1Anthu amene amakhulupirira Chauta
ndi olimba ngati phiri la Ziyoni,
limene silingathe kugwedezeka,
koma ndi lokhala mpaka muyaya.
2Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu,
momwemonso Chauta akuzinga anthu ake
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
3Mafumu oipa sadzalamulira nthaƔi yonse
dziko limene lapatsidwa kwa anthu ake,
kuti nawonso anthu olungamawo angachite zoipa.
4Chauta, achitireni zabwino
anthu amene ali abwino,
amene ali olungama mtima.
5Koma anthu amene amatsata njira zao zokhotakhota,
Chauta adzaƔapirikitsira
kumene kuli anthu ochita zoipa.
Mtendere ukhale ndi Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.