1Pamene Yesu ankachoka ku Nyumba ya Mulungu, wophunzira wake wina adamuuza kuti, “Aphunzitsi, taonani kukongola kwake miyalayi ndi nyumbazi.”
2Yesu adamuuza kuti, “Kodi mukuziwona nyumba zikuluzikuluzi? Sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.”
Za mavuto ndi mazunzo(Mt. 24.3-14; Lk. 21.7-19)3Pambuyo pake Yesu adakhala pansi, pa Phiri la Olivi, kuyang'anana ndi Nyumba ya Mulungu. Tsono Petro, Yakobe, Yohane ndi Andrea adamufunsa paokha, kuti,
42Es. 4.51—5.19“Tatiuzani bwino, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti zonsezi zili pafupi kuchitika?”
5Yesu adayamba kuŵauza kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni.
6Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine,’ ndipo adzasokeza anthu ambiri.
7Koma inu mukadzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno, kapena mphekesera za nkhondo zakutali, musadzade nkhaŵa ai. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.
8Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana, ndipo kudzakhala njala. Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto.
9 Mt. 10.17-20; Lk. 12.11, 12 “Koma inu muchenjere. Anthu adzakuperekani ku mabwalo amilandu a Ayuda, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero. Mudzaonekera kwa akulu a Boma ndi kwa mafumu chifukwa cha Ine, kuti mukandichitire umboni pamaso pao.
10Nkofunika kuti Uthenga Wabwino uyambe walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.
11Tsono akadzakugwirani ndi kukuperekani ku mlandu, musadzaderetu nkhaŵa nkumaganiza kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Ai, inu mukangonena zimene Mulungu akakuuzeni pa nthaŵi imeneyo. Pajatu odzalankhula sindinu ai, koma Mzimu Woyera.
12Mbale azidzapereka mbale wake kuti aphedwe, bambo azidzapereka mwana wake. Ana azidzaukira makolo ao, mpaka kuŵaphetsa.
13Mt. 10.22Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.”
Chosakaza chonyansa(Mt. 24.15-28; Lk. 21.20-24)14 Dan. 9.27; 11.31; 12.11; 1Am. 1.54; 6.7 “Chosakaza chonyansa chija chidzakhala atachiimika pamalo pomwe sichiyenera kukhalapo. (Umvetse bwino amene ukuŵerengawe.) Mukadzaona zimenezi, pamenepo amene ali m'Yudeya adzathaŵire ku mapiri.
15Lk. 17.31Amene ali padenga pa nyumba yake, asati atsike kuti akatenge chinthu m'nyumba mwakemo.
16Yemwe ali ku munda, asabwererenso ku nyumba kuti akatenge mwinjiro.
17Ali ndi tsoka akazi amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo.
18Pempherani kuti zimenezi zisadzaoneke pa nyengo yachisanu,
19Dan. 12.1; Chiv. 7.14chifukwa masautso amene adzaoneke masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso.
20Tsonotu masiku amenewo, Ambuye akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma masikuwo Mulungu adaŵachepetsa chifukwa cha anthu omwe Iye adaŵasankha.
21“Pa nthaŵi imeneyo, wina akadzakuuzani kuti, ‘Ali panotu Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Uyo ali apoyo,’ musadzakhulupirire.
22Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti, ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
23Koma inu chenjerani. Ine ndiye ndakuuziranitu zonse.”
Za kubwera kwa Mwana wa Munthu(Mt. 24.29-31; Lk. 21.25-28)24 Yes. 13.10; Yow. 2.10, 31; 3.15; Chiv. 6.12; Yes. 13.10; Ezek. 32.7 “Masiku amenewo, mavutowo atatha, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala.
25Yes. 34.4; Chiv. 6.13; Yow. 2.10Nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka.
26Dan. 7.13; Chiv. 1.7Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu zazikulu ndi ulemerero.
27Tsono Iye adzatuma angelo ake kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”
Phunziro la mkuyu(Mt. 24.32-35; Lk. 21.29-33)28“Phunziriraniko kwa mkuyu. Mukamaona kuti nthambi zake zayamba kukhala zanthete ndipo masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira.
29Momwemonso mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziŵe kuti Mwana wa Munthu ali pafupi, ali pakhomo penipeni.
30Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse.
31Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.”
Tsiku lomaliza silidziŵika(Mt. 24.36-44)32 Mt. 24.36 “Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa, amadziŵa ndi Atate okha basi.
33Tsono chenjerani, khalani maso, chifukwa simudziŵa kuti nthaŵiyo idzakwana liti.
34Lk. 12.36-38Ndi monga ngati bwana amene akunyamuka ulendo kuchoka kunyumba kwake. Amasiya zinthu m'manja mwa antchito ake, aliyense ntchito yake, ndipo amauza wapakhomo kuti azikhala maso.
35Nanunso tsono khalani maso, chifukwa simudziŵa mwini nyumba adzabwerera nthaŵi yanji: kaya ndi madzulo, kaya ndi pakati pa usiku, kaya ndi tambala woyamba, kapena mbandakucha.
36Atha kudzabwera mwadzidzidzi, tsono asadzakupezeni muli m'tulo.
37Zimene ndikunenazi, sindikuuza inu nokha ai, koma ndikuuza anthu onse kuti, ‘Khalani maso.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.