Mla. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nzeru zimaposa uchitsiru

1Ntchentche zakufa zimaika fungo loipa

m'mafuta onunkhira bwino.

Choncho kupusa kwapang'ono

kumatha kuwononga nzeru ndi ulemu.

2Mtima wa munthu wanzeru umamtsogolera bwino,

koma mtima wa munthu wopusa umamsokeza.

3Chitsiru ngakhale chikamayenda mu mseu,

zochita zake nzopanda nzeru ndithu,

ndipo aliyense amachizindikira kuti nchitsirudi.

4Wolamula akakukwiyira,

usachoke pa ntchito yako,

pakuti kufatsa kumakonza ngakhale zolakwa zazikulu.

5Pansi pano pali choipa china chimene ndachiwona, choipa chake ndi cholakwa chimene amachichita wolamula.

6Opusa amaŵapatsa ntchito zapamwamba, olemera nkumaŵapatsa ntchito zotsika.

7Ndaona akapolo akuyenda pa akavalo, m'menemo akalonga akuyenda pansi ngati akapolo.

8 Mas. 7.15; Miy. 26.27; Mphu. 27.26, 27 Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha.

Amene amaboola khoma njoka idzamuluma.

9Amene amakumba miyala,

itha kumpweteka miyalayo.

Amene amaŵaza nkhuni,

atha kudzipweteka nazo.

10Nkhwangwa ikakhala yobuntha,

nkupandanso kuinola,

imalira mphamvu zambiri potema.

Koma nzeru zimathandiza munthu

kuti athedi kudula kanthu.

11Nkopanda phindu kudziŵa kuseŵeretsa njoka

ngati njokayo yakuluma kale.

12Mau a pakamwa pa munthu wanzeru amakondweretsa,

koma pakamwa pa chitsiru mpoononga.

13Chitsiru chimayamba ndi mau opusa,

potsiriza zolankhula zake zimangokhala zamisala basi.

14Chitsiru chimangochulutsa mau.

Kodi ndani angadziŵe

zimene zidzachitike kutsogolo?

Ndani angathe kumuuza munthu

zimene zidzachitike iye atafa?

15Chitsiru chimagwira ntchito modzitopetsa,

koma njira yopita ku mzinda sichiidziŵa.

16Tsoka kwa iwe dziko,

ngati mfumu yako ikali mwana,

ndipo nduna zako zimachezera madyerero usiku wonse.

17Koma ndiwe wodala iwe dziko,

ngati mfumu yako ndi mwana wa mfulu.

Ndiwe wodala ngati nduna zako zimachita phwando

pa nthaŵi yabwino,

kuti zikhale zamphamvu,

osati kuti ziledzere.

18Denga limaloshoka,

mwini wake akakhala waulesi,

ndipo nyumba imadontha,

mwiniwake akakhala nthyamba.

19Phwando ndi lokondwetsa anthu,

ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo.

Komatu zonsezo nzolira ndalama.

20Ngakhale mumtima mwako usamainyoza mfumu.

Ngakhale m'chipinda mwako momwe usamatukwana wolemera.

Mwina kambalame kamumlengalenga

kapena kachilombo kena kouluka nkukumvera,

kenaka nkukaulula zonse kwa amene umaŵanenawo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help