1Pambuyo pake ndidamva ngati mau amphamvu a chinamtindi cha anthu Kumwamba. Mauwo ankati,
“Aleluya!
Chipulumutso, ulemerero ndi mphamvu
ndi zake za Mulungu wathu,
2 Deut. 32.43; 2Maf. 9.7 pakuti chiweruzo chake chilichonse
nchoona ndi cholungama.
Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja
amene ankaipitsa dziko lapansi
ndi chigololo chake,
wamlanga chifukwa cha kupha atumiki ake.”
3 Yes. 34.10 Kachiŵiri mau aja adanenanso kuti,
“Aleluya!
Utsi wa mzindawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”
4Akuluakulu 24 aja, pamodzi ndi Zamoyo zinai zija, adadzigwetsa pansi moŵerama, napembedza Mulungu amene amakhala pa mpando wachifumu. Adayankha kuti, “Amen, Aleluya!”
Za phwando la ukwati wa Mwanawankhosa5 Mas. 115.13 Pambuyo pake ku mpando wachifumu uja kudachoka mau akuti,
“Tamandani Mulungu wathu, inu nonse atumiki ake,
inu nonse omuwopa, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe.”
6 2Es. 6.17; Ezek. 1.24; Mas. 93.1; 97.1; 99.1 Pamenepo ndidamva ngati mau a chinamtindi cha anthu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Mauwo ankati,
“Aleluya!
Paja Ambuye Mulungu wathu Mphambe akulamulira.
7Tikondwere ndi kusangalala, ndi kumtamanda,
pakuti nthaŵi ya ukwati wa Mwanawankhosa uja yafika,
mkwati wake wamkazi waukonzekera ukwatiwo.
8Iye waloledwa kuvala zovala za nsalu yabafuta,
yoŵala, yoombedwa bwino.”
(Zovala zabafutazo zikutanthauza ntchito zabwino za anthu a Mulungu.)
9 Mt. 22.2, 3 Pamenepo mngelo uja adandiwuza kuti, “Lemba mau aŵa akuti, ‘Ngodala anthu oitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa uja’.” Adandiwuzanso kuti, “Mau ameneŵa ndi mau oona a Mulungu.”
10Apo ndidadzigwetsa ku mapazi ake kuti ndimpembedze. Koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ndiponso ngati abale ako amene amachitira Yesu umboni. Iwe pembedza Mulungu.” Pajatu kuchitira Yesu umboni ndiye thima la uneneri.
Za wokwera pa kavalo woyera11 Ezek. 1.1; Mas. 96.13; Yes. 11.4 Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama.
12Dan. 10.6Maso ake anali psuu ngati malaŵi a moto, ndipo pamutu pake panali zisoti zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lolidziŵa iye yekha, osati wina aliyense.
13Lun. 18.14-18Chovala chake chinali choviika m'magazi, ndipo ankatchedwa, “Mau a Mulungu.”
14Magulu a ankhondo a Kumwamba ankamutsatira atakwera akavalo oyera, ndipo iwowo atavala zabafuta, zoyera ndi zangwiro.
15Mas. 2.9; Yes. 63.3; Yow. 3.13; Chiv. 14.20M'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa lotulukira kunja, loti adzalangire mitundu ya anthu. Adzaŵalamulira ndi ndodo yachitsulo, ndipo m'chopondera mphesa adzaponda mphesa za vinyo wa mkwiyo waukali wa Mulungu Mphambe.
16Pa mkanjo wake, ndi pantchafu pake padaalembedwa dzina loti, “Mfumu ya mafumu onse, ndi Mbuye wa ambuye onse.”
17 Ezek. 39.17-20 Kenaka ndidaona mngelo mmodzi ataimirira pa dzuŵa. Adafuula mokweza mau, nauza mbalame zonse zouluka mu mlengalenga kuti, “Dzasonkhaneni ku mgonero waukulu wa Mulungu.
18Bwerani, mudzadye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi wa okwerapo, mnofu wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, ang'onoang'ono ndi akuluakulu.”
19Pambuyo pake ndidaona chilombo chija pamodzi ndi mafumu a pa dziko lapansi, ndi magulu ao ankhondo. Adaasonkhana kuti amenyane nkhondo ndi wokwera pa kavalo uja, pamodzi ndi gulu lake la ankhondo.
20Chiv. 13.1-18Chilombocho chidagwidwa pamodzi ndi mneneri wonama uja amene anali atachita zozizwitsa pamaso pake. Zozizwitsazo, iye anali atanyenga nazo anthu amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, ndiponso anthu amene anali atapembedza fano lake lija. Chilombo chija ndi mneneri wonama uja, onse aŵiri adaŵaponya m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala yoyaka ya sulufure.
21Ena onse adaphedwa ndi lupanga lija lotuluka m'kamwa mwa wokwera pa kavalo uja. Ndipo mbalame zonse zidadya ndi kukhuta mnofu wa anthuwo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.