1Chifukwa chokonda Ziyoni
sindidzakhala chete,
chifukwa chokonda Yerusalemu
sindidzakhala chete,
mpaka chilungamo chake
chitaoneka poyera ngati kuŵala,
ndipo chipulumutso chake
chitaoneka ngati muuni woyaka.
2Iwe Yerusalemu,
mitundu ya anthu idzakuwona utapambana pa nkhondo,
mafumu ao onse adzaona ulemerero wako.
Adzakuitanira dzina latsopano,
limene adzakutche ndi Chauta yemwe.
3Udzakhala ngati chisoti chaufumu
chokongola m'manja mwa Chauta,
ngati nsangamutu yaulemerero
m'manja mwa Mulungu wako.
4Sudzatchedwanso “Wosiyidwa,”
dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.”
Dzina lako latsopanolo lidzakhala “Ndikukondwera naye.”
Dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa mwachimwemwe,”
chifukwa choti Chauta akukondwera nawe,
ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.
5Monga mnyamata amakwatira namwali,
chonchonso mmisiri wodzakumanganso adzakukwatira.
Monganso mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi,
chonchonso Mulungu adzasangalala nawe.
6Iwe Yerusalemu,
pa malinga ako ndaikapo alonda,
usana wonse ndi usiku wonse sadzakhala chete.
Inu amene mumakumbutsa Chauta za malonjezo ake,
musapumule.
7Musaleke kumkumbutsa mpaka atakhazikitsanso Yerusalemu,
ndi kuusandutsa mzinda umene dziko lapansi lidzautamanda.
8Chauta adalumbira motsimikiza,
ndipo adzasunga malumbirowo ndi mphamvu zake.
Adati, “Adani ako sadzadyanso tirigu wako,
ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako.
9Koma inu amene mudabzala ndi kukolola tiriguyo,
ndiye amene mudzadye buledi,
ndipo mudzatamanda Chauta.
Inu amene munkasamala mitengo yamphesa
ndi kumathyola mphesa,
ndiye amene mudzamwe vinyo m'mabwalo a Nyumba yanga.”
10Tulukani, inu a mu Yerusalemu,
inde tulukani mumzindamo,
mukakonze mseu woti anthu anu obwerera kwao aziyendamo.
Mulambule mseu waukulu, ndipo muchotsemo miyala.
Mukweze mbendera kuti mitundu ya anthu iziwona.
11 Yes. 40.10; Chiv. 22.12 Chauta walengeza ku dziko lonse lapansi
zakuti muuze anthu a ku Yerusalemu kuti,
“Chipulumutso chanu chikubwera.
Chauta akubwera ndi mphotho yake,
akubwera nazo zokuyenererani.
12Mudzatchedwa anthu opatulika a Mulungu,
anthu amene Chauta waŵapulumutsa.
Iwe Yerusalemu,
udzatchedwa Mzinda wokondedwa wa Chauta,
mzinda umene Mulungu sadausiye.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.