1Yobe adapitiriza nati,
2“Ha, ndikadabwerera mwakale
monga m'mene ndinkakhalira pa nthaŵi yamakedzana,
pa masiku amene Mulungu ankandisunga bwino.
3Nthaŵi imeneyo Mulungu anali nane,
nyale yake inkandiwunikira mu mdima.
4Masiku amenewo ndinali pabwino zedi,
madalitso a Mulungu anali pabanja panga.
5Nthaŵi imeneyo Mphambe anali nane,
ana anga ali kwete m'mbalimu.
6Nthaŵi imeneyo ng'ombe ndi mbuzi
zanga zinkandipatsa mkaka wambiri,
mitengo yanga ya olivi inkamera ndi m'matanthwe momwe.
7Pamene ndinkapita ku chipata cha mzinda,
pamene ndinkakonzekera zokakhala nawo pabwalopo,
8anyamata akandiwona ankapatuka,
ndipo madoda ankadzambatuka nkukhala chilili.
9Akalonga ankakhala chete,
atangoti pakamwa gwirire.
10Atsogoleri ankangoti duu,
lilime litangoti nganganga ku nkhama.
11Aliyense womva za ine,
ankanditchula kuti ndine wodala,
aliyense wondiwona ankandilemekeza.
12Zidatero chifukwa choti
ndinkapulumutsa amphaŵi olira,
ndinkalanditsa ana amasiye opanda woŵathandiza.
13Anthu amene anali pa zoopsa
kwambiri ankanditamanda,
akazi amasiye ndinkaŵasangalatsa.
14Nthaŵi zonse ndinkachita zoyenera,
ntchito zanga zonse zinali zangwiro.
15Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya,
ndinali ngati mapazi kwa anthu opunduka.
16Osauka ndinali ngati bambo wao,
anthu osaŵadziŵa konse ndinali mtetezi wao pa milandu.
17Ndinkaononga mphamvu za anthu ankhalwe,
ndinkalanditsa amene anali atagwidwa.
18“Tsono mumtimamu ndinkati,
‘Ndidzafera pakati pa ana anga,
masiku a moyo wanga ndidzaŵachulukitsa kwambiri
ngati mchenga.
19Ndinali ngati mtengo umene
mizu yake yatambalalira ku madzi
umene masamba ake ndi onyowa ndi mame.
20Aliyense ankandilemekeza,
nthaŵi zonse mphamvu zanga zinali ngati uta wolimba.’
21“Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena,
ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga.
22Ine nditalankhula, iwowo sankalankhulanso,
mau anga ankaŵagwira mtima.
23Ankayembekeza ine monga momwe amayembekezera mvula,
ankangoti kukamwa yasa
ngati anthu odikira mvula yam'malimwe.
24Ndinkaŵasekerera pamene iwowo
analibenso chikhulupiriro,
kukoma mtima kwanga kunkaŵalimbitsa mtima.
25Ndinkasankhula njira yao,
ndipo ndinkaŵatsogolera ngati mfumu,
tsono ndidakhazikika pakati pao,
ngati mfumu pakati pa ankhondo ake,
ndinali ngati msangalatsi pakati pa olira.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.