Yob. 30 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1“Koma tsopano akundiyesa chinthu chochiseka,

anthu amene ali ana kwa ine,

anthu oti ndi atate ao omwe sindikadaŵayesa

oyenera kuti athandizane ndi agalu kuŵeta nkhosa zanga.

2Kodi mphamvu zao zikadandipinduliranji,

anthu amene nyonga zao zidatha kale?

3Anali atatheratu kuwonda ndi njala,

natsala mafupa okhaokha,

ankakungudza nthaka youma yachipululu.

4Ankathyola therere ndi masamba a zitsamba,

ankadya mizu ya dinde.

5Ankaŵapirikitsa pakati pa anthu,

anzao ankaŵakuwa ngati mbala.

6Ankaumirizidwa kumakhala m'zigwembe za mitsinje,

m'maenje am'nthaka ndi am'matanthwe.

7Ankalira ngati nyama kuthengo,

ndipo ankaunjikana pamodzi pa zitsamba zaminga.

8Iwowo anali opusa, achabechabe okhaokha,

ndipo adaŵachotsa m'dziko.

9“Tsopano ine ndasanduka nyimbo yao,

ndasanduka chisudzo chao.

10Ineyo ndimaŵanyansa,

ndipo amandithaŵa. Akangondiwona,

salephera kuti malovu nzee m'maso mwangamu.

11Poti Mulungu adandifooketsa ndi kundichepetsa,

iwowo adalekeratu kundiwopa.

12Ku dzanja langa lamanja

anthu achiwawa akundiwukira,

akukumba mbuna yoti ndigweremo,

akukonzekera njira zondiwonongeratu.

13Akunditsekera njira,

ndipo akufuna kundichititsa ngozi,

palibe wina aliyense woŵaletsa.

14Akundithamangira ngati madzi

oloŵera pa linga logumuka,

akubwererabwerera pakati pa chipasupasu.

15Zoopsa zandigwera.

Ulemu wanga wachita ngati kuuluzika ndi mphepo,

chuma changa chija chazimirira ngati mtambo.

16“Tsopano mtima wanga wachokamo.

Ndili pa mavuto, ndilibe popumira.

17Mafupa anga akuphwanya usiku,

zoŵaŵa sizikuleka.

18Chovala changa chakwinyikakwinyika

chifukwa cha matenda,

chikundithina ngati khosi la mkanjo wanga.

19Mulungu wandiponya m'matope,

ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa.

20“Ndimalira kwa Inu Mulungu,

koma simundiyankha. Ndimapemphera,

koma inu simundiyang'anako.

21Inu mwandichita zankhanza,

mwandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu.

22Inu mwandiika pa mphepo,

mwandinyamula ndi mphepoyo,

ndipo mwandiponya mu mkuntho wa namondwe.

23Tsono ndikudziŵa

kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa yanga,

kumene aliyense adzapitako.

24“Komabe kodi munthu wam'mazunzo

satambalitsa dzanja?

Kodi salira chithandizo m'mavuto mwakemo?

25Kodi ine sindidalire nawo anzanga

amene anali pa mavuto?

Kodi mtima wanga sudaŵamvere chisoni anthu osauka?

26Koma pamene ndinkayembekeza zabwino,

zovuta ndiye zimene zidandigwera.

Pamene ndinkayembekeza kuŵala,

mdima ndi umene udandiphimba.

27Mtima wanga ukuŵaŵa,

ndikusoŵa mpumulo,

masiku onse ndili pa mavuto.

28Ndikuyenda mu mdima popanda dzuŵa konse.

Komabe ndimaimirira pa msonkhano

ndi kupempha chithandizo molira.

29Kulira kwanga kuli ngati kwa nkhandwe,

ndimakhala ndekha ngati nthiŵatiŵa.

30Khungu langa likuyamba kuda ndi kunyenyeka,

Mafupa anga akutentha ndi chitungu.

31Pangwe wanga wasanduka woimbira maliro,

chitoliro changa chikupolokeza anthu olira.”

Yobe avomera kuchimwa kwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help