1Yobe adapitiriza kulankhula nati,
2“Pali Mulungu wamoyo
amene wakana kundiweruza molungama,
pali Mphambe amene wandipweteketsa mtima.
3Nthaŵi zonse pamene ndikupumabe,
Mulungu namandipatsa mpweya wa moyo,
4pakamwa panga sipadzatuluka mau oipa,
lilime langa silidzalankhula zonyenga.
5Zakuti mukunena zoona, ine sindikuvomera.
Kunena za ine ndidzakhalabe
wokhulupirika mpaka kufa kwanga.
6Sindidzaleka kunena kuti ndine wolungama,
sindidzasintha maganizo anga.
Mtima wanga sukunditsutsa pa chinthu chilichonse.
7“Adani anga ziŵaonekere zinthu
zoyenerera anthu oipa. Ondiwukira alangidwe
monga momwe amachitira osalungama.
8Nanga chiyembekezo cha munthu
wopanda Mulungu nchiyani pamene aphedwa,
pamene Mulungu amchotsera moyo wake?
9Kodi Mulungu angamve kulira kwa munthu wotere,
pamene zovuta zimgwera?
10Kodi angakondwere ndi Mphambe?
Kodi angapemphere kwa Mulungu nthaŵi zonse?
11“Ndidzakuphunzitsani
za mphamvu zazikulu za Mulungu,
ndidzakusimbirani zimene Mphambe adakonza.
12Ndithu, inu mwadziwonera nokha,
nanga bwanji mukulankhula zachabe?
13“Chilango chimene Mulungu amasungira munthu woipa,
choloŵa chimene munthu wozunza anzake
amalandira kwa Mphambe ndi ichi:
14ana ake ngakhale achuluke chotani,
adzaphedwa ndi lupanga,
zidzukulu zake zidzasoŵa chakudya.
15Amene adzamtsalireko adzafa ndi matenda,
akazi ao amasiye sadzaŵalira.
16Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi,
kapena kukundika zovala ngati mchenga,
17koma olungama ndiwo amene adzavala zimenezo,
ndipo anthu osachimwa adzagaŵana siliva ameneyo.
18Nyumba imene akuimanga ili ngati ukonde wa kangaude,
ili ngati msasa umene mlonda amamanga.
19Amapita ku bedi ali wolemera,
koma kutha kwake nkumeneko, poti aphenyule maso,
angoona chuma chakecho pali ng'wa!
20Zoopsa zimamkokolola ngati madzi a chigumula,
ndipo usiku mkuntho umamnyamula.
21Mphepo yakuvuma imamuulutsa,
iye nkuzimirira, imamchotsa pamalo pake.
22Imakuntha pa iye osamchitira chifundo,
pamene iye akuyesa kuithaŵa mwaliŵiro.
23Koma mphepoyo imamuwomba ndithu,
ndipo kuchokera pamalo pake imamuwopseza.”
Nyimbo yotamanda Nzeru.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.