Yes. 37 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Hezekiya apempha nzeru kwa Yesaya(2 Maf. 19.1-7)

1Hezekiya atangomva zimenezi, adang'amba zovala zake mwachisoni, ndipo adavala chiguduli, nakaloŵa m'Nyumba ya Chauta.

2Tsono adatuma Eliyakimu mkulu wa nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa mfumu, ndiponso ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya, mwana wa Amozi.

3Iwowo adauza Yesaya mau a Hezekiya onena kuti, “Lero ndi tsiku la mavuto, la chilango ndi la manyazi. Tili ngati mkazi wapathupi amene ali pafupi kubala mwana, koma alibe mphamvu zomubalira mwanayo.

4Mfumu ya ku Asiriya yatuma kazembe wake wankhondo kudzanyoza Mulungu wamoyo. Makamaka Chauta, Mulungu wanu, wamva kunyoza kumeneku, ndipo adzaŵalanga anthu amene adamunyozawo. Motero muŵapempherere anthu otsalaŵa amene akali ndi moyo.”

5Pamene Yesaya adamva mau a mfumu Hezekiyawo,

6adati, “Kauzeni mbuyanu mau a Chauta akuti, ‘Usade nawo nkhaŵa mau ondinyoza a atumiki a mfumu ya ku Asiriya.

7Ndidzaika mumtima mwa mfumuyo ganizo lina lakuti, ikadzangomva mphekesera, idzaumirizidwa kubwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzamphetsa kwao komweko.’ ”

Aasiriya aopsezanso kachiŵiri.(2 Maf. 19.8-19)

8Kazembe wankhondo uja adamva kuti mfumu ya ku Asiriya ija inachoka ku Lakisi, ndipo inali kuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina. Motero anapita kumeneko kukakambirana nayo.

9Tsono pamene mfumu ya ku Asiriya idamva kuti mfumu Tirihaka wa ku Etiopiya akubwera kudzachita nayo nkhondo, idatumanso amithenga kwa mfumu Hezekiya ndi mau onena kuti,

10“Mulungu wako amene ukumkhulupirirayo asakunyenge pokulonjeza kuti Yerusalemu sadzagwa m'manja mwa ine mfumu ya ku Asiriya.

11Wakhala ulikumva zimene mafumu a ku Asiriya adaŵachita maiko onse, kuti adaŵaononga kotheratu. Tsono iweyo ndiye nkupulumuka?

12Makolo anga adaononga mizinda ya Gozani, Harani ndi Rezefe. Ndipo adapha anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu ya anthu a mitundu inawo idaŵapulumutsa?

13Nanga mafumu a m'mizinda ya Hamati, Aripadi, Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?”

14Mfumu Hezekiya adalandira kalata kwa amithenga aja, naiŵerenga. Pomwepo adapita ku Nyumba ya Chauta, naika kalatayo m'menemo pamaso pa Chauta,

15ndipo adapemphera kuti,

16Eks. 25.22 “Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pamwamba pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi.

17Tsono Inu Chauta, tcherani khutu, mumve. Inu Chauta tsekulani maso, muwone. Mumve mau onse amene Senakeribu adalankhula, onyoza Inu Mulungu wamoyo.

18Inu Chauta, zoonadi mafumu a ku Asiriya adaononga anthu a mitundu ina yonse, nasandutsa maiko ao chipululu.

19Adatentha milungu yao imene siinali milungu konse, koma mafano amitengo ndi amiyala opangidwa ndi anthu, nchifukwa chake adaiwononga.

20Ndiye Inu Chauta, Mulungu wathu, mutipulumutse ife kwa munthu ameneyu, kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziŵe kuti Inu nokha, Chauta, ndiye Mulungu.”

Chauta ayankha pemphero la Hezekiya(2 Maf. 19.20-37)

21Tsono Yesaya, mwana wa Amozi, adatumiza kwa mfumu Hezekiya mau ochokera kwa Chauta, Mulungu wa Israele, oyankha pemphero lake lija lonena za Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya.

22Poitsutsa za mfumuyo Chauta adati,

“Mzinda wa Ziyoni ukukunyoza ndi kukuseka,

iwe Senakeribu,

mzinda wa Yerusalemu ukupukusa mutu

kumbuyo kwako monyodola.

23“Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira yani?

Kodi ndani amene wamufuulira ndi kumuyang'ana monyada?

Si wina ai, koma Woyera uja wa Israele!

24Udatuma atumiki ako kudzanyoza Ine,

ndipo udati,

‘Ndi magaleta anga ochuluka

ndidakwera mapiri ataliatali,

ndidafika mpaka pa nsonga za mapiri a ku Lebanoni.

Ndidagwetsa mitengo yake ya mkungudza yaitali kwambiri,

ndiponso mitengo yake ya paini yabwino koposa.

Ndidaloŵanso m'kati mwake mwenimweni,

mwankhalango yake yoŵirira kwabasi.

25Ndidakumba zitsime ku maiko achilendo

ndi kumwamo madzi.

Ndi mapazi anga ndidapondereza

ndi kuumitsa

mitsinje ya ku Ejipito.’

26“Koma Ine Chauta ndikuti,

Kodi sudamvepo kuti zimenezi ndidazikonzeratu kalekale?

Ndidaaziganiziratu masiku amakedzana.

Tsopano ndazichitadi.

Iweyo kwako kunali kungogwetsa mizinda yamalinga

ndi kuisandutsa miyulu ya miyala.

27Anthu amene ankakhala kumeneko

anali opanda mphamvu,

ankada nkhaŵa, ndipo adaasokonezeka.

Anali ngati mbeu zam'munda,

ngati udzu wanthete.

Anali ngati udzu wapadenga,

umene mphepo imauumitsa usanakule nkomwe.

28“Koma Ine ndimadziŵa zonse za iwe

pamene ukukhala pansi,

pamene ukuyenda kwina ndi kubwerako,

ndiponso pamene ukundikwiyira.

29Chifukwa chakuti udandikwiyira,

ndipo kudzitukumula kwako kudamveka kwa Ine,

ndidzakola mphuno yako ndi mbedza,

ndi kuika chitsulo m'kamwa mwako.

Ndidzakubweza pokuyendetsa m'njira

yomwe udadzera pobwera.”

30Tsono Yesaya adauza mfumu Hezekiya kuti,

“Chizindikiro cha zimene zidzachitika ndi ichi:

Chaka chino mudzadya tirigu wa mphulumukwa.

Chaka chamaŵa mudzadya tirigu wongodzimerera.

Tsono chaka chamkucha mudzabzala tirigu ndi kukolola,

mudzaoka mitengo yamphesa nkudya zipatso zake.

31Anthu a m'banja la Yuda amene adzatsalire,

adzapezanso bwino,

ngati zomera zimene zazimitsa mizu pansi

ndi kubala zipatso poyera.

32Ku Yerusalemu kudzafumira anthu otsala,

ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.

Changu cha Chauta Mphambe chidzachitadi zimenezi.

33“Zimene akunena Chauta

za mfumu ya ku Asiriya, ndiizi,

akuti, ‘Sadzaloŵa mu mzinda umenewu,

sadzaponyamo muvi ndi umodzi womwe.

Ankhondo ake azishango

sadzafika pafupi ndi mzinda umenewu,

ndipo sadzauzinga ndi mtumbira wankhondo.

34Adzabwerera potsata njira yomwe adaadzera pobwera,

ndipo sadzaloŵa mu mzinda umenewu.

Ine Chauta ndatero.

35Ine ndidzautchinjiriza ndi kuuteteza mzinda umenewu

chifukwa cha ulemerero wanga,

ndiponso chifukwa cha chipangano changa

chimene ndidachita ndi Davide mtumiki wanga.’ ”

36Mngelo wa Chauta adapita ku zithando zankhondo za Aasiriya, naphako asilikali 185,000. M'maŵa mwake anthu adangoona asilikaliwo ali ngundangunda, atafa onsewo.

37Tsono Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adachoka ndi kubwerera kwao, nakakhala ku Ninive.

38Tsiku lina pamene ankapembedza m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wake, ana ake aŵiri, Adrameleki ndi Sarezere, adamupha ndi malupanga ao, nathaŵira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake wina, adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help