Mas. 46 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu ali nafeKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la ana a Kora.Nyimbo yoimba anamwali.

1Mulungu ndiye kothaŵira kwathu,

ndiye mphamvu zathu.

Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

2Nchifukwa chake sitidzaopa

ngakhale dziko lapansi lisinthike,

ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,

3ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma.

Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja.

4Koma kuli mtsinje umene mifuleni yake

imasangalatsa anthu amumzinda wa Mulungu,

malo oyera okhalako Wopambanazonse.

5Mulungu ali m'kati mwa mzindawo,

sudzaonongeka konse.

Mulungu adzauthandiza dzuŵa lisanatuluke.

6Mitundu ya anthu ikunjenjemera kwambiri,

maufumu akugwedezeka,

Mulungu akalankhula mau ake,

dziko lapansi likusungunuka.

7Chauta Wamphamvuzonse ali nafe.

Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu.

8Bwerani kuti muwone ntchito za Chauta,

m'mene amachitira zozizwitsa pa dziko lapansi.

9Amaletsa nkhondo

mpaka ku mathero a dziko lapansi.

Amathyola uta, ndi kupokonyola mkondo.

Amatentha magaleta ankhondo ndi moto.

10“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu.

Mitundu ya anthu imanditamanda,

a m'dziko lapansi amandiyamika.”

11Chauta Wamphamvuzonse ali nafe,

Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help