Yes. 63 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta adzagonjetsa anthu a mitundu ina

1 Yes. 34.5-17; Yer. 49.7-22; Ezek. 25.12-14; 35.1-15; Amo. 1.11, 12; Oba. 1.1-14; Mal. 1.2-5 “Ndaninso kodi akuchokera ku Edomuyu,

atavala zofiira za ku Bozira?

Ndani ameneyu wovala zovala zokongola,

akuyenda monyadira mphamvu zake?

Ndi Ineyo, wolankhula zachilungamo,

ndiponso wa mphamvu zoti nkupulumutsa.”

2Nanga bwanji zovala zanu zili psuu,

ndiponso zikuwoneka ngati za munthu woponda mphesa?

3 Chiv. 14.20; 19.15; Chiv. 19.13 “Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina

ngati mphesa,

ndipo palibe ndi mmodzi yemwe

amene adadzandithandiza.

Ndidaŵapondereza ndili wokwiya,

magazi ao nkufalikira pa zovala zanga.

4Mumtima mwanga ndidatsimikiza kuti

lafika tsiku loti ndilange adani anga molipsira,

chafika chaka choti ndipulumutse anthu anga.

5 Yes. 59.16 Ndidayang'ana, koma panalibe wondithandiza.

Ndidadabwa kwabasi kuti panalibe wondichirikiza.

Choncho ndidapambana ndi mphamvu za ine ndekha,

unkandilimbitsa ndi mkwiyo wanga.

6Ndidapondereza anthu a mitundu ina ndili wokwiya,

ndipo ndidaŵasakaza. Magazi ao ndidaŵathira pansi.”

Chauta achitira Aisraele zabwino

7Ndidzasimba za chikondi chosasinthika cha Chauta.

Ndidzamtamanda chifukwa cha zonse zimene watichitira.

Wadalitsa kwambiri anthu a ku Israele,

potsata chifundo ndi kukula

kwa chikondi chake chosasinthika.

8Chauta adati,

“Iwo ndi anthu anga,

ana anga amene sadzandinyenga.”

Motero adaŵapulumutsa.

9Adavutika poona mavuto ao onse,

Mngelo wochokera kwa Iye adaŵapulumutsa.

Adaŵaombola mwa chikondi ndi chifundo chake.

Wakhala akuŵasamala ngati ana kuyambira kale.

10Komabe iwo adampandukira,

namkwiyitsa Mulungu.

Motero Chauta adasanduka mdani wao,

ndipo adamenyana nawo nkhondo.

11Pamenepo anthuwo adakumbuka zamakedzana,

masiku a Mose mtumiki wake,

ndipo adafunsa kuti,

“Ali kuti tsopano Chautayo

amene adapulumutsa anthu ake

pamodzi ndi mtsogoleri wao pa nyanja?

Ali kuti Chautayo

amene adaika mwa anthu ake mzimu wake woyera?

12 Eks. 14.21 Ali kuti Chautayo

amene adachita zinthu zodabwitsa ndi

mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose?

Adagaŵa madzi am'nyanja, anthu ake akuwona,

kuti dzina lake limveke mpaka muyaya.

13Adaŵayendetsa pa nyanja pouma,

ndipo monga kavalo woyenda m'chipululu,

iwo sadakhumudwe.

14Mzimu wa Chauta udaŵapumitsa,

monga m'mene ng'ombe zimapumulira ku dambo.”

Motero Inu Chauta mudatsogolera anthu anu,

kuti dzina lanu lilemekezeke.

Pemphero lopempha chithandizo

15Inu Chauta kumwambako,

ku malo anu oyera ndi aulemerero,

mutiyang'ane ife.

Kodi chisamaliro chanu chili kuti?

Mphamvu zanu zili kuti?

Simukutiwonetsanso chikondi chanu ndi chifundo chanu.

16Inu ndinu Atate athu ndithu,

ngakhale Abrahamu satidziŵa,

ngakhale Israele sakutivomera.

Koma Inu, Chauta, ndinu Atate athu,

ndinu Momboli wathu kuyambira kalekale.

17Chifukwa chiyani mukutisokeretsa pa njira zanu?

Bwanji mukutilola kuti tizikhala ouma mtima

kotero kuti sitikukuwopaninso?

Bwererani chifukwa cha atumiki anu,

mafuko a anthu amene ali choloŵa chanu.

18Anthu anu opatulika adangoti atakhala

nawo malo anu oyera kanthaŵi pang'ono,

adani adaŵasakaza malowo.

19Tasanduka ngati anthu amene simudatilamulepo,

ngati kuti sitidakhalepo anthu anu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help