Zek. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Magaleta anai

1Pambuyo pake ndidaona zinthu zinanso m'masomphenya: ndidaona magaleta anai akutuluka pakati pa mapiri aŵiri, mapiri ake amkuŵa.

2Chiv. 6.4; Chiv. 6.5 Galeta loyamba linkakokedwa ndi akavalo ofiira, lachiŵiri akavalo akuda,

3Chiv. 6.2 lachitatu akavalo oyera, lachinai linkakokedwa ndi akavalo otuŵa a maŵanga ofiirira.

4Tsono ndidafunsa mngelo amene ndinkalankhula naye uja kuti, “Mbuye wanga, kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?”

5Chiv. 7.1 Iye adayankha kuti, “Zimenezi zikutanthauza mphepo zinai zakumwamba, zimene zimachokera kwa Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi.

6Galeta la akavalo akudali likupita ku dziko lakumpoto. Galeta la akavalo oyerali likupita kutali kuzambwe. Galeta la akavalo amaŵangali likupita ku dziko lakumwera, ndipo galeta la akavalo ofiirali likupita ku dziko lakuvuma.”

7Akavalowo atatuluka, anali ndi phamphu kufuna kuyendera dziko lonse lapansi. Iye uja adaŵauza kuti, “Pitani mukayendere dziko lapansi.” Akavalowo adapitadi kukayendera dziko lapansi.

8Apo mngeloyo adandiŵuza mokweza mau kuti, “Amene apita ku dziko lakumpotowo atsitsa mzimu wanga kumeneko.”

Yerusalemu watsopano

9Kenaka Chauta adandipatsa uthenga wakuti,

10“Ulandire mphatso kwa anthu aŵa: Heledai, Tobiya, ndi Yedaya, amene abwerako ku ukapolo wa ku Babiloni. Iweyo upite tsiku lomwelo kwa Yosiya mwana wa Zefaniya.

11Siliva ndi golide amene ulandireyo upangire chisoti chaufumu. Chisoticho uchiike pamutu pa mkulu wa ansembe uja Yoswa, mwana wa Yehozadaki.

12Yer. 23.5; 33.15; Zek. 3.8 Tsono umuuze kuti, Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Ndi ameneyutu munthu wotchedwa ‘Nthambi’ uja. Adzaphuka ndi kukulira pomwe aliripo, ndipo adzamangapo Nyumba ya Chauta.

13Ndiye amene adzamange Nyumba ya Chauta. Ndiye amene adzakhale ndi ukulu waufumu, ndi kumalamulira atakhala pa mpando wake waufumu. Pafupi ndi mpando wake padzakhala wansembe, ndipo aŵiriwo adzagwira ntchito mwamtendere ndi mogwirizana.

14Chisoti chaufumucho azidzachisunga m'Nyumba ya Chauta, kuti chikhale chikumbutso kwa Heledai, Tobiya, Yedaya ndi Yosiya, mwana wa Zefaniya.

15“Anthu okhala kutali adzabwera kudzamanga Nyumba ya Chauta. Motero mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse wandituma kwa inu. Zimenezi zidzachitika ngati mumveradi mwachangu Chauta, Mulungu wanu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help