Yob. 36 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za tanthauzo la masautso a Yobe

1Ndipo Elihu adapitirira kulankhula, nati:

2“Mundilole pang'ono,

ndipo ndikuphunzitsani.

Pakuti zilipobe zoti ndinene m'malo mwa Mulungu.

3Nzeru zanga zikhala zochokera patali,

ndiwonetsa kulungama kwa Mlengi wanga.

4Ndithudi, sindikunena zabodza.

Wolankhula nanune ndine wanzeru kotheratu.

5“Zoonadi, Mulungu ndi wamphamvu,

sanyoza munthu aliyense, ndipo amadziŵa zonse.

6Salola oipa kuti akhalebe ndi moyo,

koma anthu osauka amaŵachitira zolungama.

7Iyeyo amatchinjiriza anthu opanda chifukwa,

amalola kuti alamulire ngati mafumu,

ndipo motero amalemekezeka mpaka muyaya.

8Koma anthu akamangidwa ndi nsinga,

namazunzika chifukwa cha zimene adachita,

9pamenepo Mulungu amaŵasonyeza ntchito zao

ndi zolakwa zao,

kutsutsa kudzikuza kwao kochita kunyanya.

10Amaŵatsekula makutu kuti amve malangizo ake,

amaŵalamula kuti asiye zoipa.

11Ngati anthu amumvera ndi kumamtumikira,

adzatsiriza masiku a moyo wao mwamtendere,

adzatsiriza zaka zao mosangalala.

12Koma akapanda kumvera,

adzaonongeka ndi lupanga, adzafa osadziŵa kanthu.

13“Anthu onyoza Mulungu mumtima mwao

amaputa mkwiyo wake, Mulungu akaŵalanga,

iwo safuula kupempha chithandizo.

14Amafa akali biriŵiri,

ndipo moyo wao umathera m'zonyansa.

15Koma Mulungu amapulumutsa ovutika

mwa njira ya mazunzo ao omwe,

amaŵatsekula makutu poŵagwetsa m'mavuto.

16Inuyo Mulungu adakutulutsaninso m'mavutowo,

afuna kukuikani pabwino, osasoŵa kanthu kalikonse.

17“Koma tsopano inu mwapezeka opalamula

ngati anthu oipa,

choncho chilango cholungama cha Mulungu chakugwerani.

18Muchenjere kuti chuma chingakuphimbeni m'maso,

musalole kuti chiphuphu chikusokezeni.

19Kodi kulira kwanu kungakuchotseni m'mavuto?

Kodi mphamvu zanu zingakupulumutseni?

20Musalakelake kuti usiku ubwere,

chifukwa ndiyo nthaŵi

imene mitundu ya anthu idzaonongeka.

21Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo,

chifukwa uchimowu ndiwo udadzetsa kuzunzika kwanu.

22Zoonadi, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu.

Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye?

23Palibe ndi mmodzi yemwe angauze Mulungu zoti achite.

Palibe aliyense amene anganene kuti

‘Mulungu ndi wolakwa.’

24“Kumbukirani kutamanda ntchito za Mulungu,

zimene anthu amaziyamika ndi nyimbo.

25Anthu onse amaona ntchitozo,

koma palibe wozindikira m'mene ziliri.

26Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu kwambiri,

sitimdziŵa mpang'ono pomwe.

Chiŵerengero cha zaka zake nchosadziŵika.

27Mulungu ndiye amakweza timadontho ta madzi

ku thambo kuchokera pansi,

ndipo amasungunula mitambo kuti ikhale mvula.

28Mitambo imatsanyula mvulayo,

ndipo mvulayo imavumba pa anthu mokwanira.

29Kodi alipo wina woti angadziŵe kuyenda kwa mitambo

kapena kugunda kwa zing'aning'ani?

30Mulungu amaŵalitsa zing'aning'ani

kuthambo kwake konse,

zimafika ngakhale pansi pa nyanja.

31Mulungu amachenjeza mitundu ya anthu

podzera m'zimenezi,

komabe amapereka chakudya chochuluka.

32Amagwira zing'aning'ani,

ndipo amazilamula kuti zigwe pa malo amene Iye akufuna.

33Kugunda kwake kumalengeza kuti Iye alipo,

ndiye amalanga uchimo mwaukali.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help