1“Pomadzagaŵa dziko kuti fuko lililonse lilandire chigawo chake, chimodzi adzachipatule kuti chidzakhale cha Chauta. M'litali mwake mudzakhale makilomita 12 ndi theka, muufupi mwake khumi. Malo onsewo adzakhala opatulika.
2M'kati mwa chigawo chimenechi, malo a mamita 250 mbali iliyonse adzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. Pozungulira pake ponse padzakhala malo a mamita 25.
3M'chigawo chopatulikacho uyese malo a makilomita 12 ndi theka m'litali mwake, makilomita asanu muufupi mwake. Pamenepo padzakhala malo opatulika, malo oyera kwambiri.
4Malo ameneŵa adzakhalanso a ansembe amene amatumikira ku malo opatulika, amene amayandikira Chauta pomutumikira. Pamenepo padzakhala malo omangapo nyumba zao ndi Nyumba ya Mulungu yomwe.
5Alevi otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzakhala ndi chigawo china cha makilomita 12 ndi theka m'litali mwake, ndi makilomita asanu muufupi mwake. Kumeneko ndiko kudzakhalenso midzi yao.
6“Poyandikana ndi malo opatulikawo, musankhe kadziko kokwanira makilomita aŵiri ndi theka muufupi mwake, m'litali mwake makilomita 12 ndi hafu, kuti akhale malo a mzinda. Malo ameneŵa adzakhala a banja lonse la Israele.
Dera la mfumu7“Mupatulenso dera la mfumu. Likhudzane ndi chigawo cha malo opatulika ndi cha mzinda, liyandikane ndi zigawozo chakuzambwe ndi chakuvuma. Litalike ngati chigawo chimodzi cha fuko la Israele, mpaka kukafika ku malire a dziko kuzambwe ndi kuvuma.
8Deralo lidzakhala choloŵa cha mfumu m'dziko la Israele. Choncho mafumu anga sadzazunzanso anthu anga, koma azidzaŵalola Aisraele kuti akhale ndi zigawo zaozao.
Chauta adzudzula olamulira9“Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Tsono pakwana, inu olamulira a ku Israele. Lekani nkhanza ndi kuzunza anthu. Muzimvera malamulo ndipo muzichita zachilungamo. Alekeni anthu anga, musamaŵachotsa pa dziko lao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
10 Lev. 19.36 “Miyeso yanu yoyesera zinthu monga efa ndi bati, izikhala yokhulupirika.
11Efa ndi bati ikhale miyeso yolingana kukula kwake. Muyeso wa homeri ukhale wokwanira mabati khumi, ukhalenso wokwanira maefa khumi. Ndiye kuti kukula kwa miyeso iŵiriyo kuzidzatsata kukula kwa homeriyo.
12Muyeso wa sekeli ukhale wokwanira magera makumi aŵiri. Muyeso wa mina ukhale wolemera masekeli makumi asanu ndi limodzi.
13“Nazi zopereka zimene mudzazipereke: chimodzi mwa zigawo 60 za tirigu, barelenso chimodzimodzi,
14ndiponso chimodzi mwa zigawo 100 za mafuta. Miyeso yake ili motere: mabati khumi alingana ndi homeri imodzi kapena kori imodzi.
15Mupereke nkhosa imodzi pa gulu la nkhosa 200 za m'mabusa abwino a Israele. Ndimo m'mene mudzaperekere nsembe zatirigu, nsembe zopsereza ndiponso nsembe zachiyanjano, kupepesera milandu ya anthu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
16“Anthu onse a m'dzikomo azipereka zimenezi kwa mfumu ya ku Israele.
17Ndipo mfumu izipereka zofunikira ku nsembe zopsereza, nsembe zatirigu ndi nsembe zazakumwa pa masiku achikondwerero, ndi a pokhala mwezi, masiku a Sabata, ndiponso pa masiku ena amene Aisraele amaŵasunga. Mfumuyo ipereke zofunikira ku nsembe zopepesera machimo, nsembe zatirigu, nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kuti zonsezo zikhale zopepesera machimo a Aisraele.
Masiku achikondwerero(Eks. 12.1-20; Lev. 23.33-43)18“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, muzitenga mwanawang'ombe wamphongo wopanda chilema, ndi kuchita mwambo woyeretsa malo opatulika.
19Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera machimoyo, ndipo aŵapake pa mphuthu za Nyumba ya Mulungu, pa ngodya zinai za pamwamba pa guwa ndi pa mphuthu za pa chipata cha bwalo lam'kati.
20Muzichita chimodzimodzi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mwezi, kuti mupepesere aliyense amene adachimwa mosafuna kapena mosadziŵa. Motero Nyumba ya Mulungu mudzaisunga yoyera.
21 Eks. 12.1-20; Num. 28.16-25 “Pa tsiku la khumi ndi chinai la mwezi woyamba, muzichita chikondwerero cha Paska, chikondwerero chake cha masiku asanu ndi aŵiri. Masiku amenewo muzidya buledi wosatupitsa.
22Pa tsiku loyamba la chikondwererocho, mfumu ipereke nsembe ya ng'ombe yamphongo kupepesera machimo ake ndiponso a anthu onse.
23Pa masiku asanu ndi aŵiri a chikondwererocho, mfumuyo izipereka kwa Chauta nsembe izi zopsereza: ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, zonsezo zopanda chilema. Tsiku lililonse iziperekanso nsembe ya tonde mmodzi, kupepesera machimo.
24Pamodzi ndi ng'ombe iliyonse yamphongo ndi nkhosa iliyonse yamphongo, mfumu ipereke chopereka cha zakudya chokwanira efa imodzi ndiponso ya mafuta okwanira hini imodzi.
25 Lev. 23.33-36; Num. 29.12-38 “Tsono mfumu ichitenso chimodzimodzi pa tsiku la khumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Chikondwerero chimenecho chizichitika masiku asanu ndi aŵiri. Izipereka nsembe za mtundu womwewonso, zopepesera machimo, nsembe zopsereza, ndiponso nsembe zaufa ndi zamafuta zomwe.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.