1Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
2“Aisraele, pomanga zithando, aliyense azimanga pafupi ndi mbendera yake imene ili ndi zizindikiro za banja la kholo lake. Azimanga moyang'anana ndi chihema chamsonkhano, tsono mochizungulira.
3Amene amange kuvuma, kotulukira dzuŵa, akhale a mbendera ya zithando za fuko la Yuda, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Yudalo ndi Nasoni, mwana wa Aminadabu,
4ndipo ankhondo ake ngokwanira 74,600.
5Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Isakara. Mtsogoleri wa fuko la Isakaralo ndi Netanele mwana wa Zuwara,
6ndipo ankhondo ake ngokwanira 54,400.
7Tsono pabwere fuko la Zebuloni, limene mtsogoleri wake ndi Eliyabu mwana wa Heloni,
8ndipo ankhondo ake ngokwanira 57,400.
9Gulu lonse lathunthu la ku zithando za Yuda, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 186,400. Iwowo azikhala patsogolo poyenda.
10“Mbali yakumwera kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Rubeni, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri,
11ndipo ankhondo ake ngokwanira 45,500.
12Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Simeoni, limene mtsogoleri wake ndi Selumiele mwana wa Zurishadai,
13ndipo ankhondo ake ngokwanira 59,300.
14Tsono pabwere fuko la Gadi, limene mtsogoleri wake ndi Eliyasafu, mwana wa Deuwele,
15ndipo ankhondo ake ngokwanira 45,650.
16Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Rubeni, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 151,450. Iwo akhale a gulu lachiŵiri poyenda.
17“Pamenepo mpamene anyamule chihema chamsonkhano, chifukwa zithando za Alevi zimakhala pakati pa zithando zina. Monga momwe adamangira zithando zao, ndimo aziyendera, gulu lililonse pamalo pake motsatira mbendera yake.
18“Mbali yakuzambwe kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Efuremu, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Efuremulo ndi Elisama mwana wa Amihudi,
19ndipo ankhondo ake ngokwanira 40,500.
20Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Manase, limene mtsogoleri wake ndi Gamaliele mwana wa Pedazuri,
21ndipo ankhondo ake ngokwanira 32,200.
22Tsono pabwere fuko la Benjamini, limene mtsogoleri wake ndi Abidani mwana wa Gideoni,
23ndipo ankhondo ake ngokwanira 35,400.
24Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Efuremu, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 108,100. Iwo akhale a gulu lachitatu poyenda.
25“Mbali yakumpoto kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Dani, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Danilo ndi Ahiyezere mwana wa Amishadai,
26ndipo ankhondo ake ngokwanira 62,700.
27Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Asere, limene mtsogoleri wake ndi Pagiyele mwana wa Okarani,
28ndipo ankhondo ake ngokwanira 41,500.
29Tsono pabwere fuko la Nafutali, limene mtsogoleri wake ndi Ahira mwana wa Enani,
30ndipo ankhondo ake ngokwanira 53,400.
31Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Dani ndi 157,600. Iwo akhale a gulu lotsiriza poyenda motsatira mbendera zao.”
32Ameneŵa ndiwo Aisraele monga momwe adaŵaŵerengera potsata banja la makolo ao. Anthu onse a m'zithandomo anali 603,550 amene adaŵaŵerenga m'magulumagulu.
33Koma Alevi sadaŵaŵerengere kumodzi ndi Aisraele, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
34Umu ndi m'mene adachitira Aisraele. Iwo adachita zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Adamanga zithando zao pafupi ndi mbendera zao. Choncho adanyamuka ulendo wao aliyense pa banja lake, potsata banja la makolo ao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.