Mali. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za chilango, kulapa ndi chikhulupiriro

1Ine ndine munthu amene ndaona mavuto,

ndalangidwa ndi ndodo ya ukali wa Mulungu.

2Adandiyendetsa ndi kubwera nane mu mdima

mopanda nkuŵala komwe.

3Zoonadi adandikantha ndi dzanja lake,

ankachita zimenezi mobwerezabwereza tsiku lonse.

4Adandipweteka m'thupi lonse,

ndipo adaphwanya mafupa anga onse.

5Adandizinga ndi kundizunguliza ponseponse

ndi mazunzo ndi masautso.

6Adanditaya m'malo a mdima wabii,

kuti ndikhale ngati munthu wofa kalekale.

7Adanditsekera m'malinga kuti ndisathaŵe.

Adandimanga ndi maunyolo olemera kwambiri.

8Ngakhale pamene ndinkafuula ndi kupempha chithandizo,

sankalimva pemphero langalo.

9Adanditsekera mseu ndi miyala yosema,

ndipo adakhotetsa njira zanga.

10Adandiwukira ngati chimbalangondo

kapena ngati mkango wondilalira.

11Adandisiyitsa njira nanding'ambang'amba,

kenaka nkundisiya.

12Adakoka uta wake

nandiyesa chinthu chochitirapo chandamale.

13Adalasa mtima wanga

ndi mivi ya m'phodo lake.

14Ndasanduka chinthu chomachiseka,

kwa anthu a mitundu ina,

amandiimba nyimbo zondinyoza.

15Chauta adandidyetsa zoŵaŵa,

adandimwetsa chivumulo.

16Adandigulula mano ndi timiyala,

adandivimviniza m'phulusa.

17Mumtima mwanga mulibenso mtendere,

chimwemwe ndidachiiŵaliratu.

18Choncho ndikuti,

“Ulemerero wanga wonse watha,

chandithera chikhulupiriro cholandira kanthu ka Chauta.”

19Ndimakumbukira masautso anga ndi kuzunzika kwanga,

zili ngati chivumulo ndi ndulu.

20Nthaŵi zonse ndimangozilingalirabe zimenezi,

nkuwona ndataya mtima.

21Koma pali chinanso chimene ndimachikumbukira,

chimenecho ndicho chimandilimbitsa mtima.

22Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha,

chifundo chakenso nchosatha.

23M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano,

chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.

24Chauta ndiye zanga zonse

motero ndimadalira Iyeyo.

25Chauta ndi wabwino kwa amene amamudalira,

kwa onse amene amafuna kuchita zimene Iye afuna.

26Nkwabwino kumdikira Chauta mopirira

kuti aonetse chipulumutso chake.

27Nkwabwinonso kuti munthu asenze goli la kupirira

pamene iye ali pa unyamata.

28Akhale pansi yekha mkachete,

pamene Chauta amsenzetsa golilo.

29Agwetse nkhope yake pa fumbi,

mwina chikhulupiriro nkukhalapobe.

30Apereke tsaya lake kwa wofuna kumumenya,

apirire zomunyoza zonse.

31Ndithudi Ambuye sadzataya atumiki ao mpaka muyaya.

32Angathe kulanga mwankhalwe,

komabe adzaonetsa chifundo,

chifukwa chikondi chao nchochuluka.

33Savutitsa mwadala,

sakonda kusautsa munthu aliyense.

34Chauta amadziŵa

pamene akulu amapondereza am'ndende am'dziko.

35Amadziŵa pamene olamula amapsinja munthu

popanda chilungamo pamaso pa Wopambanazonse.

36Pamene iwo amagamula mlandu mokondera,

kodi Ambuye saona zimenezi?

37Ndani angathe kulamula kuti zakutizakuti zichitike,

ngati Chauta waletsa zimenezo?

38Paja madalitso ndi matsoka

zonse nzochokera kwa Wopambanazonse.

39Munthu wina aliyense wamoyo angadandaulirenji

pamene alangidwa chifukwa cha machimo ake?

40Tiyeni tiŵaone ndi kuŵayesa makhalidwe athu,

ndipo tibwerere kwa Chauta.

41Tikweze mitima yathu ndi manja athu

kwa Mulungu kumwamba.

42Ifeyo tachimwa, ndipo tapanduka,

tsono Inu simudakhululuke.

43Mwatipirikitsa muli okwiya,

ndipo mwatipha mopanda chifundo.

44Mwadzibisa ndi mitambo,

kumene mapemphero athu sangathe kufikako.

45Mwatisandutsa onyozeka ngati zinyatsi,

m'maso mwa anthu a mitundu ina.

46Adani athu akutinyodola.

47Tagwa m'zoopsa ndi m'mbuna,

m'chipasupasu ndi m'chiwonongeko.

48M'maso mwanga misozi ikungoti mbwembwembwe,

chifukwa anthu anga aonongeka.

49Ndidzalira misozi kosalekeza

ndiponso osapumulira,

50mpaka Chauta adzayang'ane pansi kuchokera kumwamba

ndi kuwona mavuto anga.

51Mtima wanga ukupweteka

poona zimene zikuŵachitikira akazi a mumzinda mwanga.

52Amene anali adani anga popanda chifukwa,

akhala akundisaka ngati mbalame.

53Adandiponya m'dzenje ndili moyo,

nkumandiponya miyala ndili momwemo.

54Madzi adaamiza mutu wanga,

ine nkunena ku, “Mayo, ndikufa ine!”

55Ndidatama dzina lanu mopemba, Inu Chauta,

ndili m'dzenje lozamalo.

56Inu mudamva mau anga akuti,

“Musagonthetse dala makutu anu

pamene ndikupemphera kuti mudzandithandize.”

57Inu mudasendera pafupi pamene ndinkakutamani mopemba,

ndipo mudanena kuti “Usachite mantha.”

58Inu Chauta, mudandithandiza pa mlandu wanga,

ndipo mudaombola moyo wanga.

59Inu Chauta, mudaona zoipa zimene anthu adandichita,

tsono muweruze ndinu pamenepo.

60Mudaona m'mene ankandilipsirira,

mudaonanso ziwembu zimene adandichita.

61Inu Chauta mudamva kunyoza kwao koopsa

ndiponso ziwembu zimene ankakonzekera kuti andichite.

62Mudamva manong'onong'ono ao,

ndi m'mene adani anga ankandinenera tsiku lonse.

63Onani m'mene akundinyozera,

m'maŵa ndi madzulo akungokhalira kundiimba nyimbo.

64Inu Chauta, muŵalange potsata zolakwa zao,

potsata ntchito zimene adachita.

65Muŵazamitse mtima

muŵatemberere basi.

66Inu Chauta, muŵapirikitse mwaukali,

muŵaonongeretu pa dziko lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help