1Inu Mulungu, anthu azikutamandani ku Ziyoni,
achitedi zimene adalumbira kwa Inu.
2Inu amene mumamvera pemphero,
anthu onse adzabwera kwa Inu,
3chifukwa cha machimo ao.
Pamene zochimwa zathu zitipambana,
Inu mumazifafaniza.
4Ngwodala munthu amene Inu mumamsankha
nkubwera naye kudzakhala m'mabwalo anu.
Mutikhutitse ndi zinthu zabwino za m'Nyumba yanu,
Nyumba yanu yoyera.
5Tsono Inu mumatiyankha
potipulumutsa ndi ntchito zanu zodabwitsa,
Inu Mulungu Mpulumutsi wathu.
Anthu a pa dziko lonse lapansi
ndiponso a patsidya pa nyanja zakutali,
onsewo amakhulupirira Inu.
6Inu mudaonetsa mphamvu zanu,
pokhazikitsa mapiri.
7Inu mumachititsa bata mkokomo wa nyanja
ndi mkokomo wa mafunde
ndi phokoso la mitundu ina ya anthu.
8Motero okhala ku malire akutali a dziko lapansi
amaopa zizindikiro zanu zodabwitsa.
Anthu amafuula mokondwera chifukwa cha zochita zanu,
kuyambira mbali imodzi ya dziko lapansi
mpaka mbali yake inanso.
9Tsono Inu mumadalitsa dziko lapansi ndi kulithirira,
ndipo mumalilemeza kwambiri.
Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi,
Inu mumaŵapatsa anthu dzinthu,
pakuti ndimo m'mene mwalikonzera dzikolo.
10Inu mumathirira kwambiri makwaŵa am'mizere,
mumasalaza nthumbira zake,
mumafeŵetsa nthaka ndi mvula,
ndipo mumadalitsa mbeu.
11Pakutha pa chaka mumapereka zokolola zambiri
mwa ubwino wanu,
kulikonse kumene Inu mupita,
kumapezeka dzinthu dzambiri.
12Ngakhale ku mabusa akuchipululu
kumamera msipu wambiri,
ndipo mapiri amadzazidwa ndi chimwemwe.
13Madambo adzaza ndi zoŵeta,
zidikha zadzaza ndi dzinthu,
zonsezo zikufuula ndi kuimbira limodzi mwachimwemwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.