1Hezekiya atangomva zimenezi, adang'amba zovala zake mwachisoni, ndipo adavala chiguduli, nakaloŵa m'Nyumba ya Chauta.
2Tsono adatuma Eliyakimu mkulu wa nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa mfumu, ndiponso ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya, mwana wa Amozi.
3Iwowo adauza Yesaya mau a Hezekiya onena kuti, “Lero ndi tsiku la mavuto, la chilango ndi la manyazi. Tili ngati mkazi amene ali pafupi kubala mwana, koma alibe mphamvu zombalira mwanayo.
4Mfumu ya ku Asiriya yatuma kazembe wake wankhondo kudzanyoza Mulungu wamoyo. Makamaka Chauta, Mulungu wanu, wamva kunyoza kumeneku, ndipo adzaŵalanga anthu amene adamunyozawo. Nchifukwa chake muŵapempherere anthu otsalaŵa amene akali ndi moyo.”
5Pamene Yesaya adamva mau a mfumu Hezekiyawo,
6adati, “Kauzeni mbuyanu mau a Chauta akuti, ‘Usade nawo nkhaŵa mau ondinyoza a atumiki a mfumu ya ku Asiriya.
7Ndidzaika mumtima mwa mfumuyo ganizo lina lakuti ikadzangomva mphekesera, idzaumirizidwa kubwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzamphetsa kwao komweko.’ ”
Asiriya atumanso ankhondo(Yes. 37.8-20)8Kazembe wankhondo uja adamva kuti mfumu ya ku Asiriya ija inachoka ku Lakisi, ndipo inali kuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina. Motero anapita kumeneko kukakambirana nayo.
9Tsono pamene mfumu ya ku Asiriya idamva kuti mfumu Tirihaka wa ku Etiopiya akubwera kudzachita nayo nkhondo, idatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mau onena kuti,
10“Mulungu wako amene ukumkhulupirirayo asakunyenge pokulonjeza kuti Yerusalemu sadzagwa m'manja mwa ine mfumu ya ku Asiriya.
11Wakhala ulikumva zimene mafumu a ku Asiriya adaŵachita maiko onse, kuti adaŵaononga kotheratu. Tsono iweyo ndiye nkupulumuka?
12Makolo anga adaononga mizinda ya Gozani, Harani ndi Rezefe. Ndipo adapha anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu ya anthu a mitundu inawo idaŵapulumutsa?
13Nanga mafumu a m'mizinda ya Hamati, Aripadi, Separavaimu ndi Iva ali kuti?”
14Mfumu Hezekiya adalandira kalata kwa amithenga aja, naiŵerenga. Pomwepo adapita ku Nyumba ya Chauta naika kalatayo m'menemo pamaso pa Chauta.
15Eks. 25.22 Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pamwamba pa akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira mafumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi.
16Tsono Inu Chauta, tcherani khutu, mumve. Inu Chauta, tsekulani maso, muwone. Mumve mau onse amene Senakeribu adalankhula, onyoza Inu Mulungu wamoyo.
17Inu Chauta, zoonadi mafumu a ku Asiriya adaononga anthu a mitundu ina yonse, nasandutsa maiko ao chipululu.
18Adatentha milungu yao imene siinali milungu konse, koma mafano amitengo ndi amiyala opangidwa ndi anthu, nchifukwa chake adaiwononga.
19Ndiye Inu Chauta, Mulungu wathu, ndikukupemphani kuti mutipulumutse kwa munthu ameneyu, kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziŵe kuti Inu nokha, Chauta, ndiye Mulungu.”
Yesaya atumiza uthenga kwa mfumu(Yes. 37.21-38)20Tsono Yesaya mwana wa Amozi adatumiza kwa mfumu Hezekiya mau omuuza kuti Chauta, Mulungu wa Israele, wamva pemphero lake lija lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.
21Poitsutsa mfumuyo Chauta adati,
“Mzinda wa Ziyoni ukukunyoza ndi kukuseka,
iwe Senakeribu,
mzinda wa Yerusalemu ukupukusa mutu
kumbuyo kwako monyodola.
22“Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira yani?
Kodi ndani amene wamufuulira ndi kumuyang'ana monyada?
Si wina ai, koma Woyera uja wa Israele!
23Udatuma amithenga ako kudzandinyoza Ine,
ndipo udati,
‘Ndi magareta anga ochuluka
ndidakwera mapiri ataliatali,
ndidafika mpaka pa nsonga za mapiri a ku Lebanoni.
Ndidagwetsa mitengo yake ya mkungudza yaitali kwambiri,
ndiponso mitengo yake ya paini yabwino koposa.
Ndidaloŵanso m'kati mwake mwenimweni,
m'nkhalango yake yoŵirira kwabasi.
24Ndidakumba zitsime ku maiko achilendo
ndi kumwamo madzi.
Ndi mapazi anga ndidapondereza
ndi kuumitsa mitsinje ya ku Ejipito.’
25“Koma Ine Chauta ndikuti,
Kodi sudamvepo kuti zimenezi ndidazikonzeratu kalekale?
Ndidaaziganiziratu masiku amakedzana,
tsopano ndazichitadi.
Iweyo kwako kunali kungogwetsa mizinda yamalinga
ndi kuisandutsa miyulu ya miyala.
26Anthu amene ankakhala kumeneko anali opanda mphamvu,
ankada nkhaŵa, ndipo adaasokonezeka.
Anali ngati mbeu zam'munda, ngati udzu wanthete.
Anali ngati udzu wapadenga,
umene mphepo imauumitsa usanakule nkomwe.
27“Koma Ine ndimadziŵa zonse za iwe,
pamene ukhala pansi, pamene uyenda kwina ndi kubwerako,
ndiponso pamene undikwiyira.
28Chifukwa chakuti udandikwiyira,
ndipo kudzitukumula kwako kudamveka kwa Ine,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza,
ndi kuika chitsulo m'kamwa mwako.
Ndidzakubweza pokuyendetsa m'njira
yomwe udadzera pobwera.”
Chizindikiro kwa Hezekiya29Tsono Yesaya adauza mfumu Hezekiya kuti,
“Chizindikiro cha zimene zidzachitika ndi ichi:
Chaka chino mudzadya tirigu wa mphulumukwa.
Chaka chamaŵa mudzadya tirigu wongodzimerera.
Tsono chaka chamkucha mudzafesa tirigu nkukolola,
mudzaoka mitengo yamphesa nkudya zipatso zake.
30Anthu a m'banja la Yuda amene adzatsalire
adzapezanso bwino,
ngati zomera zimene zazamitsa mizu pansi
ndi kubala zipatso poyera.
31Ku Yerusalemu kudzafumira anthu otsala,
ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.
Changu cha Chauta chidzachitadi zimenezi.
32Zimene akunena Chauta za mfumu ya ku Asiriya
ndi izi, akuti,
‘Sadzaloŵa mu mzinda umenewu,
sadzaponyamo muvi ndi umodzi womwe.
Ankhondo ake azishango
sadzafika pafupi ndi mzinda umenewu,
ndipo sadzauzinga ndi mtumbira wankhondo.
33Adzabwerera potsata njira yomwe adaadzera pobwera,
ndipo sadzaloŵa mu mzinda umenewu.
Ine Chauta ndatero.
34Ine ndidzautchinjiriza ndi kuuteteza mzinda umenewu
chifukwa cha ulemerero wanga,
ndiponso chifukwa cha chipangano changa
chimene ndidachita ndi Davide mtumiki wanga.’ ”
35Ndiye usiku umenewo mngelo wa Chauta adapita ku zithando zankhondo za Aasiriya naphako asilikali 185,000. M'maŵa mwake adangoona asilikaliwo ali ngundangunda, atafa onsewo.
36Tsono Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adachoka ndi kubwerera kwao, nakakhala ku Ninive.
37Tsiku lina pamene ankapembedza m'nyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake aŵiri, Adrameleki ndi Sarezere, adamupha ndi malupanga ao, nathaŵira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake wina, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.