1Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni,
kuti moto upsereze mikungudza yako.
2Lirani mokweza, inu mitengo ya paini,
pakuti mikungudza yagwa,
mitengo yamphamvu yaonongeka.
Lirani mokweza inu mitengo ya thundu ya ku Basani,
pakuti nkhalango yoŵirira ija aiyeretsa.
3Imvani abusa, nawonso akulira mokweza,
pakuti mabusa ao obiriŵira auma.
Imvani misona ya mikango ikubangula,
pakuti nkhalango yoŵirira ya ku Yordani aiyeretsa.
Abusa aŵiri4Chauta, Mulungu wanga, adandiwuza kuti, “Ŵeta bwino nkhosa zimene zili kukaphedwa.
5Amene amagula nkhosa amazipha, koma salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Atamandike Chauta, ine ndalemera!’ Ndipo abusa ake sadzazimvera chifundo nkhosazo.
6Choncho onse okhala m'dziko lapansi, sindidzaŵamveranso chifundo. Ndikutero Ine Chauta. Munthu aliyense ndidzampereka m'manja mwa mtsogoleri wake ndi mwa mfumu yake. Ndipo iwowo adzasakaza dziko lonse, koma Ine sindidzampulumutsa aliyense m'manja mwao.”
7Tsono ine ndidayamba kuŵeta nkhosa zokaphedwa zija. Ndidatenga ndodo ziŵiri: yoyamba ndidaitcha dzina lakuti “Kukoma mtima”, yachiŵiri ndidaitcha “Umodzi.” Tsono gulu la nkhosa lija ndidaliŵetadi bwino.
8Pa mwezi umodzi ndidachotsa abusa atatu aja. Adafika pondipsetsa mtima, ine osathanso kuŵapirira. Iwonso adadana nane.
9Tsono ndidauza gulu la nkhosa lija kuti, “Sindidzakuŵetaninso. Imene ikuti ife, ife basi. Imene ikuti isokere, isokere, ndipo otsalanu, muzidyana.”
10Pambuyo pake ndidatenga ndodo yanga ija yotchedwa “Kukoma mtima” ndi kuithyola, kusonyeza kuphwanya chipangano chimene ndidaapangana ndi mitundu yonse ya anthu.
11Motero chipanganocho chidatha tsiku limenelo, ndipo ochita malonda a nkhosa aja, amene ankangondiyang'anitsitsa, adazindikira kuti zonse zimene ndinkachita zinali zochokera kwa Chauta.
12 Mt. 27.9, 10 Mt. 26.15 Tsono eni nkhosawo ndidaŵauza kuti “Ngati zakukomerani, mundilipire. Koma ngati si choncho, sungani ndalama zanu.” Ndiye iwowo adandilipira masekeli asiliva makumi atatu.
13Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Uziponye mosungira chuma.” Motero ndidatenga masekeli asiliva zija, mtengo uja adaati ndiyenera kulandirawu, nkukaziponya mosungira chuma m'Nyumba ya Chauta.
14Kenaka ndidathyolanso ndodo ina ija yotchedwa “Umodzi,” kusonyeza kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israele.
15Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Tenganso zida za mbusa, mbusa wake wopandapake.
16Pakuti ndidzakuika mbusa m'dziko, mbusa amene sadzasamala nkhosa zotayika, sadzanka nafunafuna zosokera, kapena kuchiritsa zopunduka, ndi kudyetsa zamoyo. Koma iye azidzangodya nyama ya nkhosa zonona, mpaka kumapulula ndi ziboda zake zomwe.
17“Tsoka kwa mbusa wanga wopandapakeyo,
amene amasiya nkhosa!
Amkanthe ndi lupanga pa mkono,
ndi pa diso lake lakumanja.
Mkono wakewo ufwape,
ndipo diso lakelo lichite khungu kotheratu!”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.