1Idafika nthaŵi imene Chauta adafuna kutenga Eliya m'kamvulumvulu kunka kumwamba. Tsiku limenelo Eliya ndi Elisa anali pa ulendo kuchokera ku Giligala.
2Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, Elisa, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Betele.” Koma Elisa adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adapita ku Betele.
3Tsono a m'gulu la aneneri amene anali ku Beteleko adadzakumana ndi Elisa, namufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti lero Chauta akulandani mbuyanu?” Elisa adayankha kuti, “Inde, ndikudziŵa, koma musakambe za zimenezi.”
4Tsiku lomwelo Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, Elisa, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yeriko.” Koma Elisa adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adakafika ku Yeriko.
5Ndipo a m'gulu la aneneri amene anali ku Yeriko adadzakumana ndi Elisa, namufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti lero Chauta akulandani mbuyanu?” Elisa adayankha kuti, “Inde, ndikudziŵa, koma musakambe za zimenezi.”
6Pambuyo pake Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yordani.” Koma Elisa adauza Eliyayo kuti, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adapitiriza ulendo wao.
7Anthu makumi asanu a m'gulu la aneneri aja adapita nawo ndipo adakaimirira chapatali potero, pamene Eliya ndi Elisa adaakaima pa gombe la mtsinje wa Yordani.
8Apo Eliya adatenga mwinjiro wake naupinda, kenaka adamenya madzi ndi mwinjirowo. Tsono madziwo adapatukana, ena kwina ena kwina, mpaka aneneri aŵiriwo adaoloka pouma.
9 .” Ndipo sadamuwonenso Eliyayo.
Tsono Elisa adagwira zovala zake nazing'amba paŵiri.
13Kenaka adatenga mwinjiro wa Eliya umene udaagwa, nabwerera nkukaima pa gombe la Yordani.
14Adagwira mwinjiro wa Eliyawo namenya nawo madzi aja, nati, “Ali kuti Chauta, Mulungu wa Eliya?” Atamenya madziwo choncho, madzi aja adapatukana, ena kwina, ena kwina. Ndipo Elisa adaoloka.
15Pamene a m'gulu la aneneri amene ankakhala ku Yeriko adaona Elisayo akuwoloka, adati, “Mphamvu ndi nzeru za Eliya zaloŵa mwa Elisa.” Tsono adabwera kudzakumana naye, namgwadira Elisayo, nkuŵeramitsa mitu yao pansi.
16Ndipo iwo adamuuza kuti, “Taonani tsono, ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Chonde mulole kuti anyamuke akamufunefune mbuyanu Eliya. Mwina mwake mzimu wa Chauta wamtenga nkukamponya kuphiri kwina kapena ku chigwa.” Elisayo adati, “Iyai musaŵatume.”
17Koma adamkakamiza mpaka Elisayo mwamanyazi adaŵalola naŵauza kuti, “Chabwino, atumeni.” Ndiye iwo adaŵatuma anthu makumi asanuwo. Ndipo anthuwo adakafunafuna Eliya masiku atatu, koma osampeza.
18Tsono adabwerera kwa Elisayo pamene iyeyo ankadikira ku Yeriko, ndipo iye adaŵauza kuti, “Kodi suja ndidaanena kuti musapite?”
Zozizwitsa za Elisa19Tsiku lina anthu amumzinda adauza Elisa kuti, “Onani, mzinda wathuwu ngwabwino kwambiri, zonse zili bwino monga mukuwoneramu, koma madzi okha ngoipa, ndipo nthaka yake njosabereka.”
20Apo Elisa adati, “Patseni mbale yatsopano, ndipo muikemo mchere.” Anthuwo adabweradi ndi mchere m'mbale.
21Tsono Elisa adapita ku kasupe wa madzi, nathiramo mchere m'kasupemo, nati, “Chauta akunena kuti, ‘Madzi ameneŵa ndaŵakonza. Kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo, m'madzi ameneŵa simudzakhala chinthu chopha anthu kapena choletsa nthaka kubereka.’ ”
22Motero madziwo ngabwinobe kwambiri mpaka lero lino, potsata mau amene Elisa adaalankhula.
23Kuchokera kumeneko Elisa adapita ku Betele. Ndipo pamene anali pa njira, anyamata ena amumzindamo adatuluka nayamba kumseka kuti, “Choka apa, chidazi! Choka apa, chidazi!”
24Tsono Elisayo adatembenuka, ndipo ataŵaona anyamatawo, adaŵatemberera m'dzina la Chauta. Pompo padatuluka zimbalangondo ziŵiri zazikazi kuchokera kuthengo, nkuphapo anyamata 42.
25Atachoka kumeneko, Elisa adapitirira kunka ku phiri la Karimele, ndipo pochoka kumeneko adabwerera ku Samariya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.