Yos. 21 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mizinda ya Alevi.

1Tsiku lina atsogoleri a mabanja a fuko la Levi adabwera kwa wansembe Eleazara, kwa Yoswa, mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraele.

2Num. 35.1-8 Aleviwo adafika ku Silo m'dziko la Kanani, nanena kuti, “Chauta adalamula kudzera mwa Mose kuti ife atipatse mizinda yokhalamo, ndiponso atipatse mabusa pozungulira mizindayo, kuti tizidyetsapo zoŵeta zathu.”

3Motero Aisraele adapatsa Aleviwo mizindayo pochita maere, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta, kuchokera pa magawo ao omwewo, potsata zomwe Chauta adalamula.

4Mabanja a Kohati ndiwo anali oyambirira kupatsidwa mizinda. Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aroni adapatsidwa mizinda 13, kuchokera m'mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini.

5Ndipo Akohati otsalawo adapatsidwa mizinda khumi kuchokera m'mafuko a Efuremu ndi Dani ndiponso theka la fuko la Manase lokhala kuzambwe kwa Yordani.

6Ageresoni adapatsidwa mizinda 13, kuchokera m'mafuko a Isakara, Asere, Nafutali ndi theka la fuko la Manase lokhala ku Basani.

7Mabanja a Merari adapatsidwa mizinda 12, kuchokera m'mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.

8Aisraele onse pamodzi adapereka mizinda imeneyi kwa Alevi mwamaere, pamodzinso ndi mabusa odyetsapo zoŵeta, potsata zomwe Chauta adaalamula kudzera mwa Mose.

9Mizinda ya Yuda ndi Simeoni imene idapatsidwa

10kwa zidzukulu za Aroni, ku banja lina limodzi la Akohati amene anali Alevi, maina ake ndi aŵa:

11adaŵapatsa mzinda wa Kiriyati-Ariba. (Araba anali bambo wa Anaki), dzina lake linanso ndi Hebroni. Mzindawo unali m'dziko la Yuda lamapiri lija, pamodzinso ndi mabusa a zoŵeta kuzungulira mzindawo.

12Komabe minda ya mzindawo pamodzi ndi midzi yake yomwe, adaipatsa Kalebe mwana wa Yefune, kuti ikhale choloŵa chake.

13Choncho midzi yonse imene ili m'munsimuyi, adaipatsa zidzukulu za Aroni wansembe. Poyamba Hebroni, umene unali mzinda wopulumukiramo aliyense woimbidwa mlandu wa kupha mnzake mwangozi, pamodzi ndi mabusa odyetsapo zoŵeta, ndiponso Libina,

14Yatiri, Esitemowa,

15Holoni, Debiri,

16Aini, Yuta ndi Betesemesi. Yonse pamodzi inalipo mizinda isanu ndi inai kuchokera m'mafuko aŵiri aja a Yuda ndi Simeoni, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

17A fuko la Benjamini adapereka Gibiyoni, Geba,

18Anatoti ndi Alimoni. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

19Ansembe, zidzukulu za Aroni, adapatsidwa mizinda 13, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

20Mabanja ena a Kohati, a fuko la Levi, adapatsidwa mizinda ina kuchokera ku fuko la Efuremu.

21Adapatsidwa Sekemu pamodzi ndi mabusa a zoŵeta. Mzindawo unali m'dziko lamapiri la Efuremu. Unalinso mzinda wopulumukiramo munthu aliyense wopha mnzake mwangozi. Adalandiranso Gezere,

22Kibizaimu ndi Betehoroni. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

23Kuchokera ku fuko la Dani adalandirako Elitele, Gibetoni,

24Ayaloni ndi Gatirimoni. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

25Kuchokera ku theka la Manase wakuzambwe adalandira mizinda iŵiri, Taanaki ndi Ibleamu, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

26Mabanja a Akohati ameneŵa adalandira mizinda khumi yonse pamodzi, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

27Ageresoni, gulu lina la fuko la Levi, adalandira mizinda iŵiri kuchokera ku theka la Manase wakuvuma: Golani ku Basani, mzinda wopulumukirapo munthu wopha mnzake mwangozi, ndi Besetera, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta.

28Kuchokera ku fuko la Isakara, adalandira Kisiyoni, Daberati,

29Yaramuti ndi Enganimu. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

30Kuchokera ku fuko la Asere adalandira Misalu, Abidoni,

31Helekati ndi Rehobu. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

32Kuchokera ku fuko la Nafutali, adalandira Kedesi wa ku Galilea, mzinda wopulumukiramo aliyense wopha mnzake mwangozi, ndiponso Hamotidori ndi Karitani. Yonse pamodzi inalipo mizinda itatu, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

33Mabanja osiyanasiyana a Ageresoni adalandira mizinda khumi ndi itatu, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

34Onse otsala a fuko la Levi amene anali a m'banja la Merari, adalandira mizinda iyi kuchokera ku fuko la Zebuloni: Yokoneamu, Karita,

35Dimina ndi Mahalala. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

36Kuchokera ku fuko la Rubeni adalandira Bezeri, Yahazi,

37Kedemoti ndi Mefaati. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

38Kuchokera ku fuko la Gadi adalandira Ramoti ku Giliyadi, mzinda wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi, ndiponso Mahanaimu,

39Hesiboni ndi Yazere. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai kuphatikizapo mabusa a zoŵeta.

40Motero mabanja a Merari, adapatsidwa mizinda khumi ndi iŵiri mwamaere.

41Mizinda 48 ya m'dziko limene Aisraele adalandira idapatsidwa kwa Alevi, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta.

42Mzinda uliwonse unali ndi mabusa a zoŵeta.

Israele atenga dziko.

43Motero Chauta adapatsa Aisraele dziko limene Iye yemwe adaalonjeza molumbira kuti adzapatsa makolo ao. Aisraele adalandira dzikolo, nakhazikika komweko.

44Chauta adaŵapatsa mtendere pakati pa anthu ena onse oŵazungulira, potsata zomwe Iye adaalonjeza makolo ao. Panalibe ndi mmodzi yemwe mwa adani ao amene adatha kugonjetsa Aisraele, chifukwa choti Chauta adaŵapatsa mphamvu zopambanira adani ao.

45Zoonadi Chauta adasunga malonjezo onse amene adaachita ndi Aisraele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help