsanso Nyumba ya Mulungu linali tsiku lomwe alendo aja adaaiipitsa, linali tsiku la 25 la mwezi wa Kisilevi.
6Onse adakondwa nachita chikondwerero pa masiku 8, monga pa chikondwerero chamahema. Nthaŵi imeneyo ankakumbukira kuti si kale kwambiri, pa masiku a chikondwerero chamahema omwewo, ankagona pa mapiri ndi m'mapanga ngati nyama zakuthengo.
7Koma tsopano ndodo za makaka amaluŵa, nthambi za mitengo yokongola ndiponso za kanjedza zili m'manja, ankaimba nyimbo zotamanda Mulungu amene adaŵathandiza kuyeretsa bwino Nyumba yake.
8Pambuyo pake adapanga lamulo lodziŵika kwa onse, la kuti Ayuda onse azidzakumbukira masiku ameneŵa chaka chilichonse.
Ptolemeyo Makroni adzipha9Zimenezi ndiye zomwe zidachitika pa kufa kwa Antioko, wotchedwa Epifane.
10 1Am. 6.17 Tsopano tisimbe za Antioko Eupatore, mwana wake wa sapemphera uja, ndipo tinene mwachidule zoipa zotsatira nkhondo zake.
11Iyeyo ataloŵa ufumu adaika Lisiyasi kuti akhale woyang'anira ntchito za boma, ndiponso kuti akhale bwanamkubwa wa ku Celesiriya ndi Fenisiya.
12Ptolemeyo Makroni ndiye adayamba kuchitira Ayuda zolungama pokumbukira zonse zosalungama zimene adaazipirira; ndipo adayesetsa kuŵaweruza mwamtendere.
13Nchifukwa chake abwenzi ena a mfumu adakamneneza kwa Eupatore. Tsono Makroni ankamva anthu akunena kaŵirikaŵiri kuti iyeyo anali wopereka dziko lake kwa adani, poti adaasiya Kipro, mzinda umene Filometore adaamsungiza, kukagwirizana ndi Antioko Epifane. Poona kuti sankathanso kudzisungira ulemu woyenera udindo wake, adadzipha pakumwa zumu.
Yudasi Makabeo agonjetsa Aidume14Pamene Gorjiyasi adasanduka bwanamkubwa wa dziko la Idumeya, anali ndi gulu la asilikali aganyu, ndipo kaŵirikaŵiri ankamenyana nkhondo ndi Ayuda.
15Komanso Aidume ena amene ankakhala m'nyumba zankhondo zamphamvu, sankalekanso kumenyana ndi Ayuda. Ankalandira bwino anthu ochotsedwa kwao ku Yerusalemu, ndipo ankayesayesa ndithu kupitiriza nkhondo.
16Koma Makabeo ndi anthu ake, atapemba mwaulemu ndi kupempha kuti Mulungu aŵathandize, adathamangira ku nyumba zankhondo za Aidumezo.
17Adaŵathira nkhondo mwamphamvu, ndipo adagonjetsa amene ankamenya nkhondo pa malinga, nalanda nyumba zankhondozo. Adapha onse amene adaŵapeza, motero adapha anthu osachepera 20,000.
18Koma anthu okwanira 9,000 adathaŵira ku maboma ena aŵiri ankhondo olimba kwambiri, ndipo anali ndi zida zokwanira zoti nkulimbana ndi nkhondo yoŵazinga.
19Makabeo adasiya Simoni, Yosefe ndi Zakeyo kumeneko, pamodzi ndi anthu ao, okwanira kuzinga mabomawo. Iyeyo adapita kwina kumene anali wofunika koposa.
20Koma anthu ena a Simoni anali okonda ndalama, choncho adalandira chiphuphu kwa anthu okhala m'maboma aja. Ndiye atalandira makilogramu 64 a siliva, adaŵalola ena kuti athaŵe.
21Pamene Yudasi adamva zimenezo, adasonkhanitsa akuluakulu a anthu, natulutsa mlandu wakuti anthu aja adagulitsa abale ao ndi ndalama, polola kuti adaniwo athaŵe ndi kudzamenyana nawonso.
22Tsono adaŵapha anthu osakhulupirikawo, kenaka posachedwa nkulanda maboma aŵiri ankhondo aja.
23Nthaŵi zonse Yudasi akamamenya nkhondo, ankapambanadi; choncho adapha anthu opitirira 20,000 m'maboma aŵiriwo.
Yudasi agonjetsa Timoteo24Koma Timoteo, uja Ayuda adaamgonjetsa kaleyu, adasonkhanitsa gulu lalikulu la ankhondo achilendo napita ku Asiya kukatenga anthu ambirimbiri okwera pa akavalo. Adafika kuti adzakanthe Ayuda ndi kuŵagonjetsa.
25Iyeyo akuyandikira, anthu a Makabeo adayamba kupemphera kwa Mulungu, adadzithira phulusa kumutu, nkuvala ziguduli m'chiwuno.
26Adadzigwetsa chafufumimba pa makwerero apaguwa, napemphera kwa Ambuye kuti aŵachitire chifundo, kuti akhale mdani wa adani ao, ndipo kuti athyole adani olimbana nawo, monga momwe adaalonjezera m'Malamulo.
27Atatha kupemphera, adatenga zida zao nayenda mpaka kutali ndi mzinda. Atafika pafupi ndi adani ao, adaima.
28Mbandakucha adayamba kumenyana nkhondo ndi adani aowo. Ena ankakhulupirira kuti adzapambana osati chifukwa cha kulimba mtima kwao kokha, koma makamaka chifukwa cha chithandizo cha Ambuye, pamene enawo ankayesa kuti ukali waowo ndiwo udzaŵapambanitse.
29Nkhondoyo italimba kwambiri, adani a Ayudawo adaona kumwamba anthu asanu oŵala kwambiri, atakwera pa akavalo okhala ndi zitsulo zagolide m'kamwa, akutsogolera Ayuda.
30Anthuwo adaaika Makabeo pakati pao, ndipo ankamtchinjiriza ndi malaya ao achitsulo ndi zida zao kuti angapwetekedwe. Ankaponya mivi ndi ziphaliŵali pa adaniwo. Pamenepo iwo adaniwo adathobwa m'maso nkusokonezeka. Adamwazikana mwachipwirikiti nkukanthidwa kotheratu.
31Oyenda pansi 20,500 adaphedwa pamodzi ndi 600 okwera pa akavalo.
32Timoteo mwiniwake adathaŵira ku mzinda wankhondo wolimba kwambiri wa Gazara, umene Kereasi ankaulamulira.
33Anthu a Makabeo adakondwera poona zimenezi, nazinga mzindawo masiku anai.
34Anthu amumzindamo ankakhulupirira mphamvu za mzinda wao, namangotukwana koopsa ndi kulankhula mau onyoza.
35Koma mbandakucha tsiku lachisanu lake, anyamata makumi aŵiri a gulu la Makabeo, popsa mtima ndi mau oipawo, adalimba mtima nkukwera pamwamba pa malinga. Ndiye mwa ukali wao ankangobaya aliyense wokumana naye.
36Anzao ena adaŵatsatira nkumamenyana ndi adani ku mbali ina. Adatentha nsanja zankhondo, nayatsa miyulu ya nkhuni nkuŵatentha otukwanawo ali amoyo. Ena adathyola zitseko za mzinda, natsekulira njira ankhondo anzao otsala, ndipo adalanda mzindawo.
37Adampeza Timoteo atabisala m'chitsime chouma. Adamupha pamodzi ndi Kereasi mbale wake, ndiponso Apolofane.
38Atatsiriza zonsezi, adaimba nyimbo zothokoza ndi kuyamika Ambuye amene adaŵachitira zabwino Aisraele, naŵapambanitsa motero.
Yudasi agonjetsanso LisiyasiWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.