1Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wa madzi
m'manja mwa Chauta.
Amauwongolera ku zimene Iyeyo akufuna.
2Makhalidwe a munthu amakhala olungama
pamaso pa mwiniwakeyo,
koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.
3Kuchita zolungama ndi zokhulupirika
kumakondweretsa Chauta koposa kupereka nsembe.
4Maso odzikuza ndi mtima wonyada
zimatsogolera anthu oipa ngati nyale,
nchifukwa chake amachimwa.
5Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake,
koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo,
amangokhala wosoŵa.
6Chuma chomachipeza monyenga
chimangoti wuzi ngati nthunzi,
ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
7Ndeu za anthu oipa zidzaŵaononga,
poti amakana kuchita zolungama.
8Njira ya munthu woipa ndi yokhotakhota,
koma khalidwe la munthu wosachimwa ndi lolungama.
9 Mphu. 25.16 Kuli bwino kukhala potero pa denga
kupambana kukhala m'nyumba
pamodzi ndi mkazi wolongolola.
10Mtima wa munthu woipa umalakalaka zoipa.
Samva chifundo konse ndi mnzake wovutika.
11Munthu wonyoza akalangidwa,
wopusapusa amaphunzirapo nzeru.
Munthu wanzeru akamlangiza, amamvetsa zambiri.
12Mulungu ngwachilungamo nthaŵi zonse,
amadziŵa zimene anthu oipa akuchita
ndipo adzawaononga.
13Amene amatseka m'khutu wosauka akamalira,
adzalira iyenso,
koma kulira kwakeko sikudzamveka.
14Mphatso yam'seri imaposa ukali,
ndipo chiphuphu chosereza chimathetsa
mphamvu ngakhale ya mkwiyo woopsa.
15Chilungamo chikachitika,
nzika zabwino zimakondwera,
koma zimadederetsa atambwali.
16Munthu amene amasiya njira ya anthu anzeru,
adzapezeka m'gulu la anthu akufa.
17Amene amakondetsa zosangalatsa,
adzasanduka munthu wosauka.
Amene amakondetsa vinyo ndi mafuta, sadzalemera.
18Oipa adzakhala choombolera anthu abwino,
ndipo osakhulupirika adzakhala choombolera anthu
a mtima wabwino.
19Kuli bwino kukhala ku chipululu
kupambana kukhala ndi mkazi wolongolola
ndi wopsa mtima msanga.
20Munthu wanzeru samwaza chuma chake,
koma munthu wopusa amachiwononga.
21Amene amatsata chilungamo ndi
chifundo adzapeza moyo ndi ulemu.
22Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu a mphamvu,
ndipo amagwetsa linga lamphamvu
limene anthuwo ankalikhulupirira.
23Amene amagwira pakamwa ndi kusamala zokamba zake,
sapeza mavuto.
24Munthu wonyada ndi wodzikuza amamtchula “Mnyodoli,”
chifukwa amachita zinthu modzitama ndi mwachipongwe.
25Kulakalaka kwa munthu waulesi kumamupha,
poti amangokhala manja ali khoba, osagwira ntchito.
26Tsiku lathunthu anthu oipa amasirira zinthu,
koma omvera Mulungu amapatsa ndipo alibe kaliwumira.
27 Mphu. 7.9 Nsembe ya anthu oipa imamnyansa Chauta,
nanji tsono akaipereka ndi cholinga choipa!
28Mboni yonama idzaonongeka,
koma mau a munthu wakumva adzamveka nthaŵi zonse.
29Munthu woipa amafuna kuwoneka wolimba mtima,
koma munthu woongoka amaganizira bwino zochita zake.
30Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu,
palibe ngakhale uphungu,
zimene zingathe kupambana Chauta.
31Kavalo amamkonzera tsiku la nkhondo,
koma ndi Chauta amene amapambanitsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.